< Isaiæ 44 >
1 et nunc audi Iacob serve meus et Israhel quem elegi
Yehova akuti, “Mvera tsopano, iwe Yakobo, mtumiki wanga, Israeli, amene ndinakusankha.
2 haec dicit Dominus faciens et formans te ab utero auxiliator tuus noli timere serve meus Iacob et Rectissime quem elegi
Yehova amene anakupanga iwe, anakuwumba iwe mʼmimba ya amayi ako, ndi amene adzakuthandiza iwe. Iye akuti, Usachite mantha, iwe Yakobo, mtumiki wanga, Yesuruni, amene ndinakusankha.
3 effundam enim aquas super sitientem et fluenta super aridam effundam spiritum meum super semen tuum et benedictionem meam super stirpem tuam
Pakuti ndidzathira madzi pa nthaka yowuma, ndi kuyendetsa mitsinje mʼdziko lowuma; ndidzatumiza Mzimu wanga pa ana anu, ndi kutsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.
4 et germinabunt inter herbas quasi salices iuxta praeterfluentes aquas
Iwo adzakula ngati udzu wothirira bwino ndi ngati bango lomera mʼmbali mwa mitsinje ya madzi oyenda.
5 iste dicet Domini ego sum et ille vocabit in nomine Iacob et hic scribet manu sua Domino et in nomine Israhel adsimilabitur
Wina adzanena kuti, ‘Ine ndine wa Yehova;’ wina adzadzitcha yekha wa banja la Yakobo; winanso adzalemba pa dzanja lake, ‘Wa Yehova’ ndipo adzadzitcha wa banja la Israeli.
6 haec dicit Dominus rex Israhel et redemptor eius Dominus exercituum ego primus et ego novissimus et absque me non est deus
“Yehova Mfumu ndi Mpulumutsi wa Israeli, Yehova Wamphamvuzonse akuti: Ine ndine woyamba ndi wotsiriza; palibenso Mulungu wina koma Ine ndekha.
7 quis similis mei vocet et adnuntiet et ordinem exponat mihi ex quo constitui populum antiquum ventura et quae futura sunt adnuntient eis
Ndani nanga angafanane ndi Ine? Muloleni kuti ayankhule. Muloleni andifotokozere ndi kundiyalira bwino lomwe zimene zinachitika kuyambira pamene ndinkakhazikitsa anthu anga akalekale, ndi ziti zimene zidzachitike; inde, muloleni alosere zimene zikubwera.
8 nolite timere neque conturbemini ex tunc audire te feci et adnuntiavi vos estis testes mei numquid est deus absque me et formator quem ego non noverim
Musanjenjemere, musachite mantha. Kodi sindinakuwuzeni zimenezi ndi kuzilosera kalekale lomwe? Inu ndinu mboni zanga. Kodi aliponso Mulungu wina kupatula Ine? Ayi, palibe Thanthwe linanso limene sindikulidziwa.”
9 plastae idoli omnes nihil sunt et amantissima eorum non proderunt eis ipsi sunt testes eorum quia non vident neque intellegunt ut confundantur
Onse amene amapanga mafano ngachabe, ndipo milungu imene amayilemekeza ndi yopanda phindu. Iwo amene amapembedza mafano ndi wosaona; ndipo sazindikira kanthu. Choncho adzawachititsa manyazi.
10 quis formavit deum et sculptile conflavit ad nihil utile
Ndani amasema mulungu ndi kuwumba fano, limene silingamupindulire?
11 ecce omnes participes eius confundentur fabri enim sunt ex hominibus convenient omnes stabunt et pavebunt et confundentur simul
Iye pamodzi ndi anzake onse adzawachititsa manyazi; amisiri a mafano ndi anthu chabe. Aloleni onse asonkhane ndi kuyima pabwalo la milandu; onse adzaopsedwa ndipo adzachita manyazi.
12 faber ferrarius lima operatus est in prunis et in malleis formavit illud et operatus est in brachio fortitudinis suae esuriet et deficiet non bibet aquam et lassescet
Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulo ndipo amachiyika pa makala amoto; ndi dzanja lake lamphamvu amachisula pochimenya ndi nyundo. Pambuyo pake mʼmisiri uja amamva njala natha mphamvu; iye samwa madzi, ndipo amalefuka.
13 artifex lignarius extendit normam formavit illud in runcina fecit illud in angularibus et in circino tornavit illud et fecit imaginem viri quasi speciosum hominem habitantem in domo
Mmisiri wa matabwa nayenso amayeza mtengo ndi chingwe ndipo amajambula chithunzi ndi cholembera; amasema bwinobwino ndi chipangizo chake ndipo amachiwongola bwino ndi chida chake. Amachipanga ngati munthu, munthu wake wokongola kuti aliyike mʼnyumba yake yachipembedzo.
14 succidit cedros tulit ilicem et quercum quae steterat inter ligna saltus plantavit pinum quam pluvia nutrivit
Amagwetsa mitengo ya mkungudza, mwinanso amatenga mtengo wa payini kapena wa thundu nʼkudzisankhira mtengo wabwino pakati pa mitengo ya mʼnkhalango, ndipo amadzala mtengo wa payini ndi kuwuleka kuti ukule ndi mvula.
15 et facta est hominibus in focum sumpsit ex eis et calefactus est et succendit et coxit panes de reliquo autem operatus est deum et adoravit fecit sculptile et curvatus est ante illud
Mitengoyo munthu amachitako nkhuni; nthambi zina amasonkhera moto wowotha, amakolezera moto wophikira buledi ndi mbali ina ya mtengowo amapangira mulungu ndipo amapembedza; iye amapanga fano ndi kumaligwadira.
