< 1 Jaona 1 >
1 Tam-pifotorañey i Tsaran-kaveloñey, ie i jinanji’aiy, niisam-pihaino’aiy, nisambà’ay naho tsinapa-pità’aiy.
Tikukulalikirani za Mawu a moyo amene analipo kuyambira pachiyambi, amene tinawamva, amene tinawaona ndi maso athu, amene tinawapenyetsetsa, ndipo tinawakhudza ndi manja athu.
2 (Fa naboake i haveloñey le niisa’ay, naho mitalily, vaho itaroña’ay i haveloñe nainai’e aman-dRae ao vaho nabentatse ama’aiy.) (aiōnios )
Moyowo unaoneka, tinawuona ndipo tikuchitira umboni. Tikukulalikirani za moyo wosatha umene unali ndi Atate ndipo unaonekera kwa ife. (aiōnios )
3 Taroñe’ay ka o niisa’ay naho jinanji’aio, soa te hitrao-drehak’ ama’ay nahareo. Toe miharo rehak’ aman-dRae naho amy Ana’e Iesoà Norizañey zahay.
Tikukulalikirani chimene tinachiona ndi kumva, kuti inuyo muyanjane nafe. Kuyanjana kwathu, tikuyanjana ndi Atate ndiponso ndi Mwana wawo, Yesu Khristu.
4 Isokira’ay o raha zao, hañenefañe ty haeha’areo.
Tikukulemberani zimenezi kuti chimwemwe chathu chikhale chathunthu.
5 Zao ty entañe nijinanjiñe’ay naho itaroña’ay, Toe Hazavàñe t’i Andrianañahare; ie tsy aman’ ieñe, ndra loli’e.
Uthenga umene tinamva kwa Iye ndipo tikuwulalikira kwa inu ndi uwu: Mulungu ndiye kuwunika ndipo mwa Iye mulibe mdima konse.
6 Naho mihàboke t’ie mitrao-drehak’ ama’e fe mañavelo amy ieñey ao, le mandañitse, tsy mañavelo an-katò.
Tikanena kuti timayanjana naye, koma nʼkumayendabe mu mdima, tikunama ndipo sitikuchita choonadi.
7 F’ie mañavelo an-kazavàñe, amy te Ie ro an-kazavàñ’ ao, le mitrao-drehake tika vaho liove’ ty lio’ Iesoà Ana’e amy ze fonga tahiñe.
Koma tikamayenda mʼkuwunika, monga Iye ali mʼkuwunika, pamenepo timayanjana wina ndi mnzake, ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
8 Aa naho mieva t’ie tsy aman-kakeo le mamañahy vatañe, vaho tsy aman-tika ty hatò.
Tikanena kuti tilibe tchimo, tikudzinyenga tokha ndipo mwa ife mulibe choonadi.
9 Ie miantoke hakeo, le migahiñe naho vantan-dre hañaha o tahin-tikañeo, hañaliova’e amy ze fonga hatsivokarañe.
Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.
10 Ie manao te mb’e lia tsy nanao hakeo le mampandañitse aze vaho tsy aman-tika o tsara’eo.
Ife tikanena kuti sitinachimwe, tikumutenga Mulungu kukhala wonama, ndipo Mawu ake sali mwa ife.