< Jeremiæ 8 >
1 in tempore illo ait Dominus eicient ossa regis Iuda et ossa principum eius et ossa sacerdotum et ossa prophetarum et ossa eorum qui habitaverunt Hierusalem de sepulchris suis
Yehova akuti, “‘Pa nthawi imeneyo, mafupa a mafumu ndi a akuluakulu a ku Yuda, mafupa a ansembe ndi a aneneri, ndiponso mafupa a anthu a ku Yerusalemu adzafukulidwa.
2 et pandent ea ad solem et lunam et omnem militiam caeli quae dilexerunt et quibus servierunt et post quae ambulaverunt et quae quaesierunt et adoraverunt non colligentur et non sepelientur in sterquilinium super faciem terrae erunt
Adzawamwaza pa nthaka kuyangʼana dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zonse zamlengalenga, zimene ankazikonda, kuzitumikira ndi kuzitsatira, kupemphako nzeru ndiponso kuzilambira. Mafupawo sadzawasonkhanitsa kapena kuwakwirira, koma adzakhala ngati ndowe pamwamba pa nthaka.
3 et eligent magis mortem quam vitam omnes qui residui fuerint de cognatione hac pessima in universis locis quae derelicta sunt ad quae eieci eos dicit Dominus exercituum
Otsala onse a mtundu woyipawu adzafuna imfa kopambana moyo kulikonse kumene ndidzawapirikitsirako, akutero Yehova Wamphamvuzonse.’”
4 et dices ad eos haec dicit Dominus numquid qui cadet non resurget et qui aversus est non revertetur
“Tsono awuze anthuwa, ‘Yehova akuti: “‘Kodi anthu akagwa sangadzukenso? Munthu akasochera kodi sangathe kubwereranso?
5 quare ergo aversus est populus iste in Hierusalem aversione contentiosa adprehenderunt mendacium et noluerunt reverti
Chifukwa chiyani nanga anthu awa akupitirirabe kuchimwa, osabwerera? Chifukwa chiyani Yerusalemu akubwerera mʼmbuyo? Iwo akangamira chinyengo; akukana kubwerera.
6 adtendi et auscultavi nemo quod bonum est loquitur nullus est qui agat paenitentiam super peccato suo dicens quid feci omnes conversi sunt ad cursum suum quasi equus impetu vadens in proelio
Ine ndinatchera khutu kumvetsera koma iwo sanayankhulepo zoona. Palibe woyipa amene analapapo zoyipa zake, nʼkumati, ‘Ine ndachita chiyani?’ Aliyense akutsatira njira yake ngati kavalo wothamangira nkhondo.
7 milvus in caelo cognovit tempus suum turtur et hirundo et ciconia custodierunt tempus adventus sui populus autem meus non cognovit iudicium Domini
Mbalame yotchedwa kakowa ija imadziwa nthawi yake mlengalenga. Koma nkhunda, namzeze ndi chingalu zimadziwa nthawi yonyamukira ulendo, koma anthu anga sadziwa malamulo a Yehova.
8 quomodo dicitis sapientes nos sumus et lex Domini nobiscum est vere mendacium operatus est stilus mendax scribarum
“‘Inu mukunena bwanji kuti, ‘Ndife anzeru ndipo timasunga malamulo a Yehova?’ Koma ndi alembi anu amene akulemba zabodza.
9 confusi sunt sapientes perterriti et capti sunt verbum enim Domini proiecerunt et sapientia nulla est in eis
Anthu anzeru achita manyazi; athedwa nzeru ndipo agwidwa. Iwo anakana mawu a Yehova. Nanga tsono nzeru zawo ziwapinduliranji?
10 propterea dabo mulieres eorum exteris agros eorum heredibus quia a minimo usque ad maximum omnes avaritiam sequuntur a propheta usque ad sacerdotem cuncti faciunt mendacium
Nʼchifukwa chake akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena ndipo minda yawo ndidzayipereka kwa amene adzawagonjetse. Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, onse ali ndi khalidwe lofuna kupeza chuma mwakuba. Aneneri pamodzi ndi ansembe omwe, onse amachita zachinyengo.
