< Jeremiæ 18 >

1 verbum quod factum est ad Hieremiam a Domino dicens
Yehova anawuza Yeremiya kuti,
2 surge et descende in domum figuli et ibi audies verba mea
“Pita ku nyumba ya munthu wowumba mbiya, ndipo kumeneko ndikakuwuza mawu anga.”
3 et descendi in domum figuli et ecce ipse faciebat opus super rotam
Choncho ndinatsikira ku nyumba ya wowumba mbiya, ndipo ndinamuona akuwumba mbiya pa mkombero.
4 et dissipatum est vas quod ipse faciebat e luto manibus suis conversusque fecit illud vas alterum sicut placuerat in oculis eius ut faceret
Tsono amati ngati mbiya imene waumba ikhala yosawumbika bwino ankayiphwanya nʼkuwumbanso ina monga mmene afunira ndi dothi lake lomwe lija.
5 et factum est verbum Domini ad me dicens
Kenaka Yehova anandiwuza kuti,
6 numquid sicut figulus iste non potero facere vobis domus Israhel ait Dominus ecce sicut lutum in manu figuli sic vos in manu mea domus Israhel
“Inu Aisraeli, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira wowumba mbiya?” akutero Yehova. “Inu muli mʼmanja mwanga ngati mtapo mʼmanja mwa wowumba mbiya.
7 repente loquar adversum gentem et adversum regnum ut eradicem et destruam et disperdam illud
Ngati nditalengeza kuti mtundu wina wa anthu kapena ufumu wina ndiwuzula, kuwugwetsa ndi kuwuwononga,
8 si paenitentiam egerit gens illa a malo suo quod locutus sum adversum eam agam et ego paenitentiam super malo quod cogitavi ut facerem ei
ndipo ngati mtundu wa anthu umene ndawuchenjezawo ulapa zoyipa zawo, ndiye kuti Ine ndidzaleka ndipo sindidzabweretsa pa anthuwo mavuto amene ndinakonzekera kuwachitira.
9 et subito loquar de gente et regno ut aedificem et ut plantem illud
Ndipo ngati ndilengeza kuti ndikufuna kumanga ndi kukhazikitsa mtundu wa anthu kapena ufumu.
10 si fecerit malum in oculis meis ut non audiat vocem meam paenitentiam agam super bono quod locutus sum ut facerem ei
Koma mtunduwo ukachita choyipa pamaso panga nʼkusandimvera, ndiye kuti sindidzawuchitiranso zabwino zimene ndimafuna ndiwuchitire.
11 nunc ergo dic viro Iudae et habitatoribus Hierusalem dicens haec dicit Dominus ecce ego fingo contra vos malum et cogito contra vos cogitationem revertatur unusquisque a via sua mala et dirigite vias vestras et studia vestra
“Ndipo tsopano kawawuze anthu a ku Yuda ndi amene akukhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova akuti, Taonani! Ndikukukonzerani mavuto, ndi kuganizira zoti ndikulangeni. Kotero siyani makhalidwe anu oyipa aliyense wa inu, ndipo mukonzenso makhalidwe anu ndi zochita zanu.’
12 qui dixerunt desperavimus post cogitationes enim nostras ibimus et unusquisque pravitatem cordis sui mali faciemus
Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nʼzosathandiza. Ife tidzapitiriza kuchita zomwe takonzekera; aliyense wa ife adzatsatira zoyipa za mtima wake wokanika.’”
13 ideo haec dicit Dominus interrogate gentes quis audivit talia horribilia quae fecit nimis virgo Israhel
Yehova akuti, “Uwafunse anthu a mitundu ina kuti: Kodi ndani anamvapo zinthu zofanana ndi zimenezi? Israeli amene anali ngati namwali wanga wachita chinthu choopsa kwambiri.
14 numquid deficiet de petra agri nix Libani aut evelli possunt aquae erumpentes frigidae et defluentes
Kodi chisanu chimatha pa matanthwe otsetsereka a phiri la Lebanoni? Kodi madzi ozizira amitsinje ochokera ku phiri la Lebanoni adzamphwa?
15 quia oblitus est mei populus meus frustra libantes et inpingentes in viis suis in semitis saeculi ut ambularent per eas in itinere non trito
Komatu anthu anga andiyiwala; akufukiza lubani kwa mafano achabechabe. Amapunthwa mʼnjira zawo zakale. Amayenda mʼnjira zachidule ndi kusiya njira zabwino.
16 ut fieret terra eorum in desolationem et in sibilum sempiternum omnis qui praeterit per eam obstupescet et movebit caput suum
Dziko lawo amalisandutsa chipululu, chinthu chochititsa manyazi nthawi zonse; onse odutsapo adzadabwa kwambiri ndipo adzapukusa mitu yawo.
17 sicut ventus urens dispergam eos coram inimico dorsum et non faciem ostendam eis in die perditionis eorum
Ngati mphepo yochokera kummawa, ndidzawabalalitsa pamaso pa adani awo; ndidzawafulatira osawathandiza pa tsiku la mavuto awo.”
18 et dixerunt venite et cogitemus contra Hieremiam cogitationes non enim peribit lex a sacerdote neque consilium a sapiente nec sermo a propheta venite et percutiamus eum lingua et non adtendamus ad universos sermones eius
Anthuwo anati, “Tiyeni, tipangane zoti timuchitire Yeremiya; pakuti ansembe otiphunzitsa malamulo tidzakhala nawobe. Anthu anzeru otilangiza tidzakhala nawo, ndiponso aneneri otilalikira mawu. Choncho tiyeni timupezere chifukwa ndipo tisamvere chilichonse chimene akunena.”
19 adtende Domine ad me et audi vocem adversariorum meorum
Ndipo ndinapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, ndimvereni; imvani zimene adani anga akunena za ine!
20 numquid redditur pro bono malum quia foderunt foveam animae meae recordare quod steterim in conspectu tuo ut loquerer pro eis bonum et averterem indignationem tuam ab eis
Kodi chinthu choyipa nʼkukhala dipo la chinthu chabwino? Komabe iwo andikumbira dzenje. Kumbukirani kuti ndinadzayima pamaso panu kudzawapempherera kuti muwachotsere mkwiyo wanu.
21 propterea da filios eorum in famem et deduc eos in manus gladii fiant uxores eorum absque liberis et viduae et viri earum interficiantur morte iuvenes eorum confodiantur gladio in proelio
Choncho langani ana awo ndi njala; aperekeni kuti aphedwe ndi lupanga. Akazi awo asanduke opanda ana ndi amasiye; amuna awo aphedwe ndi mliri, anyamata awo aphedwe ndi lupanga ku nkhondo.
22 audiatur clamor de domibus eorum adduces enim super eos latronem repente quia foderunt foveam ut caperent me et laqueos absconderunt pedibus meis
Kulira kumveke kuchokera mʼnyumba zawo mutawatumizira gulu lankhondo mwadzidzidzi kuti liwakanthe. Iwo andikumbira dzenje kuti ndigweremo ndipo atchera msampha mapazi anga.
23 tu autem Domine scis omne consilium eorum adversum me in mortem ne propitieris iniquitati eorum et peccatum eorum a facie tua non deleatur fiant corruentes in conspectu tuo in tempore furoris tui abutere eis
Koma Inu Yehova, mukudziwa ziwembu zawo zonse zofuna kundipha. Musawakhululukire zolakwa zawo kapena kufafaniza machimo awo pamaso panu. Agonjetsedwe pamaso panu; muwalange muli wokwiya.”

< Jeremiæ 18 >