< Psalmorum 69 >
1 in finem pro his qui commutabuntur David salvum me fac Deus quoniam intraverunt aquae usque ad animam meam
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Potsata mayimbidwe a “Akakombo.” Pulumutseni Inu Mulungu, pakuti madzi afika mʼkhosi
2 infixus sum in limum profundi et non est substantia veni in altitudines maris et tempestas demersit me
Ine ndikumira mʼthope lozama mʼmene mulibe popondapo. Ndalowa mʼmadzi ozama; mafunde andimiza.
3 laboravi clamans raucae factae sunt fauces meae defecerunt oculi mei dum spero in Deum meum
Ndafowoka ndikupempha chithandizo; kummero kwanga kwawuma gwaa, mʼmaso mwanga mwada kuyembekezera Mulungu wanga.
4 multiplicati sunt super capillos capitis mei qui oderunt me gratis confortati sunt qui persecuti sunt me inimici mei iniuste quae non rapui tunc exsolvebam
Iwo amene amadana nane popanda chifukwa ndi ochuluka kuposa tsitsi la kumutu kwanga; ambiri ndi adani anga popanda chifukwa, iwo amene akufunafuna kundiwononga. Ndikukakamizidwa kubwezera zomwe sindinabe.
5 Deus tu scis insipientiam meam et delicta mea a te non sunt abscondita
Mukudziwa uchitsiru wanga, Inu Mulungu, kulakwa kwanga sikuli kobisika kwa Inu.
6 non erubescant in me qui expectant te Domine Domine virtutum non confundantur super me qui quaerunt te Deus Israhel
Iwo amene amadalira Inu asanyozedwe chifukwa cha ine, Inu Ambuye Wamphamvuzonse. Iwo amene amafunafuna Inu asachititsidwe manyazi chifukwa cha ine, Inu Mulungu wa Israeli.
7 quoniam propter te sustinui obprobrium operuit confusio faciem meam
Pakuti ndimapirira kunyozedwa chifukwa cha Inu, ndipo manyazi amaphimba nkhope yanga.
8 extraneus factus sum fratribus meis et peregrinus filiis matris meae
Ndine mlendo kwa abale anga, munthu wakudza kwa ana aamuna a amayi anga;
9 quoniam zelus domus tuae comedit me et obprobria exprobrantium tibi ceciderunt super me
pakuti changu chochitira nyumba yanu chandiphetsa ndipo chipongwe cha iwo amene amanyoza Inu chandigwera.
10 et operui in ieiunio animam meam et factum est in obprobrium mihi
Pamene ndikulira ndi kusala kudya, ndiyenera kupirira kunyozedwa;
11 et posui vestimentum meum cilicium et factus sum illis in parabolam
pomwe ndavala chiguduli, anthu amandiseweretsa.
12 adversum me exercebantur qui sedebant in porta et in me psallebant qui bibebant vinum
Iwo amene amakhala pa chipata amandinena, ndipo ine ndine nyimbo ya zidakwa.
13 ego vero orationem meam ad te Domine tempus beneplaciti Deus in multitudine misericordiae tuae exaudi me in veritate salutis tuae
Koma ndikupempha kwa Inu Ambuye, pa nthawi yanu yondikomera mtima; mwa chikondi chanu chachikulu Inu Mulungu, mundiyankhe pondipulumutsa.
14 eripe me de luto ut non infigar liberer ab his qui oderunt me et de profundis aquarum
Mundilanditse kuchoka mʼmatope, musalole kuti ndimire, pulumutseni ine kwa iwo amene amadana nane, kuchoka mʼmadzi ozama.
15 non me demergat tempestas aquae neque absorbeat me profundum neque urgeat super me puteus os suum
Musalole kuti chigumula chindimeze, kuya kusandimeze ndipo dzenje lisatseke pakamwa pake kundimiza.
16 exaudi me Domine quoniam benigna est misericordia tua secundum multitudinem miserationum tuarum respice me
Ndiyankheni Inu Yehova mwa ubwino wanu wa chikondi chanu; mwa chifundo chanu chachikulu tembenukirani kwa ine.