11 et sanabant contritionem filiae populi mei ad ignominiam dicentes pax pax cum non esset pax
Iwo amapoletsa zilonda za anthu anga pamwamba chabe nʼkumati, ‘Mtendere, mtendere,’ pamene palibe mtendere.
12 confusi sunt quia abominationem fecerunt quinimmo confusione non sunt confusi et erubescere nescierunt idcirco cadent inter corruentes in tempore visitationis suae corruent dicit Dominus
Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazi? Ayi, alibe manyazi ndi pangʼono pomwe; iwo sadziwa nʼkugwetsa nkhope komwe. Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale; adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalanga, akutero Yehova.
13 congregans congregabo eos ait Dominus non est uva in vitibus et non sunt ficus in ficulnea folium defluxit et dedi eis quae praetergressa sunt
“‘Ndidzatenga zokolola zawo, Sipadzakhalanso mphesa pa mpesa kapena nkhuyu pa mkuyu, ndipo masamba ake adzawuma. Zinthu zimene ndinawapatsa ndidzawachotsera.’”
14 quare sedemus convenite et ingrediamur civitatem munitam et sileamus ibi quia Dominus noster silere nos fecit et potum dedit nobis aquam fellis peccavimus enim Domino
Koma amati, “Tikukhala pano chifukwa chiyani? Tiyeni tonse pamodzi tithawire ku mizinda yotetezedwa ndi kukafera kumeneko. Pakuti Yehova Mulungu wathu watsimikiza kuti tiyenera kufa. Watipatsa madzi aululu kuti timwe, chifukwa tamuchimwira.
15 expectavimus pacem et non erat bonum tempus medellae et ecce formido
Tinkayembekezera mtendere koma palibe chabwino chomwe chinachitika, tinkayembekezera kuchira koma tinakumana ndi zoopsa zokhazokha.
16 a Dan auditus est fremitus equorum eius a voce hinnituum pugnatorum eius commota est omnis terra et venerunt et devoraverunt terram et plenitudinem eius urbem et habitatores eius
Kulira kwa ngʼombe zazimuna za mdani kukumveka kuchokera ku Dani; dziko lonse likunjenjemera chifukwa cha kulira kwa akavalowo. Akubwera kudzawononga dziko ndi zonse zimene zili mʼmenemo. Adzawononga mzinda ndi onse okhalamo.”
17 quia ecce ego mittam vobis serpentes regulos quibus non est incantatio et mordebunt vos ait Dominus
Yehova akuti, “Onani, ndikukutumizirani njoka zaululu, mphiri zimene munthu sangathe kuzilodza, ndipo zidzakulumani,”
18 dolor meus super dolorem in me cor meum maerens
Ndadzazidwa ndi chisoni kwambiri, mtima wanga walefukiratu.
19 ecce vox clamoris filiae populi mei de terra longinqua numquid Dominus non est in Sion aut rex eius non est in ea quare ergo me ad iracundiam concitaverunt in sculptilibus suis et in vanitatibus alienis
Imvani kulira kwa anthu anga kuchokera ku dziko lakutali: akuti, “Kodi Yehova sali ku Ziyoni? Kodi mfumu yake sili kumeneko?” “Chifukwa chiyani akundiputa ndi mafano awo osema, ndi milungu yawo yachilendo?”
20 transiit messis finita est aestas et nos salvati non sumus
“Nthawi yokolola yapita, chilimwe chapita, koma sitinapulumuke.”
21 super contritionem filiae populi mei contritus sum et contristatus stupor obtinuit me
Chifukwa cha mavuto a anthu anga, ine ndikumva kuwawa; ndikungolira ndipo mantha aakulu andigwira.
22 numquid resina non est in Galaad aut medicus non est ibi quare igitur non est obducta cicatrix filiae populi mei
Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa? Kodi kumeneko kulibe singʼanga? Nanga chifukwa chiyani mabala a anthu anga sanapole?