< Micha Propheta 1 >

1 verbum Domini quod factum est ad Micham Morasthiten in diebus Ioatham Ahaz Ezechiae regum Iuda quod vidit super Samariam et Hierusalem
Yehova anayankhula ndi Mika wa ku Moreseti pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda. Awa ndi masomphenya amene iye anaona onena za Samariya ndi Yerusalemu.
2 audite populi omnes et adtendat terra et plenitudo eius et sit Dominus Deus vobis in testem Dominus de templo sancto suo
Tamverani, inu anthu a mitundu yonse, mvetsera iwe dziko lapansi ndi okhala mʼmenemo, pakuti Ambuye Yehova achitira umboni wokutsutsani, Ambuye akuyankhula ali mʼnyumba yake yopatulika.
3 quia ecce Dominus egreditur de loco suo et descendet et calcabit super excelsa terrae
Taonani! Yehova akubwera kuchokera ku malo ake; Iye akutsika ndipo akuponda pa malo okwera a dziko lapansi.
4 et consumentur montes subtus eum et valles scindentur sicut cera a facie ignis sicut aquae quae decurrunt in praeceps
Mapiri akusungunuka pansi pake, ndipo zigwa zikugawikana ngati phula pa moto, ngati madzi ochokera mʼphiri.
5 in scelere Iacob omne istud et in peccatis domus Israhel quod scelus Iacob nonne Samaria et quae excelsa Iudae nonne Hierusalem
Zonsezi ndi chifukwa cha cholakwa cha Yakobo, chifukwa cha machimo a nyumba ya Israeli. Kodi cholakwa cha Yakobo nʼchiyani? Kodi si Samariya? Kodi malo achipembedzo a Yuda ndi ati? Kodi si Yerusalemu?
6 et ponam Samariam quasi acervum lapidum in agro cum plantatur vinea et detraham in vallem lapides eius et fundamenta eius revelabo
“Choncho Ine ndidzasandutsa Samariya kukhala bwinja, malo odzalamo mphesa. Miyala yake ndidzayitaya ku chigwa ndipo ndidzafukula maziko ake.
7 et omnia sculptilia eius concidentur et omnes mercedes eius conburentur igni et omnia idola eius ponam in perditionem quia de mercedibus meretricis congregata sunt et usque ad mercedem meretricis revertentur
Mafano ake onse ndidzawaphwanyaphwanya; mphatso zake zonse ndidzazitentha ndi moto; ndidzawononga zifanizo zonse za milungu yake. Popeza analandira mphatso zake kuchokera ku malipiro a akazi achiwerewere, mphatsozonso zidzagwiritsidwa ntchito ndi ena ngati malipiro a akazi achiwerewere.”
8 super hoc plangam et ululabo vadam spoliatus et nudus faciam planctum velut draconum et luctum quasi strutionum
Chifukwa cha zimenezi ine ndidzalira momvetsa chisoni; ndidzayenda wopanda nsapato ndi wamaliseche. Ndidzafuwula ngati nkhandwe ndi kulira ngati kadzidzi.
9 quia desperata est plaga eius quia venit usque ad Iudam tetigit portam populi mei usque ad Hierusalem
Pakuti chilonda cha Samariya nʼchosachizika; chafika ku Yuda. Chafika pa chipata chenicheni cha anthu anga, mpaka mu Yerusalemu mwenimwenimo.
10 in Geth nolite adnuntiare lacrimis ne ploretis in domo Pulveris pulvere vos conspergite
Musanene zimenezi ku Gati; musalire nʼkomwe. Mugubuduzike mu fumbi ku Beti-Leafura.
11 et transite vobis habitatio Pulchra confusa ignominia non est egressa quae habitat in Exitu planctum domus Vicinae accipiet ex vobis quae stetit sibimet
Inu anthu okhala ku Safiro, muzipita ku ukapolo muli amaliseche ndi amanyazi. Iwo amene akukhala ku Zanaani sadzatuluka. Beti-Ezeli akulira mwachisoni; chitetezo chake chakuchokerani.
12 quia infirmata est in bonum quae habitat in Amaritudinibus quia descendit malum a Domino in portam Hierusalem
Anthu amene amakhala ku Maroti akubuwula ndi ululu, akuyembekezera thandizo, chifukwa Yehova wabweretsa tsoka, lafika mpaka pa chipata cha Yerusalemu.
13 tumultus quadrigae stuporis habitanti Lachis principium peccati est filiae Sion quia in te inventa sunt scelera Israhel
Inu anthu okhala ku Lakisi mangani akavalo ku magaleta. Inu amene munayamba kuchimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni, pakuti zolakwa za Israeli zinapezeka pakati panu.
14 propterea dabit emissarios super hereditatem Geth domus Mendacii in deceptionem regibus Israhel
Chifukwa chake perekani mphatso zolawirana ndi a ku Moreseti Gati. Mzinda wa Akizibu udzaonetsa kunama kwa mafumu a Israeli.
15 adhuc heredem adducam tibi quae habitas in Maresa usque Adollam veniet gloria Israhel
Ndidzabweretsa mgonjetsi kudzalimbana ndi inu okhala mu Maresa. Ulemerero wa Israeli udzafika ku Adulamu.
16 decalvare et tondere super filios deliciarum tuarum dilata calvitium tuum sicut aquila quoniam captivi ducti sunt ex te
Metani mipala mitu yanu kuonetsa kuti mukulirira ana anu amene mumawakonda; mudzichititse dazi ngati dembo, pakuti anawo adzatengedwa pakati panu kupita ku ukapolo.

< Micha Propheta 1 >