< اعداد 33 >

این است سفرنامهٔ قوم اسرائیل از روزی که به رهبری موسی و هارون از مصر بیرون آمدند. 1
Malo otsatirawa ndi omwe Aisraeli anayima pa maulendo awo atatuluka mʼdziko la Igupto mʼmagulu awo motsogozedwa ndi Mose ndi Aaroni.
موسی طبق دستور خداوند مراحل سفر آنها را نوشته بود. 2
Mose analemba malo amene anayambira maulendo awo molamulidwa ndi Yehova. Maulendo awo ndi malo omwe anayambira ndi awa:
آنها در روز پانزدهم از ماه اول، یعنی یک روز بعد از پِسَح از شهر رَمِسیس مصر خارج شدند. در حالی که مصری‌ها همۀ نخست‌زادگان خود را که خداوند شب قبل آنها را کشته بود دفن می‌کردند، قوم اسرائیل با سربلندی از مصر بیرون آمدند. این امر نشان داد که خداوند از تمامی خدایان مصر قویتر است. 3
Aisraeli ananyamuka kuchokera ku Ramesesi pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, itangotha Paska. Iwo anatuluka nayenda molimba mtima Aigupto onse akuona,
4
pamene ankayika maliro a ana awo oyamba kubadwa, omwe Yehova anawakantha pakati pawo chifukwa Yehova anaweruza milungu yawo.
پس از حرکت از رَمِسیس، قوم اسرائیل در سوکوت اردو زدند و از آنجا به ایتام که در حاشیهٔ بیابان است رفتند. 5
Aisraeli atachoka ku Ramesesi, anamanga misasa yawo ku Sukoti.
6
Atachoka ku Sukoti anakamanga misasa yawo ku Etamu, mʼmbali mwa chipululu.
بعد به فی‌هاحیروت نزدیک بعل صفون رفته، در دامنهٔ کوه مجدل اردو زدند. 7
Ndipo atachoka ku Etamu, anabwerera ku Pihahiroti, kummawa kwa Baala-Zefoni, ndipo anamanga misasa yawo pafupi ndi Migidoli.
سپس از آنجا کوچ کرده، از میان دریای سرخ گذشتند و به بیابان ایتام رسیدند. سه روز هم در بیابان ایتام پیش رفتند تا به ماره رسیدند و در آنجا اردو زدند. 8
Atachoka ku Pihahiroti anadutsa mʼkati mwa nyanja kupita ku chipululu ndipo atayenda masiku atatu mʼchipululu cha Etamu, anamanga misasa yawo ku Mara.
از ماره کوچ کرده، به ایلیم آمدند که در آنجا دوازده چشمهٔ آب و هفتاد درخت خرما بود، و مدتی در آنجا ماندند. 9
Atachoka ku Mara anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe a madzi khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa 70 ndipo anamanga misasa yawo kumeneko.
از ایلیم به کنار دریای سرخ کوچ نموده، اردو زدند؛ 10
Atachoka ku Elimu anakamanga misasa yawo mʼmbali mwa Nyanja Yofiira.
پس از آن به صحرای سین رفتند. 11
Atachoka ku Nyanja Yofiira anakamanga misasa yawo mʼchipululu cha Sini.
سپس به ترتیب به دُفقه، 12
Atachoka ku chipululu cha Sini anakamanga ku Dofika.
الوش، 13
Atachoka ku Dofika anakamanga misasa yawo ku Alusi.
و رفیدیم که در آنجا آب نوشیدنی یافت نمی‌شد، رفتند. 14
Atachoka ku Alusi anakamanga misasa yawo ku Refidimu, kumene kunalibe madzi woti anthu ndi kumwa.
