< Leviticus 2 >
1 anima cum obtulerit oblationem sacrificii Domino simila erit eius oblatio fundetque super eam oleum et ponet tus
“‘Munthu wina aliyense akabwera ndi nsembe ya chakudya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala ufa wosalala. Ufawo ausakanize ndi mafuta ndi lubani,
2 ac deferet ad filios Aaron sacerdotes quorum unus tollet pugillum plenum similae et olei ac totum tus et ponet memoriale super altare in odorem suavissimum Domino
ndipo apite nawo kwa ansembe, ana a Aaroni. Atapeko modzazitsa dzanja ufa wosalala uja kuti ukhale wachikumbutso pamodzi ndi mafuta ndi lubani ndipo atenthe zonsezi pa guwa lansembe kuti zilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa chopereka chonse. Iyi ndi nsembe yotentha pa moto ndiponso fungo lokomera Yehova.
3 quod autem reliquum fuerit de sacrificio erit Aaron et filiorum eius sanctum sanctorum de oblationibus Domini
Zotsala za nsembe ya chakudyazo ndi za Aaroni pamodzi ndi ana ake. Chimenechi ndi chigawo chopatulika kwambiri chifukwa chatapidwa pa chopereka chotentha pa moto cha Yehova.
4 cum autem obtuleris sacrificium coctum in clibano de simila panes scilicet absque fermento conspersos oleo et lagana azyma oleo lita
“‘Ukabweretsa nsembe ya chakudya chophika mu uvuni, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta, kapena timitanda ta buledi topyapyala, topanda yisiti koma topaka mafuta.
5 si oblatio tua fuerit de sartagine similae conspersae oleo et absque fermento
Ngati nsembe yako yachakudya ndi yophika pa chitsulo chamoto, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta.
6 divides eam minutatim et fundes supra oleum
Umuduledule bulediyo ndi kumupaka mafuta; imeneyo ndi nsembe yachakudya.
7 sin autem de craticula sacrificium aeque simila oleo conspergetur
Ngati nsembe yako yachakudya ndi yophikidwa pa chiwaya, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta.
8 quam offeres Domino tradens manibus sacerdotis
Munthu azibwera ndi nsembe za chakudya zimene wapanga ndi zinthu zimenezi. Atachipereka kwa wansembe, iyeyu adzipita nacho ku guwa.
9 qui cum obtulerit eam tollet memoriale de sacrificio et adolebit super altare in odorem suavitatis Domino
Wansembeyo atengeko gawo lina la nsembeyo kukhala ufa wachikumbutso kuti ilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa nsembe yonse ndipo ayitenthe pa moto monga nsembe yopsereza ya fungo lokomera Yehova.
10 quicquid autem reliquum est erit Aaron et filiorum eius sanctum sanctorum de oblationibus Domini
Zotsala za nsembe ya chakudyayo zikhale za Aaroni ndi ana ake. Chimenechi ndi chigawo chopatulika kwambiri chifukwa chatapidwa pa chopereka chotentha pa moto cha Yehova.
11 omnis oblatio quae offertur Domino absque fermento fiet nec quicquam fermenti ac mellis adolebitur in sacrificio Domini
“‘Nsembe ya chakudya chilichonse imene ubweretsa kwa Yehova ikhale yopanda yisiti, pakuti suyenera kupereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto imene ili ndi yisiti kapena uchi.
12 primitias tantum eorum offeretis et munera super altare vero non ponentur in odorem suavitatis
Ziwirizi ungathe kubwera nazo kwa Yehova ngati chopereka cha zokolola zoyambirira. Koma usazitenthe pa guwa kuti zikhale fungo lokomera Yehova.
13 quicquid obtuleris sacrificii sale condies nec auferes sal foederis Dei tui de sacrificio tuo in omni oblatione offeres sal
Zopereka zako zonse zachakudya uzithire mchere. Usayiwale kuthira mchere pa chopereka chako popeza mcherewo ukusonyeza pangano pakati pa iwe ndi Mulungu wako. Tsono uzinthira mchere pa chopereka chako chilichonse.
14 sin autem obtuleris munus primarum frugum tuarum Domino de spicis adhuc virentibus torres eas igni et confringes in morem farris et sic offeres primitias tuas Domino
“‘Mukamapereka kwa Yehova chopereka cha chakudya choyamba kucha, choperekacho chikhale cha chipatso chatsopano chokazinga pa moto ndi chopunthapuntha.
15 fundens supra oleum et tus inponens quia oblatio Domini est
Uchithire mafuta ndi lubani pakuti ndi chopereka cha chakudya.
16 de qua adolebit sacerdos in memoriam muneris partem farris fracti et olei ac totum tus
Tsono wansembe atenthe gawo la chopereka chopunthapuntha chija kuti chikhala ufa wachikumbutso ndi cha mafuta pamodzi ndi lubani yense kuti Yehova alandire mʼmalo mwa zopereka zonse. Ichi ndi chopereka chotentha pa moto cha Yehova.