< Zachariasza 5 >
1 Potemem się obrócił, a podniósłszy oczu swych ujrzałem, a oto księga leciała.
Ndinayangʼananso ndipo taonani ndinaona chikalata chimene chimawuluka.
2 I rzekł do mnie: Cóż widzisz? I rzekłem: Widzę księgę lecącą, której długość na dwadzieścia łokci, a szerokość na dziesięć łokci.
Mngelo uja anandifunsa kuti, “Kodi ukuona chiyani?” Ndinayankha kuti, “Ndikuona chikalata chikuwuluka, mulitali mwake mamita asanu ndi anayi ndipo mulifupi mwake mamita anayi ndi theka.”
3 I rzekł do mnie: Toć jest przeklęstwo, które wyjdzie na oblicze wszystkiej ziemi: bo każdy złodziej według tego przeklęstwa, jako i ta ziemia, wygładzony, i każdy fałszywie przysięgający według niego, jako i ona, wygładzony będzie.
Ndipo mngeloyo anandiwuza kuti, “Awa ndi matemberero amene akupita pa dziko lonse lapansi; potsata zimene zalembedwa mʼkati mwa chikalatamo, aliyense wakuba adzachotsedwa, ndipo potsata zomwe zalembedwa kunja kwake, aliyense wolumbira zabodza adzachotsedwanso.
4 Wywiodę je, mówi Pan zastępów, aby przyszło na dom złodzieja, i na dom kłamliwie przez imię moje przysięgającego; owszem, mieszkać będzie w pośrodku domu jego, i zniszczy go, i drzewo jego i kamienie jego.
Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Temberero limeneli ndidzalitumiza, ndipo lidzalowa mʼnyumba ya munthu wakuba ndi munthu wolumbira zabodza mʼdzina langa. Lidzakhala mʼnyumbamo mpaka kuyiwonongeratu, matabwa ake ndi miyala yake yomwe.’”
5 Wyszedł tedy Anioł on, który zemną mówił, i rzekł mi: Podnieśże teraz oczu swych, a obacz, co to jest, co wychodzi.
Kenaka mngelo amene amayankhula nane uja anabwera patsogolo panga ndipo anandiwuza kuti, “Kweza maso ako tsopano kuti uwone kuti ndi chiyani chikubwerachi.”
6 I rzekłem: Cóż jest? A on odpowiedział: To jest efa wychodzące. Potem rzekł: Toć jest oko ich przypatrujące się wszystkiej ziemi.
Ndinafunsa kuti, “Kodi chimenechi nʼchiyani?” Mngeloyo anayankha kuti, “Limeneli ndi dengu loyezera.” Ndipo anawonjezera kunena kuti, “Umenewu ndi uchimo wa anthu mʼdziko lonse.”
7 A oto sztukę ołowiu niesiono, a przytem była niewiasta jedna, która siedziała w pośrodku efa.
Pamenepo chovundikira chake chamtovu chinatukulidwa, ndipo mʼdengumo munali mutakhala mkazi.
8 Tedy rzekł Anioł: Toć jest ona niezbożność; i wrzucił ją w pośród efa, wrzucił i onę sztukę ołowiu na wierzch efy.
Mngeloyo anati, “Chimenechi ndi choyipa,” ndipo anamukankhira mkaziyo mʼdengu muja, nabwezera chovundikira chamtovu chija pamwamba pake.
9 A podniósłszy oczu swych ujrzałem, a oto dwie niewiasty wychodziły, mające wiatr w skrzydłach swych, a miały skrzydła, jako skrzydła bocianie, i podniosły ono efa między ziemię i między niebo.
Kenaka ndinayangʼananso, ndipo ndinaona akazi awiri akuwuluka kubwera kumene kunali ine; akuwuluzika ndi mphepo. Iwo anali ndi mapiko ngati a kakowa, ndipo ananyamula dengu lija, kupita nalo pakati pa mlengalenga ndi dziko lapansi.
10 Tedym rzekł do onego Anioła, który mówił zemną: Dokądże niosą to efa?
Ine ndinafunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Dengulo akupita nalo kuti?”
11 I rzekł do mnie: Aby mu zbudowano dom w ziemi Senaar, gdzieby umocnione było i postawione na podstawku swoim.
Iye anayankha kuti, “Ku dziko la Babuloni kuti akalimangire nyumba. Nyumbayo ikadzatha, adzayikamo dengulo.”