17 et ne avertas faciem tuam a puero tuo quoniam tribulor velociter exaudi me
Musabisire nkhope yanu mtumiki wanu, ndiyankheni msanga, pakuti ndili pa mavuto.
18 intende animae meae et libera eam propter inimicos meos eripe me
Bwerani pafupi ndi kundilanditsa; ndiwomboleni chifukwa cha adani anga.
19 tu scis inproperium meum et confusionem et reverentiam meam
Inu mukudziwa momwe ndanyozedwera, kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi; adani anga onse ali pamaso panu.
20 in conspectu tuo sunt omnes qui tribulant me inproperium expectavit cor meum et miseriam et sustinui qui simul contristaretur et non fuit et qui consolaretur et non inveni
Mnyozo waswa mtima wanga ndipo wandisiya wopanda thandizo lililonse; ndinafunafuna ena woti andichitire chisoni, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti anditonthoze, sindinapeze ndi mmodzi yemwe.
21 et dederunt in escam meam fel et in siti mea potaverunt me aceto
Iwo anayika ndulu mʼchakudya changa ndi kundipatsa vinyo wosasa chifukwa cha ludzu.
22 fiat mensa eorum coram ipsis in laqueum et in retributiones et in scandalum
Chakudya chomwe chayikidwa patsogolo pawo chikhale msampha; chikhale chobwezera chilango ndiponso khwekhwe.
23 obscurentur oculi eorum ne videant et dorsum eorum semper incurva
Maso awo adetsedwe kotero kuti asaonenso ndipo misana yawo ipindike mpaka kalekale.
24 effunde super eos iram tuam et furor irae tuae conprehendat eos
Khuthulirani ukali wanu pa iwo; mkwiyo wanu woyaka moto uwathe mphamvu.
25 fiat habitatio eorum deserta et in tabernaculis eorum non sit qui inhabitet
Malo awo akhale wopanda anthu pasapezeke ndi mmodzi yemwe wokhala mʼmatenti awo.
26 quoniam quem tu percussisti persecuti sunt et super dolorem vulnerum meorum addiderunt
Pakuti iwo amazunza amene inu munamuvulaza ndi kuyankhula zowawa kwa amene munawapweteka.
27 adpone iniquitatem super iniquitatem eorum et non intrent in iustitia tua
Awonjezereni kulakwa pa kulakwa kwawo, musalole kuti akhale ndi gawo pa chipulumutso chanu.
28 deleantur de libro viventium et cum iustis non scribantur
Iwo afufutidwe mʼbuku la amoyo ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.
29 ego sum pauper et dolens salus tua Deus suscepit me
Ndikumva zowawa ndi kuzunzika; lolani chipulumutso chanu, Inu Mulungu, chinditeteze.
30 laudabo nomen Dei cum cantico magnificabo eum in laude
Ine ndidzatamanda dzina la Mulungu mʼnyimbo, ndidzalemekeza Iye ndi chiyamiko.
31 et placebit Deo super vitulum novellum cornua producentem et ungulas
Izi zidzakondweretsa Yehova kupambana ngʼombe, kupambananso ngʼombe yayimuna, pamodzi ndi nyanga ndi ziboda zake.
32 videant pauperes et laetentur quaerite Deum et vivet anima vestra
Wosauka adzaona ndipo adzasangalala, Inu amene mumafunafuna Mulungu, mitima yanu ikhale ndi moyo!
33 quoniam exaudivit pauperes Dominus et vinctos suos non despexit
Yehova amamvera anthu osowa ndipo sanyoza anthu ake omangidwa.
34 laudent illum caeli et terra mare et omnia reptilia in eis
Kumwamba ndi dziko lapansi zitamanda Iye, nyanja ndi zonse zomwe zimayenda mʼmenemo,
35 quoniam Deus salvam faciet Sion et aedificabuntur civitates Iudaeae et inhabitabunt ibi et hereditate adquirent eam
pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni ndi kumanganso mizinda ya Yuda, anthu adzakhala kumeneko ndipo dzikolo lidzakhala lawo;
36 et semen servorum eius possidebunt eam et qui diligunt nomen eius habitabunt in ea
ana atumiki ake adzalitenga kukhala cholowa chawo, ndipo iwo amene amakonda dzina lake adzakhala kumeneko.