از رفیدیم به صحرای سینا و از آنجا به قبروت هتاوه و سپس از قبروت هتاوه به حصیروت کوچ کردند و بعد به ترتیب به نقاط زیر رفتند: از حصیروت به رتمه، از رتمه به رمون فارص، از رمون فارص به لبنه، از لبنه به رسه، از رسه به قهیلاته، از قهیلاته به کوه شافر، از کوه شافر به حراده، از حراده به مقهیلوت، از مقهیلوت به تاحت، از تاحت به تارح، از تارح به متقه، از متقه به حشمونه، از حشمونه به مسیروت، از مسیروت به بنی‌یعقان، از بنی‌یعقان به حورالجدجاد، از حورالجدجاد به یطبات، از یطبات به عبرونه، از عبرونه به عصیون جابر، از عصیون جابر به قادش (در بیابان صین)، از قادش به کوه هور (در مرز سرزمین ادوم). 15
Atachoka ku Refidimu anakamanga ku chipululu cha Sinai
16
Atachoka ku chipululu cha Sinai anakamanga misasa yawo ku Kiburoti-Hataava.
17
Atachoka ku Kiburoti-Hataava anakamanga misasa yawo ku Heziroti.
18
Atachoka ku Heziroti anakamanga ku Ritima.
19
Atachoka ku Ritima anakamanga ku Rimoni-Perezi.
20
Atachoka ku Rimoni-Perezi anakamanga ku Libina.
21
Atachoka ku Libina anakamanga ku Risa.
22
Atachoka ku Risa anakamanga ku Kehelata.
23
Atachoka ku Kehelata anakamanga ku phiri la Seferi.
24
Atachoka ku phiri la Seferi anakamanga ku Harada.
25
Atachoka ku Harada anakamanga ku Mekheloti.
26
Atachoka ku Mekheloti anakamanga ku Tahati.
27
Atachoka ku Tahati anakamanga ku Tera.
28
Atachoka ku Tera anakamanga ku Mitika.
29
Atachoka ku Mitika anakamanga ku Hasimona.
30
Atachoka ku Hasimona anakamanga ku Moseroti.
31
Atachoka ku Moseroti anakamanga ku Beni Yaakani.
32
Atachoka ku Beni Yaakani anakamanga ku Hori-Hagidigadi.
33
Atachoka ku Hori-Hagidigadi anakamanga ku Yotibata.
34
Atachoka ku Yotibata anakamanga ku Abirona.
35
Atachoka ku Abirona anakamanga ku Ezioni-Geberi.
36
Atachoka ku Ezioni-Geberi anakamanga ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini chimene ndi Kadesi.
37
Anachoka ku Kadesi ndi kukamanga ku phiri la Hori, mʼmalire mwa dziko la Edomu.
وقتی در دامنهٔ کوه هور بودند، هارون کاهن به دستور خداوند به بالای کوه هور رفت. وی در سن ۱۲۳ سالگی، در روز اول از ماه پنجم سال چهلم؛ بعد از بیرون آمدن بنی‌اسرائیل از مصر، در آنجا وفات یافت. 38
Molamulidwa ndi Yehova, wansembe Aaroni anakwera ku phiri la Hori kumene anakamwalirira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, mʼchaka cha makumi anayi, Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto.
39
Aaroni anamwalira pa phiri la Hori ali ndi zaka 123.
در این هنگام بود که پادشاه کنعانی سرزمین عراد (واقع در نِگِب کنعان)، اطلاع یافت که قوم اسرائیل به کشورش نزدیک می‌شوند. 40
Mfumu ya Akanaani ya ku Aradi yomwe inkakhala ku Negevi kummwera kwa Kanaani, inamva kuti Aisraeli akubwera.
پس اسرائیلی‌ها از کوه هور به صلمونه کوچ کردند و در آنجا اردو زدند. 41
Atachoka ku phiri la Hori anakamanga ku Zalimoni.
بعد به فونون رفتند. 42
Atachoka ku Zalimoni anakamanga ku Punoni.
پس از آن به اوبوت کوچ کردند 43
Atachoka ku Punoni anakamanga ku Oboti.
