< Isaiæ 37 >
1 et factum est cum audisset rex Ezechias scidit vestimenta sua et obvolutus est sacco et intravit in domum Domini
Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova.
2 et misit Eliachim qui erat super domum et Sobnam scribam et seniores de sacerdotibus opertos saccis ad Isaiam filium Amos prophetam
Iye anatuma Eliyakimu woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo, ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi.
3 et dixerunt ad eum haec dicit Ezechias dies tribulationis et correptionis et blasphemiae dies haec quia venerunt filii usque ad partum et virtus non est parienti
Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera.’
4 si quo modo audiat Dominus Deus tuus verba Rabsaces quem misit rex Assyriorum dominus suus ad blasphemandum Deum viventem et obprobrandum sermonibus quos audivit Dominus Deus tuus leva ergo orationem pro reliquiis quae reppertae sunt
Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a kazembe amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.”
5 et venerunt servi regis Ezechiae ad Isaiam
Akuluakulu a mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya,
6 et dixit ad eos Isaias haec dicetis domino vestro haec dicit Dominus ne timeas a facie verborum quae audisti quibus blasphemaverunt pueri regis Assyriorum me
Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine.
7 ecce ego dabo ei spiritum et audiet nuntium et revertetur ad terram suam et corruere eum faciam gladio in terra sua
Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake, ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’”
8 reversus est autem Rabsaces et invenit regem Assyriorum proeliantem adversus Lobna audierat enim quia profectus esset de Lachis
Kazembe wa ankhondo uja atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.
9 et audivit de Tharaca rege Aethiopiae dicentes egressus est ut pugnet contra te quod cum audisset misit nuntios ad Ezechiam dicens
Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi akubwera kudzachita naye nkhondo. Atamva zimenezi, anatumiza amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa:
10 haec dicetis Ezechiae regi Iudae loquentes non te decipiat Deus tuus in quo tu confidis dicens non dabitur Hierusalem in manu regis Assyriorum
“Kawuzeni Hezekiya mfumu ya ku Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’
11 ecce tu audisti omnia quae fecerunt reges Assyriorum omnibus terris quas subverterunt et tu poteris liberari
Ndithudi iwe unamva zimene mafumu a ku Asiriya akhala akuchitira mayiko onse. Iwo anawawononga kotheratu. Tsono iwe ndiye ndi kupulumuka?
12 numquid eruerunt eos dii gentium quos subverterunt patres mei Gozan et Aran et Reseph et filios Eden qui erant in Thalassar
Makolo anga anawononga mizinda ya Gozani, Harani, Rezefi ndi anthu a ku Edeni amene ankakhala ku Telasara. Kodi milungu inayi ija anawapulumutsa anthu a mizindayi?
13 ubi est rex Emath et rex Arfad et rex urbis Seffarvaim Anahe et Ava
Kodi mafumu a ku Hamati, Aripadi, Safaravaimu, Hena ndi Iva ali kuti?”
14 et tulit Ezechias libros de manu nuntiorum et legit eos et ascendit in domum Domini et expandit eos Ezechias coram Domino
Hezekiya analandira kalata kwa amithenga nayiwerenga pomwepo. Hezekiya anapita ku Nyumba ya Yehova ndipo anayika kalatayo pamaso pa Yehova.
15 et oravit Ezechias ad Dominum dicens
Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova:
16 Domine exercituum Deus Israhel qui sedes super cherubin tu es Deus solus omnium regnorum terrae tu fecisti caelum et terram
“Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pakati pa akerubi, Inu nokha ndiye Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
17 inclina Domine aurem tuam et audi aperi Domine oculos tuos et vide et audi omnia verba Sennacherib quae misit ad blasphemandum Deum viventem
Inu Yehova tcherani khutu ndipo mumve. Inu Yehova, tsekulani maso anu ndipo muone. Imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza, kunyoza Mulungu wamoyo.
18 vere enim Domine desertas fecerunt reges Assyriorum terras et regiones earum
“Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu yonse ya anthu ndi mayiko awo.
19 et dederunt deos earum igni non enim erant dii sed opera manuum hominum lignum et lapis et comminuerunt eos
Iwo anaponyera pa moto milungu yawo ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mafano a mitengo ndi miyala, yopangidwa ndi manja a anthu.
20 et nunc Domine Deus noster salva nos de manu eius et cognoscant omnia regna terrae quia tu es Dominus solus
Tsono Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni mʼdzanja lake kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndiye Mulungu.”
21 et misit Isaias filius Amos ad Ezechiam dicens haec dicit Dominus Deus Israhel pro quibus rogasti me de Sennacherib rege Assyriorum
Tsono Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga wochokera kwa Yehova kwa Hezekiya poyankha pemphero lake lokhudza Senakeribu mfumu ya ku Asiriya.
22 hoc est verbum quod locutus est Dominus super eum despexit te subsannavit te virgo filia Sion post te caput movit filia Hierusalem
Mawu amene Yehova wayankhula motsutsana naye ndi awa: “Mwana wamkazi wa Ziyoni akukunyoza ndi kukuseka. Mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusa mutu wake pamene iwe ukuthawa.
23 cui exprobrasti et quem blasphemasti et super quem exaltasti vocem et levasti altitudinem oculorum tuorum ad Sanctum Israhel
Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira ndani? Kodi iwe wafuwulira ndi kumuyangʼana monyada ndani? Watsutsana ndi Woyerayo wa Israeli!
