< یونس 3 >
آنگاه خداوند بار دیگر به یونس فرمود: | 1 |
Ndipo Yehova anayankhula ndi Yona kachiwiri kuti,
«به شهر بزرگ نینوا برو و پیامی را که به تو میدهم، به آنها اعلام کن!» | 2 |
“Nyamuka, pita ku mzinda waukulu wa Ninive ndipo ukalalikire uthenga umene ndikupatsa.”
یونس اطاعت کرده، به نینوا رفت. نینوا شهر بسیار بزرگی بود به طوری که سه روز طول میکشید تا کسی سراسر آن را بپیماید. | 3 |
Yona anamvera mawu a Yehova ndipo anapita ku Ninive. Tsono Ninive unali mzinda waukulu kwambiri; wofunika masiku atatu kuwudutsa.
یونس وارد شهر شد و پس از طی یک روز راه شروع به موعظه کرده، گفت: «بعد از چهل روز نینوا ویران خواهد شد!» | 4 |
Yona analowa mu mzindawo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye ankalalikira kuti, “Atsala masiku makumi anayi kuti Ninive awonongedwe.”
اهالی شهر حرفهایش را باور کرده، به همه اعلان کردند که روزه بگیرند؛ و همه، از بزرگ تا کوچک، پلاس پوشیدند. | 5 |
Anthu a ku Ninive anakhulupirira Mulungu. Analengeza kuti aliyense, wamkulu ndi wamngʼono yemwe asale zakudya ndipo avale chiguduli.
هنگامی که پادشاه نینوا شنید که یونس چه گفته است از تخت خود پایین آمده، لباس شاهانه را از تن درآورد و پلاس پوشیده، در خاکستر نشست. | 6 |
Mfumu ya ku Ninive itamva nkhaniyi, inatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake waufumu ndipo inavala chiguduli ndi kukhala pansi pa fumbi.
پادشاه و بزرگان دربار او این پیام را به سراسر شهر فرستادند: «نه مردم و نه حیوانات، هیچکدام نباید چیزی بخورند و حتی آب بنوشند. | 7 |
Tsono mfumuyo inalengeza mu Ninive kuti, “Mwa lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake: “Munthu aliyense kapenanso nyama, ngʼombe kapena nkhosa, zisadye kanthu kalikonse; musazilole kuti zidye kapena kumwa.
همهٔ مردم باید پلاس پوشیده، به درگاه خداوند التماس کنند و از راههای بد خود بازگشت نموده، از اعمال زشت خود دست بکشند. | 8 |
Koma anthu avale ziguduli, ndipo nyamanso aziveke ziguduli. Munthu aliyense azifuwula kwa Mulungu ndi mphamvu zake zonse. Anthuwo asiye makhalidwe awo oyipa ndi machitidwe achiwawa.
کسی چه میداند، شاید خداوند از خشم خود برگردد و بر ما ترحم کرده، ما را از بین نبرد.» | 9 |
Angadziwe ndani? Mwina Mulungu nʼkutikhululukira ndipo mwa chifundo chake nʼkuleka kutikwiyira, ifeyo osawonongedwa.”
وقتی خدا دید آنها از راههای بد خود دست کشیدهاند بر آنها ترحم کرده، بلایی را که گفته بود بر ایشان نفرستاد. | 10 |
Mulungu ataona zimene anthuwo anachita, ndi mmene anasiyira makhalidwe awo oyipa, anawachitira chifundo ndipo sanabweretse chiwonongeko chimene anawaopseza nacho.