< Canticum Canticorum 8 >
1 quis mihi det te fratrem meum sugentem ubera matris meae ut inveniam te foris et deosculer et iam me nemo despiciat
Ukanakhala kuti ndiwe mlongo wanga, amene anayamwa mawere a amayi anga! Ndikanakumana nawe pa njira, ndikanakupsompsona, ndipo palibe wina aliyense akanandinyoza.
2 adprehendam te et ducam in domum matris meae ibi me docebis et dabo tibi poculum ex vino condito et mustum malorum granatorum meorum
Ndikanakutenga ndi kukulowetsa mʼnyumba ya amayi anga, amayi amene anandiphunzitsa, ndikanakupatsa vinyo wotsekemera kuti umwe, zotsekemera za makangadza.
3 leva eius sub capite meo et dextera illius amplexabitur me
Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.
4 adiuro vos filiae Hierusalem ne suscitetis et evigilare faciatis dilectam donec ipsa velit
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani: musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa mpaka pamene chifunire ichocho.
5 quae est ista quae ascendit de deserto deliciis affluens et nixa super dilectum suum sub arbore malo suscitavi te ibi corrupta est mater tua ibi violata est genetrix tua
Kodi ndani uyo akutuluka ku chipululuyo, atatsamira wokondedwa wakeyo? Mkazi Ndinakudzutsa pa tsinde pa mtengo wa apulosi, pamenepo ndi pamene amayi anachirira, pamenepo ndi pamene wokubereka anamva ululu pokubala iweyo.
6 pone me ut signaculum super cor tuum ut signaculum super brachium tuum quia fortis est ut mors dilectio dura sicut inferus aemulatio lampades eius lampades ignis atque flammarum (Sheol )
Undiyike pamtima pako ngati chidindo, ngati chidindo cha pa dzanja lako; pakuti chikondi nʼchamphamvu ngati imfa, nsanje ndiyaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti lawilawi ngati malawi a moto wamphamvu. (Sheol )
7 aquae multae non poterunt extinguere caritatem nec flumina obruent illam si dederit homo omnem substantiam domus suae pro dilectione quasi nihil despicient eum
Madzi ochuluka sangachizimitse chikondi, mitsinje singachikokolole chikondicho. Ngati wina apereka chuma chonse cha mʼnyumba mwake chifukwa cha chikondi, adzangonyozeka nazo kotheratu.
8 soror nostra parva et ubera non habet quid faciemus sorori nostrae in die quando adloquenda est
Ife tili naye mlongo wathu wamngʼono, koma alibe mawere, kodi tidzamuchitira chiyani mlongo wathuyu pa tsiku limene adzamufunsire?
9 si murus est aedificemus super eum propugnacula argentea si ostium est conpingamus illud tabulis cedrinis
Ngati iye ndi khoma, tidzamumangira nsanja ya siliva. Ngati iye ndi chitseko, tidzamutchinga ndi matabwa a mkungudza.
10 ego murus et ubera mea sicut turris ex quo facta sum coram eo quasi pacem repperiens
Ine ndili ngati khoma, ndipo mawere anga ndi nsanja zake. Tsono mʼmaso mwa bwenzi langa ndine wobweretsa mtendere.
11 vinea fuit Pacifico in ea quae habet populos tradidit eam custodibus vir adfert pro fructu eius mille argenteos
Solomoni anali ndi munda wampesa ku Baala-Hamoni; iyeyo anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi, aliyense mwa iwo ankayenera kupereka ndalama zasiliva 1,000 mʼmalo mwa zipatso zake.
12 vinea mea coram me est mille tui Pacifice et ducenti his qui custodiunt fructus eius
Koma munda wanga wampesa ndi wangawanga ndiponso wa ine ndekha. Iwe Solomoni, khala nazo ndalama zasiliva 1,000 ndipo ndalama zasiliva 200 ndi za amene akusamalira mundawo.
13 quae habitas in hortis amici auscultant fac me audire vocem tuam
Iwe amene umakhala mʼminda uli pamodzi ndi anzako, ndilole kuti ndimve liwu lako!
14 fuge dilecte mi et adsimilare capreae hinuloque cervorum super montes aromatum
Fulumira wokondedwa wanga, ndipo ukhale ngati gwape kapena mwana wa mbawala wothamanga mʼmapiri mʼmene mumamera mbewu zokometsera chakudya.