< Rodzaju 49 >

1 Wezwał tedy Jakób synów swoich i rzekł: Zbierzcie się, a oznajmię wam, co ma przyjść na was w ostatnie dni.
Pambuyo pake Yakobo anayitanitsa ana ake aamuna nati: Sonkhanani pamodzi kuti ndikuwuzeni zimene zidzakuchitikireni mʼmasiku a mʼtsogolo.
2 Zbierzcie się, i słuchajcie synowie Jakóbowi, a słuchajcie Izraela, ojca waszego.
“Bwerani ndipo imvani mawu anga, inu ana a Yakobo; mverani abambo anu Israeli.
3 Ruben pierworodny mój, tyś moc moja, i początek siły mojej, zacny dostojeństwem, i zacny męstwem.
“Rubeni, ndiwe woyamba kubadwa; mphamvu yanga ndiponso chizindikiro choyamba cha mphamvu zanga, wopambana pa ulemerero ndi mphamvu.
4 Spłyniesz jako woda: nie będziesz zacnym, boś wstąpił na łoże ojca twego, i splugawiłeś łoże moje, i zginęło dostojeństwo twoje.
Wokokoma ngati madzi a chigumula, koma sudzakhalanso wopambana, iwe unagona pa bedi la abambo ako, ndithu unayipitsa bedi la mdzakazi wake.
5 Symeon i Lewi, bracia, naczynia nieprawości miecze ich.
“Simeoni ndi Levi ndi pachibale pawo, anachitira nkhanza anthu amene anachita nawo pangano.
6 W radę ich niechaj nie wchodzi dusza moja, a z zgromadzeniem ich niech się nie jednoczy sława moja; bo w zapalczywości swej zabili męża, a w swej woli wywrócili mur.
Iwe moyo wanga, usakhale nawo pa misonkhano yawo ya mseri, kapena kugwirizana nawo mʼmabwalo awo, pakuti anapha anthu mu mkwiyo wawo ndipo anapundula ngʼombe zamphongo monga kunawakomera.
7 Przeklęta zapalczywość ich, iż uporna, i gniew ich, iż zatwardziały. Rozdzielę je w Jakóbie, a rozproszę je w Izraelu.
Matemberero awagwere chifukwa cha mkwiyo wawo woopsa chonchi ndi ukali wawo wankhanza choterewu! Ine ndidzawabalalitsa mʼdziko la Yakobo ndi kuwamwaza iwo mʼdziko la Israeli.
8 Juda, tyś jest, ciebie chwalić będą bracia twoi; ręka twoja będzie na szyi nieprzyjaciół twoich; kłaniać się tobie będą synowie ojca twego.
“Yuda, ndiwe amene abale ako adzatamanda; dzanja lako lidzagwira pa khosi pa adani ako; abale ako adzakugwadira iwe.
9 Szczenię lwie Juda, od łupu, synu mój, wróciłeś się; skłonił się i położył się jako lew, i jako lwica, a któż go obudzi?
Yuda ali ngati mwana wa mkango; umabwerera ku malo ako ndi zofunkha, mwana wanga. Monga mkango, amadziwongola ndi kugona pansi, ndipo ngati mkango waukazi, ndani angalimbe mtima kumudzutsa?
10 Nie będzie odjęte sceptrum od Judy, ani Zakonodawca od nóg jego, aż przyjdzie Szylo, i jemu będzie oddane posłuszeństwo narodów.
Ndodo yaufumu sidzachoka mwa Yuda, udzawupanirira ulamuliro motero kuti palibe amene adzawuchotse, mpaka mwini wake weniweni atabwera ndipo mitundu yonse ya anthu idzamumvera.
11 Uwiąże u winnej macicy oślę swe, a u wybornej macicy winnej oślątko oślicy swej; omyje w winie szatę swoję, a we krwi jagód winnych odzienie swoje
Ndiye amene amamangirira bulu wake wamkazi kumtengo wa mpesa, ndi mwana wa bulu ku nthambi ya mpesa wabwino. Ndi iye amene amachapa zovala zake mu vinyo; ndi mkanjo wake mu vinyo wofiira ngati magazi.
12 Czerwieńsze oczy jego nad wino, a bielsze zęby jego nad mleko.
Maso ake adzakhala akuda chifukwa cha vinyo, mano ake woyera chifukwa cha mkaka.
13 Zabulon na brzegu morskim mieszkać będzie, i przy porcie okrętów, a granice jego aż do Sydonu.
“Zebuloni adzakhala mʼmphepete mwa nyanja; adzakhala pa dooko la sitima zapamadzi; malire ake adzafika ku Sidoni.
14 Isaszar jako osieł kościsty, leżący między dwoma brzemiony.
“Isakara ali ngati bulu wamphamvu wogona pansi pakati pa makola.
15 Upatrzył pokój, że jest dobry, i ziemię, że piękna, nachylił ramię swe ku noszeniu, dla tegoż będzie hołd dawał.
Ataona ubwino wake wa pamalo pake popumira ndi kukongola kwa dziko lake, iye anaweramutsa msana kuti anyamule katundu wake ndipo anasanduka wogwira ntchito ya ukapolo.
16 Dan sądzić będzie lud swój, jako jedno z pokoleń Izraelskich.
“Dani adzaweruza mwachilungamo anthu ake monga limodzi mwa mafuko a anthu a mu Israeli.
