< Zaccharias Propheta 9 >
1 onus verbi Domini in terra Adrach et Damasci requiei eius quia Domini est oculus hominis et omnium tribuum Israhel
Mawu a Yehova odzudzula dziko la Hadiraki ndi mzinda wa Damasiko pakuti maso a anthu ndiponso mafuko onse a Israeli ali pa Yehova—
2 Emath quoque in terminis eius et Tyrus et Sidon adsumpserunt quippe sibi sapientiam valde
ndiponso mzinda wa Hamati, umene ukuchita malire ndi dzikoli, komanso pa Turo ndi Sidoni, ngakhale kuti iwo ndi anzeru kwambiri.
3 et aedificavit Tyrus munitionem suam et coacervavit argentum quasi humum et aurum ut lutum platearum
Ndipo Turo anadzimangira linga; wadziwunjikira siliva ngati fumbi, ndi golide ngati zinyalala za mʼmisewu.
4 ecce Dominus possidebit eam et percutiet in mari fortitudinem eius et haec igni devorabitur
Taonani Ambuye adzamulanda chuma chakecho ndi kuwononga mphamvu zake mʼnyanja, ndipo adzapserera ndi moto.
5 videbit Ascalon et timebit et Gaza et dolebit nimis et Accaron quoniam confusa est spes eius et peribit rex de Gaza et Ascalon non habitabitur
Mzinda wa Asikeloni udzaona zimenezi, nʼkuchita mantha; Gaza adzanjenjemera ndi ululu, chimodzimodzinso Ekroni, chifukwa chiyembekezo chake chidzatheratu. Mfumu ya ku Gaza idzaphedwa ndipo Asikeloni adzakhala opanda anthu.
6 et sedebit separator in Azoto et disperdam superbiam Philisthinorum
Mu Asidodi mudzakhala mlendo, ndipo ndidzathetsa kunyada kwa Afilisti.
7 et auferam sanguinem eius de ore eius et abominationes eius de medio dentium eius et relinquetur etiam ipse Deo nostro et erit quasi dux in Iuda et Accaron quasi Iebuseus
Ndidzachotsa nyama ya magazi mʼkamwa mwawo, chakudya choletsedwa mʼmano mwawo. Amene atsala adzakhala anthu a Mulungu wathu, adzasanduka atsogoleri mu Yuda, ndipo Ekroni adzakhala ngati Ayebusi.
8 et circumdabo domum meam ex his qui militant mihi euntes et revertentes et non transibit super eos ultra exactor quia nunc vidi in oculis meis
Koma Ine ndidzalondera Nyumba yanga ndi kuyiteteza kwa ankhondo osakaza. Palibenso mdani amene adzagonjetse anthu anga, pakuti tsopano ndikuwayangʼanira.
9 exulta satis filia Sion iubila filia Hierusalem ecce rex tuus veniet tibi iustus et salvator ipse pauper et ascendens super asinum et super pullum filium asinae
Sangalala kwambiri, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni! Fuwula, mwana wamkazi wa Yerusalemu! Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe, yolungama ndi yogonjetsa adani, yodzichepetsa ndi yokwera pa bulu, pa mwana wamphongo wa bulu.
10 et disperdam quadrigam ex Ephraim et equum de Hierusalem et dissipabitur arcus belli et loquetur pacem gentibus et potestas eius a mari usque ad mare et a fluminibus usque ad fines terrae
Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efereimu ndi akavalo ankhondo ku Yerusalemu, ndipo uta wankhondo udzathyoka. Mfumuyo idzabweretsa mtendere pakati pa mitundu ya anthu. Ulamuliro wake udzayambira ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina, ndipo kuchokera ku Mtsinje (Yufurate) mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
11 tu quoque in sanguine testamenti tui emisisti vinctos tuos de lacu in quo non est aqua
Tsono kunena za iwe, chifukwa cha magazi a pangano lako ndi Ine, ndidzamasula amʼndende ako, ndidzawatulutsa mʼdzenje lopanda madzi.
12 convertimini ad munitionem vincti spei hodie quoque adnuntians duplicia reddam tibi
Bwererani ku malo anu otetezedwa, inu amʼndende achiyembekezo; ngakhale tsopano ndikulengeza kuti ndidzakubwezerani zabwino mowirikiza.
13 quoniam extendi mihi Iudam quasi arcum implevi Ephraim et suscitabo filios tuos Sion super filios tuos Graecia et ponam te quasi gladium fortium
Ndidzakoka Yuda monga ndimakokera uta wanga, ndipo Efereimu ndiye muvi wake. Ndidzadzutsa ana ako iwe Ziyoni, kulimbana ndi ana ako iwe Grisi, ndipo ndidzakusandutsa iwe lupanga la munthu wankhondo.
14 et Dominus Deus super eos videbitur et exibit ut fulgur iaculum eius et Dominus Deus in tuba canet et vadet in turbine austri
Pamenepo Yehova adzaonekera kwa anthu ake; mivi yake idzangʼanima ngati chingʼaningʼani. Ambuye Yehova adzaliza lipenga; ndipo adzayenda mu mkuntho wochokera kummwera,
15 Dominus exercituum proteget eos et devorabunt et subicient lapidibus fundae et bibentes inebriabuntur quasi vino et replebuntur ut fialae et quasi cornua altaris
ndipo Yehova Wamphamvuzonse adzawateteza. Iwo adzawononga ndipo adzagonjetsa ndi miyala ya legeni. Adzamwa magazi ndi kubangula ngati amwa vinyo; magazi adzayenderera ngati a mʼmbale yowazira magazi pa ngodya za guwa lansembe.
16 et salvabit eos Dominus Deus eorum in die illa ut gregem populi sui quia lapides sancti elevantur super terram eius
Tsiku limenelo Yehova Mulungu wawo adzawapulumutsa pakuti anthu ake ali ngati nkhosa. Adzanyezimira mʼdziko lake ngati miyala yokongola pa chipewa chaufumu.
17 quid enim bonum eius est et quid pulchrum eius nisi frumentum electorum et vinum germinans virgines
Taonani chikoka ndi kukongola kwawo! Tirigu adzasangalatsa anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.