24 in manu servorum tuorum exprobrasti Domino et dixisti in multitudine quadrigarum mearum ego ascendi altitudinem montium iuga Libani et succidam excelsa cedrorum eius electas abietes illius et introibo altitudinem summitatis eius saltum Carmeli eius
Kudzera mwa amithenga ako iwe wanyoza Ambuye. Ndipo wanena kuti, ‘Ndi magaleta anga ochuluka ndafika pamwamba pa mapiri, pamwamba penipeni pa mapiri a Lebanoni. Ndagwetsa mitengo yamkungudza yayitali kwambiri, ndi mitengo yabwino kwambiri ya payini. Ndafika pa msonga pake penipeni, nkhalango yake yowirira kwambiri.
25 ego fodi et bibi aquam et exsiccavi vestigio pedis mei omnes rivos aggerum
Ndakumba zitsime ku mayiko achilendo ndi kumva madzi akumeneko ndi mapazi anga ndawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’
26 numquid non audisti quae olim fecerim ei ex diebus antiquis ego plasmavi illud et nunc adduxi et factum est in eradicationem collium conpugnantium et civitatum munitarum
“Kodi sunamvepo kuti zimenezi ndinazikonzeratu kalekale? Ndinazikonzeratu masiku amakedzana; tsopano ndazichitadi, kuti iwe kwako nʼkusandutsa mizinda yotetezedwa kukhala milu ya miyala.
27 habitatores earum breviata manu contremuerunt et confusi sunt facti sunt sicut faenum agri et gramen pascuae et herba tectorum quae exaruit antequam maturesceret
Anthu amene ankakhala kumeneko analibenso mphamvu, ankada nkhawa ndi kuchititsidwa manyazi. Anali ngati mbewu za mʼmunda, ngati udzu wanthete, ali ngati udzu omera pa denga, umene mphepo imawumitsa usanakule nʼkomwe.
28 habitationem tuam et egressum tuum et introitum tuum cognovi et insaniam tuam contra me
“Koma Ine ndimadziwa zonse za iwe; ndimadziwa pamene ukuyima ndi pamene ukukhala; ndimadziwa pamene ukutuluka ndi pamene ukulowa, ndiponso momwe umandikwiyira Ine.
29 cum fureres adversum me superbia tua ascendit in aures meas ponam ergo circulum in naribus tuis et frenum in labiis tuis et reducam te in viam per quam venisti
Chifukwa umandikwiyira Ine ndi kuti mwano wako wamveka mʼmakutu anga, ndidzakola mphuno yako ndi mbedza ndikuyika chitsulo mʼkamwa mwako, ndipo ndidzakubweza pokuyendetsa njira yomwe unadzera pobwera.
30 tibi autem hoc erit signum comede hoc anno quae sponte nascuntur et in anno secundo pomis vescere in anno autem tertio seminate et metite et plantate vineas et comedite fructum earum
“Iwe Hezekiya, chizindikiro chako cha zimene zidzachitike ndi ichi: “Chaka chino mudzadya zimene zamera zokha, ndipo chaka chachiwiri zimene zaphukira pa zomera zokha, koma chaka chachitatu mudzafesa ndi kukolola, mudzawoka mitengo yamphesa ndi kudya zipatso zake.
31 et mittet id quod salvatum fuerit de domo Iuda et quod reliquum est radicem deorsum et faciet fructum sursum
Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsalire adzazika mizu yawo pansi ndipo adzabereka zipatso poyera.
32 quia de Hierusalem exibunt reliquiae et salvatio de monte Sion zelus Domini exercituum faciet istud
Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala, ndi ku phiri la Ziyoni gulu la anthu opulumuka. Changu cha Yehova Wamphamvuzonse chidzachita zimenezi.
33 propterea haec dicit Dominus de rege Assyriorum non introibit civitatem hanc et non iaciet ibi sagittam et non occupabit eam clypeus et non mittet in circuitu eius aggerem
“Choncho Yehova akunena izi za mfumu ya ku Asiriya: “Iye sadzalowa mu mzinda umenewu kapena kuponyamo muvi uliwonse. Sadzafika pafupi ndi mzindawu ndi ankhondo ake a zishango kapena kuwuzinga ndi mitumbira yankhondo.
34 in via qua venit per eam revertetur et civitatem hanc non ingredietur dicit Dominus
Adzabwerera potsata njira yomwe anadzera pobwera; sadzalowa mu mzinda umenewu,” akutero Yehova.
35 et protegam civitatem istam ut salvem eam propter me et propter David servum meum
“Ine ndidzawuteteza ndi kuwupulumutsa mzindawu, chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha pangano ndi mtumiki wanga Davide!”
36 egressus est autem angelus Domini et percussit in castris Assyriorum centum octoginta quinque milia et surrexerunt mane et ecce omnes cadavera mortuorum
Tsopano mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya nkhondo ya ku Asiriya ndikukapha asilikali 185,000. Podzuka mmawa mwake anthu anangoona mitembo ponseponse!
37 et egressus est et abiit et reversus est Sennacherib rex Assyriorum et habitavit in Nineve
Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anasasula misasa nʼkuchoka kubwerera kukakhala ku Ninive.
38 et factum est cum adoraret in templo Nesrach deum suum Adramelech et Sarasar filii eius percusserunt eum gladio fugeruntque in terram Ararat et regnavit Asoraddon filius eius pro eo
Tsiku lina, pamene ankapembedza mʼnyumba ya mulungu wake, Nisiroki, ana ake awiri, Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga, ndipo anathawira mʼdziko la Ararati. Ndipo mwana wake Esrahadoni analowa ufumu mʼmalo mwake.