< UmTshumayeli 4 >

1 Mina ngasengiphenduka ngabona incindezelo zonke ezenziwa ngaphansi kwelanga; khangela-ke inyembezi zabacindezelweyo, njalo babengelamduduzi; lehlangothini lwababacindezelayo kwakulamandla, kodwa babengelamduduzi.
Ndinayangʼananso ndi kuona chipsinjo chimene chimachitika pansi pano: ndinaona misozi ya anthu opsinjika, ndipo iwo alibe owatonthoza; mphamvu zinali ndi anthu owapsinjawo ndipo iwonso analibe owatonthoza.
2 Ngakho ngancoma abafileyo, abavele sebefile, okwedlula abaphilayo, abalokhu besaphila.
Ndipo ndinanena kuti akufa, amene anafa kale, ndi osangalala kuposa amoyo, amene akanalibe ndi moyo.
3 Yebo ungcono kulabo bobabili, ongakabi khona, ongabonanga umsebenzi omubi owenziwa ngaphansi kwelanga.
Koma wopambana onsewa ndi amene sanabadwe, amene sanaone zoyipa zimene chimachitika pansi pano.
4 Ngasengibona mina wonke umtshikatshika lempumelelo yonke yomsebenzi, ngoba lokhu kungumhawu womuntu ovela kumakhelwane wakhe. Lokhu lakho kuyize lokukhathazeka komoya.
Ndipo ndinazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
5 Isiphukuphuku sigoqa izandla zaso sidle inyama yaso.
Chitsiru chimangoti manja ake lobodo ndi kudzipha chokha ndi njala.
6 Singcono isandla esigcwele ukuthula kulezandla ezimbili ezigcwele ukutshikatshika lokukhathazeka komoya.
Nʼkwabwino kukhala ndi dzanja limodzi lodzaza uli pa mtendere, kuposa kukhala ndi manja awiri odzaza uli pa mavuto, ndipo uku nʼkungodzivuta chabe.
7 Mina ngasengiphenduka ngabona ize ngaphansi kwelanga.
Ndinaonanso chinthu china chopanda phindu pansi pano:
8 Kukhona oyedwa, njalo kakho owesibili, yebo kalamntwana kumbe umfowabo, njalo kakulakuphela komtshikatshika wakhe wonke, lelihlo lakhe kalisuthiswa yinotho, njalo katsho ukuthi: Ngitshikatshikela bani, ngenze umphefumulo wami uswele okuhle? Lokhu lakho kuyize, yebo, kungumsebenzi omubi.
Panali munthu amene anali yekhayekha; analibe mwana kapena mʼbale. Ntchito yake yolemetsa sinkatha, ndipo maso ake sankakhutitsidwa ndi chuma chake. Iye anadzifunsa kuti, “Kodi ntchito yosautsayi ndikuyigwirira yani? Nanga nʼchifukwa chiyani ndikudzimana chisangalalo?” Izinso ndi zopandapake, zosasangalatsa!
9 Ababili bangcono kuloyedwa, ngoba balomvuzo omuhle ngokutshikatshika kwabo.
Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha, chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu:
10 Ngoba uba besiwa omunye uzamvusa umngane wakhe; kodwa maye kuye oyedwa nxa esiwa, ngoba kungekho owesibili ongamvusa.
Ngati winayo agwa, mnzakeyo adzamudzutsa. Koma tsoka kwa munthu amene agwa ndipo alibe wina woti amudzutse!
11 Futhi uba ababili belala ndawonye, ngakho balokukhudumala; kodwa ngoyedwa angakhudumala njani?
Komanso ngati anthu awiri agona malo amodzi, adzafunditsana. Koma nanga mmodzi angadzifunditse yekha?
12 Njalo uba omunye engehlula oyedwa, ababili bazamelana laye; lentambo elemicu emithathu kayiqanyulwa masinyane.
Munthu mmodzi angathe kugonjetsedwa, koma anthu awiri akhoza kudziteteza. Chingwe cha maulusi atatu sichidukirapo.
13 Umfana ongumyanga ohlakaniphileyo ungcono kulenkosi endala eyisithutha engasakwazi ukwelulekwa.
Wachinyamata wosauka koma wanzeru aposa mfumu yokalamba koma yopusa imene simvanso malangizo.
14 Ngoba uyaphuma entolongweni ukuthi abe yinkosi, lanxa futhi owayezelwe embusweni wakhe esiba ngumyanga.
Wachinyamatayo angathe kuchokera ku ndende ndi kudzakhala mfumu, kapena angathe kubadwa wosauka mʼdziko la mfumuyo.
15 Ngabona bonke abaphilayo abahamba ngaphansi kwelanga, lomfana wesibili ozakuma esikhundleni sakhe.
Ndipo ndinaona kuti iwo onse amene anakhala ndi moyo ndi kuyenda pansi pano anatsatira wachinyamatayo, amene anatenga malo a mfumu.
16 Kakulasiphetho sabantu bonke, sabo bonke ababephambi kwabo, lalabo abeza emva kabayikuthokoza ngaye. Isibili lokhu lakho kuyize lokukhathazeka komoya.
Mfumu ikhoza kulamulira anthu osawerengeka, komabe itamwalira, palibe amene adzayamikire zomwe mfumuyo inachita. Izinso ndi zopandapake, nʼkungozivuta chabe.

< UmTshumayeli 4 >