و از آنجا به عیی‌عباریم در مرز موآب رفته، در آنجا اردو زدند. 44
Atachoka ku Oboti anakamanga ku Iye-Abarimu.
سپس به دیبون جاد رفتند 45
Atachoka ku Iye-Abarimu anakamanga ku Diboni Gadi.
و از دیبون جاد به علمون دبلاتایم 46
Atachoka ku Diboni Gadi anakamanga ku Alimoni-Dibulataimu.
و از آنجا به کوهستان عباریم، نزدیک کوه نبو کوچ کردند. 47
Atachoka ku Alimoni-Dibulataimu anakamanga mʼmapiri a Abarimu, pafupi ndi Nebo.
سرانجام به دشت موآب رفتند که در کنار رود اردن در مقابل شهر اریحا بود. 48
Atachoka ku mapiri a Abarimu anakamanga ku zigwa za Mowabu mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko.
در دشت موآب، از بیت‌یشیموت تا آبل شطیم در جاهای مختلف، کنار رود اردن اردو زدند. 49
Ali ku zigwa za Mowabu anamanga mʼmbali mwa Yorodani kuchokera ku Beti-Yesimoti mpaka ku Abeli-Sitimu.
زمانی که آنها در کنار رود اردن، در مقابل اریحا اردو زده بودند، خداوند به موسی فرمود که به قوم اسرائیل بگوید: «وقتی که از رود اردن عبور کردید و به سرزمین کنعان رسیدید، 50
Pa zigwa za Mowabu, mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi ku Yeriko, Yehova anawuza Mose kuti,
51
“Nena kwa Aisraeli kuti, ‘Pamene muwoloka Yorodani kulowa mʼdziko la Kanaani,
باید تمامی ساکنان آنجا را بیرون کنید و همهٔ بتها و مجسمه‌هایشان را از بین ببرید و عبادتگاهای واقع در بالای کوهها را که در آنجا بتهایشان را پرستش می‌کنند خراب کنید. 52
mukathamangitse nzika zonse za mʼdzikomo pamaso panu. Mukawononge mafano awo onse a miyala ndi osula ndi malo awo achipembedzo.
من سرزمین کنعان را به شما داده‌ام. آن را تصرف کنید و در آن ساکن شوید. 53
Mukalande dzikolo ndi kukhalamo chifukwa ndakupatsani dziko limenelo kuti mukhalemo.
زمین به تناسب جمعیت قبیله‌هایتان به شما داده خواهد شد. قطعه‌های بزرگتر زمین به قید قرعه بین قبیله‌های بزرگتر و قطعه‌های کوچکتر بین قبیله‌های کوچکتر تقسیم شود. 54
Mukagawane dzikolo pochita maere monga mwa mafuko anu. Kwa omwe ali ambiri, cholowa chambiri, ndipo amene ali ocheperapo, chocheperanso. Chilichonse chimene chidzawagwere iwo mwa maere chidzakhala chawo. Mukaligawane monga mwa mafuko a makolo anu.
ولی اگر تمامی ساکنان آنجا را بیرون نکنید، باقیماندگان مثل خار به چشمهایتان و چون تیغ در پهلویتان فرو خواهند رفت و شما را در آن سرزمین آزار خواهند رساند. 55
“‘Koma ngati simukathamangitsa nzika zimene zili mʼdzikomo, amene mukawalole kukhalamo adzakhala ngati zisonga mʼmaso mwanu ndi ngati minga mʼmbali mwanu. Adzakubweretserani mavuto mʼdziko limene mudzakhalemolo.
آری، اگر آنان را بیرون نکنید آنگاه من شما را هلاک خواهم کرد همان‌طور که قصد داشتم شما آنها را هلاک کنید.» 56
Ndipo pamenepo ndidzachitira inu zomwe ndinaganiza kuwachitira iwowo.’”

< اعداد 33 >