< Psalmorum 36 >
1 in finem servo Domini David dixit iniustus ut delinquat in semet ipso non est timor Dei ante oculos eius
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova. Uthenga uli mu mtima mwanga wonena za kuchimwa kwa munthu woyipa: Mu mtima mwake mulibe kuopa Mulungu.
2 quoniam dolose egit in conspectu eius ut inveniatur iniquitas eius ad odium
Pakuti iye mʼkuona kwake amadzinyenga yekha kwambiri, sazindikira kapena kudana ndi tchimo lake.
3 verba oris eius iniquitas et dolus noluit intellegere ut bene ageret
Mawu a pakamwa pake ndi oyipa ndi achinyengo; iyeyo waleka kukhala wanzeru ndi kuchita zabwino.
4 iniquitatem meditatus est in cubili suo adstetit omni viae non bonae malitiam autem non odivit
Ngakhale ali pa bedi pake amakonzekera zoyipa; iye amadzipereka yekha ku njira ya uchimo ndipo sakana cholakwa chilichonse.
5 Domine in caelo misericordia tua et veritas tua usque ad nubes
Chikondi chanu Yehova, chimafika ku mayiko a kumwamba, kukhulupirika kwanu mpaka ku mitambo.
6 iustitia tua sicut montes Dei iudicia tua abyssus multa homines et iumenta salvabis Domine
Chilungamo chanu Mulungu chili ngati mapiri aakulu, chiweruzo chanu chili ngati kuzama kwakukulu. Yehova mumasunga munthu pamodzi ndi chinyama.
7 quemadmodum multiplicasti misericordiam tuam Deus filii autem hominum in tegmine alarum tuarum sperabunt
Chikondi chanu chosatha ndi chamtengowapatali! Otchuka pamodzi ndi anthu wamba pakati pa anthu amapeza pothawirapo mu mthunzi wa mapiko anu.
8 inebriabuntur ab ubertate domus tuae et torrente voluntatis tuae potabis eos
Iwo amadyerera zinthu zambiri za mʼnyumba yanu; Inu mumawapatsa chakumwa kuchokera mu mtsinje wanu wachikondwerero.
9 quoniam apud te fons vitae in lumine tuo videbimus lumen
Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo; mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala.
10 praetende misericordiam tuam scientibus te et iustitiam tuam his qui recto sunt corde
Pitirizani chikondi chanu pa iwo amene amakudziwani, chilungamo chanu kwa olungama mtima.
11 non veniat mihi pes superbiae et manus peccatoris non moveat me
Musalole kuti phazi la wodzikuza libwere kulimbana nane, kapena dzanja la oyipa kundithamangitsa.
12 ibi ceciderunt qui operantur iniquitatem expulsi sunt nec potuerunt stare
Onani momwe ochita zoyipa agonera atagwa, aponyeni pansi, kuti asathe kudzukanso!