16 medium eius conbusit igni et de medio eius carnes comedit coxit pulmentum et saturatus est et calefactus est et dixit va calefactus sum vidi focum
Chigawo china cha mtengowo amasonkhera moto wowotcherapo nyama imene amadya, nakhuta. Iye amawotha motowo ndipo amanena kuti, “Aa! Ndikumva kutentha; pano pali moto.”
17 reliquum autem eius deum fecit sculptile sibi curvatur ante illud et adorat illud et obsecrat dicens libera me quia deus meus es tu
Chigawo chotsala amapanga kamulungu, fano lake limenelo; amaligwadira ndi kulipembedza. Amapemphera kwa fanolo ndipo amanena kuti, “Iwe ndiwe mulungu wanga, ndipulumutse.”
18 nescierunt neque intellexerunt lutati enim sunt ne videant oculi eorum et ne intellegant corde suo
Anthu otere sadziwa kanthu, samvetsa kanthu kalikonse; maso awo ndi omatirira ndipo sangathe kuona, ndipo mitu yawo ndi yogontha kotero sangathe kumvetsa.
19 non recogitant in mente sua neque cognoscunt neque sentiunt ut dicant medietatem eius conbusi igne et coxi super carbones eius panes coxi carnes et comedi et de reliquo eius idolum faciam ante truncum ligni procidam
Palibe amene amayima nʼkulingalira. Palibe wanzeru kapena womvetsa zinthu bwino woti nʼkunena kuti, chigawo china cha mtengowo ndinasonkhera moto; pa makala ake ndinaphikira buledi, ndinawotchapo nyama ndipo ndinadya. Chigawo chotsalachi ndipangire chinthu chonyansachi. Kodi ndidzagwadira mtengo?
20 pars eius cinis est cor insipiens adoravit illud et non liberabit animam suam neque dicet forte mendacium est in dextera mea
Munthu wotere ali ngati wodya phulusa, maganizo ake opusa amusocheretsa; motero kuti sangathe kudzipulumutsa yekha kapena kudzifunsa kuti, “Kodi chinthu chili mʼmanja mwangachi si chabodza?”
21 memento horum Iacob et Israhel quoniam servus meus es tu formavi te servus meus es tu Israhel non oblivisceris mei
Yehova akuti, “Iwe Yakobo, kumbukira zinthu izi popeza kuti ndiwe mtumiki wanga, iwe Israeli. Ine ndinakupanga iwe, ndiwe mtumiki wanga; iwe Israeli, sindidzakuyiwala.
22 delevi ut nubem iniquitates tuas et quasi nebulam peccata tua revertere ad me quoniam redemi te
Ndachotsa zolakwa zako ngati mitambo, ndi machimo ako ngati nkhungu ya mmawa. Bwerera kwa Ine, popeza ndakupulumutsa.”
23 laudate caeli quoniam fecit Dominus iubilate extrema terrae resonate montes laudationem saltus et omne lignum eius quoniam redemit Dominus Iacob et Israhel gloriabitur
Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga, pakuti Yehova wachita zimenezi; fuwula, iwe dziko lapansi. Imbani nyimbo, inu mapiri, inu nkhalango ndi mitengo yonse, chifukwa Yehova wawombola Yakobo, waonetsa ulemerero wake mwa Israeli.
24 haec dicit Dominus redemptor tuus et formator tuus ex utero ego sum Dominus faciens omnia extendens caelos solus stabiliens terram et nullus mecum
Yehova Mpulumutsi wanu, amene anakuwumbani mʼmimba ya amayi anu akuti: “Ine ndine Yehova, amene anapanga zinthu zonse, ndinatambasula ndekha zinthu zakuthambo, ndinayala ndekha dziko lapansi.
25 irrita faciens signa divinorum et ariolos in furorem vertens convertens sapientes retrorsum et scientiam eorum stultam faciens
Ndine amene ndinalepheretsa mipingo ya anthu onyenga, ndipo ndimapusitsa owombeza mawula. Ndimasokoneza anthu a nzeru, ndi kuonetsa kuti nzeru zawo nʼzopusa.
26 suscitans verbum servi sui et consilium nuntiorum suorum conplens qui dico Hierusalem habitaberis et civitatibus Iuda aedificabimini et deserta eius suscitabo
Ndine amene ndimatsimikiza mawu a atumiki ake ndi kukwaniritsa zimene analosera amithenga ake. “Ndine amene ndinanena za Yerusalemu kuti mudzakhalanso anthu. Ndinanenanso za mizinda ya Yuda kuti idzamangidwanso. Za mabwinja awo ndinanena kuti ndidzawawutsanso.
27 qui dico profundo desolare et flumina tua arefaciam
Ndine amene ndinawuza nyanga yayikulu kuti, ‘Uma’ ndipo ndidzawumitsa mitsinje yako.
28 qui dico Cyro pastor meus es et omnem voluntatem meam conplebis qui dico Hierusalem aedificaberis et templo fundaberis
Ndine amene ndinanena kwa Koresi kuti, ‘Iye ndiye mʼbusa wanga,’ ndipo adzachita zonse zimene ndikufuna; iye adzalamula kuti, ‘Yerusalemu amangidwenso’ ndi kuti, ‘Maziko a Nyumba ya Mulungu ayikidwenso.’”