< Micha Propheta 4 >
1 et in novissimo dierum erit mons domus Domini praeparatus in vertice montium et sublimis super colles et fluent ad eum populi
Mʼmasiku otsiriza, phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse. Lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse, ndipo anthu amitundu yonse adzathamangira kumeneko.
2 et properabunt gentes multae et dicent venite ascendamus ad montem Domini et ad domum Dei Iacob et docebit nos de viis suis et ibimus in semitis eius quia de Sion egredietur lex et verbum Domini de Hierusalem
Mayiko ambiri adzabwera ndikunena kuti, “Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.” Malangizo adzachokera ku Ziyoni, mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.
3 et iudicabit inter populos multos et corripiet gentes fortes usque in longinquum et concident gladios suos in vomeres et hastas suas in ligones non sumet gens adversus gentem gladium et non discent ultra belligerare
Iye adzaweruza pakati pa anthu amitundu yambiri ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu amphamvu akutali ndi apafupi omwe. Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera. Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina, kapena kuphunziranso za nkhondo.
4 et sedebit vir subtus vineam suam et subtus ficum suam et non erit qui deterreat quia os Domini exercituum locutum est
Munthu aliyense adzakhala pansi pa tsinde pa mtengo wake wa mpesa ndi pa tsinde pa mtengo wake wamkuyu, ndipo palibe amene adzawachititse mantha, pakuti Yehova Wamphamvuzonse wayankhula.
5 quia omnes populi ambulabunt unusquisque in nomine dei sui nos autem ambulabimus in nomine Domini Dei nostri in aeternum et ultra
Mitundu yonse ya anthu itha kutsatira milungu yawo; ife tidzayenda mʼnjira za Yehova Mulungu wathu mpaka muyaya.
6 in die illa dicit Dominus congregabo claudicantem et eam quam eieceram colligam et quam adflixeram
“Tsiku limenelo, Yehova akuti, “ndidzasonkhanitsa olumala; ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu ochotsedwa ndiponso amene ndinawalanga.
7 et ponam claudicantem in reliquias et eam quae laboraverat in gentem robustam et regnabit Dominus super eos in monte Sion ex hoc nunc et usque in aeternum
Anthu olumalawo ndidzawasandutsa anthu anga otsala. Anthu amene ndinawachotsa ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu. Yehova adzawalamulira mʼPhiri la Yehova kuyambira tsiku limenelo mpaka muyaya.
8 et tu turris Gregis nebulosa filiae Sion usque ad te veniet et veniet potestas prima regnum filiae Hierusalem
Kunena za iwe, nsanja ya ziweto zanga, iwe linga la mwana wamkazi wa Ziyoni, ulamuliro wako wakale udzabwezeretsedwa kwa iwe; ufumu udzabwera pa mwana wamkazi wa Yerusalemu.”
9 nunc quare maerore contraheris numquid rex non est tibi aut consiliarius tuus periit quia conprehendit te dolor sicut parturientem
Chifukwa chiyani tsopano ukulira mofuwula, kodi ulibe mfumu? Kodi phungu wako wawonongedwa, kotero kuti ululu wako uli ngati wa mayi amene akubereka?
10 dole et satage filia Sion quasi parturiens quia nunc egredieris de civitate et habitabis in regione et venies usque ad Babylonem ibi liberaberis ibi redimet te Dominus de manu inimicorum tuorum
Gubuduka ndi ululu, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mayi pa nthawi yake yobereka, pakuti tsopano muyenera kuchoka mu mzinda ndi kugona kunja kwa mzindawo. Udzapita ku Babuloni; kumeneko udzapulumutsidwa, kumeneko Yehova adzakuwombola mʼmanja mwa adani ako.
11 et nunc congregatae sunt super te gentes multae quae dicunt lapidetur et aspiciat in Sion oculus noster
Koma tsopano mitundu yambiri ya anthu yasonkhana kulimbana nawe. Iwo akuti, “Tiyeni timudetse, maso athu aone chiwonongeko cha Ziyoni!”
12 ipsi autem non cognoverunt cogitationes Domini et non intellexerunt consilium eius quia congregavit eos quasi faenum areae
Koma iwo sakudziwa maganizo a Yehova; iwo sakuzindikira cholinga chake, Iye amene amawatuta ngati mitolo ya tirigu ku malo opunthira tirigu.
13 surge et tritura filia Sion quia cornu tuum ponam ferreum et ungulas tuas ponam aereas et comminues populos multos et interficiam Domino rapinas eorum et fortitudinem eorum Domino universae terrae
“Imirira, puntha, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, pakuti ndidzakupatsa nyanga zachitsulo; ndidzakupatsa ziboda zamkuwa ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu.” Phindu lawo lolipeza molakwikalo udzalipereka kwa Yehova, chuma chawo kwa Yehova wa dziko lonse lapansi.