17 Dan będzie wężem na drodze, żmiją na ścieżce, kąsając pięty końskie, że spadnie nazad jeździec jego.
Dani adzakhala ngati njoka ya mʼmphepete mwa msewu, songo yokhala mʼnjira imene imaluma chidendene cha kavalo kuti wokwerapoyo agwe chagada.
18 Zbawienia twego oczekiwam, Panie!
“Ndikuyembekeza chipulumutso chanu Yehova.
19 Gad od wojska zwyciężony będzie; ale i on potem zwycięży.
“Gadi adzachitidwa chiwembu ndi gulu la amaliwongo, koma iye adzawathamangitsa.
20 Z Asera tłusty chleb jego, a on wyda rozkoszy królewskie.
“Dziko la Aseri lidzabereka chakudya chokoma, ndipo iye adzapereka chakudya kwa mafumu.
21 Neftali jako łani wypuszczona, mówiąc piękne słowa.
“Nafutali ali ngati mbawala yayikazi yokhala ndi ana okongola kwambiri.
22 Latorośl płodna Józef, latorośl wyrastająca nad źródłem, a latorośli jego rozchodzą się po murze.
“Yosefe ali ngati mtengo wobereka zipatso, mtengo wobereka zipatso pafupi ndi kasupe, nthambi zake zimayanga pa chipupa cha mwala.
23 Acz gorzkością napełnili go, i strzelali nań, a nienawidzili go strzelcy.
Alenje a uta anamuchita chiwembu mwankhanza; anamuthamangitsa ndi mauta awo.
24 Jednak został potężny łuk jego, a zmocniły się ramiona rąk jego, w rękach mocnego Boga Jakóbowego, stąd się stał pasterzem i opoką Izraelową.
Koma uta wake sunagwedezeke, ndi manja ake amphamvu aja analimbika, chifukwa cha mphamvu za Mulungu Wamphamvu wa Yakobo, chifukwa ali Mʼbusa ndi Thanthwe la Israeli.
25 Od Boga ojca twego, który cię wspomógł, i od Wszechmogącego, któryć błogosławił błogosławieństwy niebieskiemi z wysoka, i błogosławieństwy przepaści leżącej głęboko, i błogosławieństwy piersi i żywota.
Chifukwa cha Mulungu wa makolo ako amene amakuthandiza; chifukwa cha Mulungu Wamphamvu, amene amakudalitsa ndi mvula yochokera kumwamba, ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka, ndipo amakudalitsa pokupatsa ana ambiri ndi ngʼombe zambiri.
26 Błogosławieństwa ojca twego mocniejsze będą nad błogosławieństwa przodków moich, aż do granic pagórków wiecznych; będą nad głową Józefową, i nad wierzchem głowy odłączonego między bracią swą.
Madalitso a kholo lako ndi amphamvu kuposa madalitso a mapiri akale oposa zabwino za ku zitunda zamgonagona. Zonse izi zikhale pamutu pa Yosefe, pa mphumi pa wopatulika uja amene anapatulidwa pakati pa abale ake.
27 Benjamin jako wilk porywający, rano jeść będzie łup, a wieczór będzie dzielił korzyść.
“Benjamini ali ngati mʼmbulu wolusa; umene mmawa umapha ndi kudya zofunkha, ndipo madzulo umagawa zofunkhazo,”
28 Teć wszystkie są dwanaście pokolenia Izraelskie, i to, co im powiedział ojciec ich, i błogosławił im; każdemu według błogosławieństwa jego błogosławił im.
Onse awa ndi mafuko khumi ndi awiri a Israeli, ndipo zimenezi ndi zomwe abambo awo ananena pamene anawadalitsa, kuwapatsa aliyense madalitso ake womuyenera iye.
29 A rozkazał im, i rzekł do nich: Ja będę przyłączon do ludu mego; pogrzebcież mię z ojcy moimi w jaskini, która jest na polu Efrona Hetejczyka;
Kenaka Yakobo analamula ana ake nati: “Ine ndatsala pangʼono kufa. Tsono mukandiyike pamodzi ndi makolo anga mʼphanga la mʼmunda wa Efroni Mhiti.
30 W jaskini, która jest na polu Machpela, która jest na przeciwko Mamre w ziemi Chananejskiej, którą kupił Abraham z rolą od Efrona Hetejczyka, w osiadłość grobu.
Ili ndi phanga la mʼmunda wa Makipela, pafupi ndi Mamre mʼdziko la Kanaani. Abrahamu anagula phangalo pamodzi ndi munda womwe kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda.
31 Tam pogrzebiono Abrahama, i Sarę, żonę jego; tam pogrzebiono Izaaka, i Rebekę żonę jego; tamem też pogrzebał Liję.
Kumeneko kunayikidwa Abrahamu ndi mkazi wake Sara, Isake ndi mkazi wake Rebeka ndipo ndinayikakonso Leya.
32 A kupiono tę rolą i jaskinią, która na niej, od synów Hetowych.
Munda ndi manda amene ali mʼmenemo zinagulidwa kwa Ahiti.”
33 Tedy przestawszy Jakób mówić do synów swoich, złożył nogi swe na łoże i umarł, i przyłączon jest do ludu swego.
Yakobo atamaliza kupereka malangizo kwa ana ake, anabwezera miyendo yake pa bedi, namwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake.

< Rodzaju 49 >