< Isaiæ 47 >

1 descende sede in pulverem virgo filia Babylon sede in terra non est solium filiae Chaldeorum quia ultra non vocaberis mollis et tenera
“Tsika, ndi kukhala pa fumbi, iwe namwali, Babuloni; khala pansi wopanda mpando waufumu, iwe namwali, Kaldeya pakuti sadzakutchulanso wanthete kapena woyenera kumugwira mosamala.
2 tolle molam et mole farinam denuda turpitudinem tuam discoperi umerum revela crus transi flumina
Tenga mphero ndipo upere ufa; chotsa nsalu yako yophimba nkhope kwinya chovala chako mpaka ntchafu ndipo woloka mitsinje.
3 revelabitur ignominia tua et videbitur obprobrium tuum ultionem capiam et non resistet mihi homo
Maliseche ako adzakhala poyera ndipo udzachita manyazi. Ndidzabwezera chilango ndipo palibe amene adzandiletse.”
4 redemptor noster Dominus exercituum nomen illius Sanctus Israhel
Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wathu, dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
5 sede tace et intra in tenebras filia Chaldeorum quia non vocaberis ultra domina regnorum
“Khala chete, ndipo lowa mu mdima, iwe namwali, Kaldeya; chifukwa sadzakutchulanso mfumukazi ya maufumu.
6 iratus sum super populum meum contaminavi hereditatem meam et dedi eos in manu tua non posuisti eis misericordias super senem adgravasti iugum tuum valde
Ndinawakwiyira anthu anga, osawasamalanso. Ndinawapereka manja mwako, ndipo iwe sunawachitire chifundo. Iwe unachitira nkhanza ngakhale nkhalamba.
7 et dixisti in sempiternum ero domina non posuisti haec super cor tuum neque recordata es novissimi tui
Iwe unati, ‘Ine ndidzakhalapo nthawi zonse ngati mfumukazi.’ Koma sunaganizire zinthu izi kapena kusinkhasinkha za mmene ziti zidzathere.
8 et nunc audi haec delicata et habitans confidenter quae dicis in corde tuo ego sum et non est praeter me amplius non sedebo vidua et ignorabo sterilitatem
“Ndipo tsopano, tamvera, iwe wongokonda zokondweretsawe, amene ukukhala mosatekesekawe, umaganiza mu mtima mwako kuti, ‘Ine ndi Ine, ndipo kupatula ine palibenso wina. Sindidzakhala konse mkazi wamasiye, ndipo ana anga sadzamwalira.’
9 venient tibi duo haec subito in die una sterilitas et viduitas universa venerunt super te propter multitudinem maleficiorum tuorum et propter duritiam incantatorum tuorum vehementem
Koma mʼkamphindi, ndiponso tsiku limodzi, zinthu ziwiri izi zidzakuchitikira: ana ako kukufera komanso kukhala mkazi wamasiye. Zimenezi zidzakuchitikira kwathunthu ngakhale ali ndi amatsenga ambiri ndi mawula amphamvu.
10 et fiduciam habuisti in malitia tua et dixisti non est qui videat me sapientia tua et scientia tua haec decepit te et dixisti in corde tuo ego sum et praeter me non est altera
Iwe unkadalira kuyipa kwako ndipo unati, ‘Palibe amene akundiona.’ Kuchenjera ndi nzeru zako zidzakusokoneza, choncho ukuganiza mu mtima mwako kuti, ‘Ine ndine basi, ndipo kupatula ine palibenso wina.’
11 veniet super te malum et nescies ortum eius et inruet super te calamitas quam non poteris expiare veniet super te repente miseria quam nescies
Ngozi yayikulu idzakugwera ndipo sudzadziwa momwe ungayipewere ndi matsenga ako. Mavuto adzakugwera ndipo sudzatha kuwachotsa; chipasupasu chimene iwe sukuchidziwa chidzakugwera mwadzidzidzi.
12 sta cum incantatoribus tuis et cum multitudine maleficiorum tuorum in quibus laborasti ab adulescentia tua si forte quid prosit tibi aut si possis fieri fortior
“Pitiriza tsono kukhala ndi matsenga ako, pamodzi ndi nyanga zako zochulukazo, wakhala ukuzigwiritsa ntchito kuyambira ubwana wako. Mwina udzatha kupambana kapena kuopsezera nazo adani ako.
13 defecisti in multitudine consiliorum tuorum stent et salvent te augures caeli qui contemplabantur sidera et supputabant menses ut ex eis adnuntiarent ventura tibi
Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi! Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni. Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezi zimene ziti zidzakuchitikire.
14 ecce facti sunt quasi stipula ignis conbusit eos non liberabunt animam suam de manu flammae non sunt prunae quibus calefiant nec focus ut sedeant ad eum
Ndithudi, anthuwo ali ngati phesi; adzapsa ndi moto. Sangathe kudzipulumutsa okha ku mphamvu ya malawi a moto. Awa si makala a moto woti wina nʼkuwotha; kapena moto woti wina nʼkuwukhalira pafupi.
15 sic facta sunt tibi in quibuscumque laboraveras negotiatores tui ab adulescentia tua unusquisque in via sua erraverunt non est qui salvet te
Umu ndi mmene adzachitire amatsenga, anthu amene wakhala ukugwira nawo ntchito ndi kuchita nawo malonda chiyambire cha ubwana wako. Onse adzamwazika ndi mantha, sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”

< Isaiæ 47 >