< Canticum Canticorum 2 >
1 ego flos campi et lilium convallium
Ine ndine duwa la ku Saroni, duwa lokongola la ku zigwa.
2 sicut lilium inter spinas sic amica mea inter filias
Monga duwa lokongola pakati pa minga ndi momwe alili wokondedwa wanga pakati pa atsikana.
3 sicut malum inter ligna silvarum sic dilectus meus inter filios sub umbra illius quam desideraveram sedi et fructus eius dulcis gutturi meo
Monga mtengo wa apulosi pakati pa mitengo ya mʼnkhalango ndi momwe alili bwenzi langa pakati pa anyamata. Ndimakondwera kukhala pansi pa mthunzi wako, ndipo chipatso chake ndi chokoma mʼkamwa mwanga.
4 introduxit me in cellam vinariam ordinavit in me caritatem
Iye wanditengera ku nyumba yaphwando, ndipo mbendera yake yozika pa ine ndi chikondi.
5 fulcite me floribus stipate me malis quia amore langueo
Undidyetse keke ya mphesa zowuma, unditsitsimutse ndi ma apulosi, pakuti chikondi chandifowoketsa.
6 leva eius sub capite meo et dextera illius amplexabitur me
Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere, ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.
7 adiuro vos filiae Hierusalem per capreas cervosque camporum ne suscitetis neque evigilare faciatis dilectam quoadusque ipsa velit
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo: Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa mpaka pamene chifunire ichocho.
8 vox dilecti mei ecce iste venit saliens in montibus transiliens colles
Tamverani bwenzi langa! Taonani! Uyu akubwera apayu, akulumphalumpha pa mapiri, akujowajowa pa zitunda.
9 similis est dilectus meus capreae hinuloque cervorum en ipse stat post parietem nostrum despiciens per fenestras prospiciens per cancellos
Bwenzi langa ali ngati gwape kapena mwana wa mbawala. Taonani! Uyo wayima kuseri kwa khoma lathulo, akusuzumira mʼmazenera, akuyangʼana pa mpata wa zenera.
10 et dilectus meus loquitur mihi surge propera amica mea formonsa mea et veni
Bwenzi langa anayankha ndipo anati kwa ine, “Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga, ndipo tiye tizipita.
11 iam enim hiemps transiit imber abiit et recessit
Ona, nyengo yozizira yatha; mvula yatha ndipo yapitiratu.
12 flores apparuerunt in terra tempus putationis advenit vox turturis audita est in terra nostra
Maluwa ayamba kuoneka pa dziko lapansi; nthawi yoyimba yafika, kulira kwa njiwa kukumveka mʼdziko lathu.
13 ficus protulit grossos suos vineae florent dederunt odorem surge amica mea speciosa mea et veni
Mtengo wankhuyu ukubereka zipatso zake zoyambirira; mitengo ya mpesa ya maluwa ikutulutsa fungo lake. Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga tiye tizipita.”
14 columba mea in foraminibus petrae in caverna maceriae ostende mihi faciem tuam sonet vox tua in auribus meis vox enim tua dulcis et facies tua decora
Nkhunda yanga yokhala mʼmingʼalu ya thanthwe, mʼmalo obisala a mʼmbali mwa phiri, onetsa nkhope yako, nʼtamvako liwu lako; pakuti liwu lako ndi lokoma, ndipo nkhope yako ndi yokongola.
15 capite nobis vulpes vulpes parvulas quae demoliuntur vineas nam vinea nostra floruit
Mutigwirire nkhandwe, nkhandwe zingʼonozingʼono zimene zikuwononga minda ya mpesa, minda yathu ya mpesa imene yayamba maluwa.
16 dilectus meus mihi et ego illi qui pascitur inter lilia
Bwenzi langa ndi wangadi ndipo ine ndine wake; amadyetsa gulu lake la ziweto pakati pa maluwa okongola.
17 donec adspiret dies et inclinentur umbrae revertere similis esto dilecte mi capreae aut hinulo cervorum super montes Bether
Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira ndipo mithunzi ikayamba kuthawa, unyamuke bwenzi langa, ndipo ukhale ngati gwape kapena ngati mwana wa mbawala pakati pa mapiri azigwembezigwembe.