< Genesis 26 >
1 orta autem fame super terram post eam sterilitatem quae acciderat in diebus Abraham abiit Isaac ad Abimelech regem Palestinorum in Gerara
Tsono kunagwa njala ina mʼdzikomo kuwonjezera pa ija ya poyamba ya nthawi ya Abrahamu ndipo Isake anapita kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari.
2 apparuitque ei Dominus et ait ne descendas in Aegyptum sed quiesce in terra quam dixero tibi
Yehova anadza kwa Isake nati, “Usapite ku Igupto; koma ukhale mʼdziko limene ndidzakuwuza kuti ukakhalemo.
3 et peregrinare in ea eroque tecum et benedicam tibi tibi enim et semini tuo dabo universas regiones has conplens iuramentum quod spopondi Abraham patri tuo
Khala mʼdziko lino ndipo ndidzakhala nawe ndi kukudalitsa. Pakuti kwa iwe ndi zidzukulu zako ndidzapereka mayiko onsewa. Choncho ndidzakwaniritsa pangano limene ndinalumbira kwa Abrahamu, abambo ako.
4 et multiplicabo semen tuum sicut stellas caeli daboque posteris tuis universas regiones has et benedicentur in semine tuo omnes gentes terrae
Zidzukulu zako ndidzazichulukitsa ngati nyenyezi za mu mlengalenga ndi kuzipatsa mayiko onsewa. Ndiponso anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako,
5 eo quod oboedierit Abraham voci meae et custodierit praecepta et mandata mea et caerimonias legesque servaverit
chifukwa Abrahamu anandimvera, nasunga malamulo anga onse.”
6 mansit itaque Isaac in Geraris
Choncho Isake anakhala ku Gerari.
7 qui cum interrogaretur a viris loci illius super uxore sua respondit soror mea est timuerat enim confiteri quod sibi esset sociata coniugio reputans ne forte interficerent eum propter illius pulchritudinem
Anthu akumaloko atafunsa Isake za mkazi wake, iye anati, “Ndi mlongo wanga ameneyu.” Iye anaopa kunena kuti, “Ndi mkazi wanga ameneyu,” popeza ankaganiza kuti anthu akumeneku akhoza kumupha ndi kukwatira mkazi wake popeza Rebeka anali wokongola.
8 cumque pertransissent dies plurimi et ibi demoraretur prospiciens Abimelech Palestinorum rex per fenestram vidit eum iocantem cum Rebecca uxore sua
Isake atakhalako kumeneko nthawi yayitali, Abimeleki mfumu ya Afilisti, anasuzumira pa zenera kuyangʼana kunja, ndipo anaona Isake akugwiragwira Rebeka, mkazi wake.
9 et accersito ait perspicuum est quod uxor tua sit cur mentitus es sororem tuam esse respondit timui ne morerer propter eam
Choncho Abimeleki anamuyitanitsa Isake nati, “Uyu ndi mkazi wako ndithu! Nanga bwanji umati, ‘Ndi mlongo wanga’?” Ndipo Isake anamuyankha kuti, “Ine ndimaganiza kuti ndingataye moyo wanga chifukwa cha iyeyu.”
10 dixitque Abimelech quare inposuisti nobis potuit coire quispiam de populo cum uxore tua et induxeras super nos grande peccatum praecepitque omni populo dicens
Tsono Abimeleki anati, “Nʼchiyani chimene watichitira? Mmodzi mwa anthuwa anatsala pangʼono kugona ndi mkazi wako ndipo ukanatisandutsa ife kukhala olakwa.”
11 qui tetigerit hominis huius uxorem morte morietur
Choncho Abimeleki analamula anthu ake onse nati, “Aliyense amene avutitse munthu uyu pamodzi ndi mkazi wake adzaphedwa ndithu.”
12 seruit autem Isaac in terra illa et invenit in ipso anno centuplum benedixitque ei Dominus
Isake anadzala mbewu mʼmunda, ndipo chaka chomwecho anakolola zinthu zambiri chifukwa Yehova anamudalitsa.
13 et locupletatus est homo et ibat proficiens atque succrescens donec magnus vehementer effectus est
Isake analemera. Chuma chake chinkachulukirachulukira mpaka anasanduka munthu wolemera kwambiri.
14 habuit quoque possessionem ovium et armentorum et familiae plurimum ob haec invidentes ei Palestini
Anali ndi nkhosa, ngʼombe ndi antchito ambiri mwakuti Afilisti anamuchitira nsanje.
15 omnes puteos quos foderant servi patris illius Abraham illo tempore obstruxerunt implentes humo
Nthawi iyi nʼkuti Afilisti atakwirira ndi dothi zitsime zonse zimene antchito abambo ake Abrahamu anakumba mu nthawi ya abambo akewo.
16 in tantum ut ipse Abimelech diceret ad Isaac recede a nobis quoniam potentior nostri factus es valde
Ndipo Abimeleki anati kwa Isake, “Muchoke pakati pathu chifukwa mwasanduka wamphamvu kuposa ife.”
17 et ille discedens veniret ad torrentem Gerarae habitaretque ibi
Choncho Isake anachokako kumeneko nakakhala ku chigwa cha Gerari kumene anakhazikikako.
18 rursum fodit alios puteos quos foderant servi patris sui Abraham et quos illo mortuo olim obstruxerant Philisthim appellavitque eos hisdem nominibus quibus ante pater vocaverat
Isake anafukulanso zitsime zija zimene zinakumbidwa mu nthawi ya abambo ake Abrahamu. Atamwalira Abrahamu, Afilisti anakwirira zitsimezi. Tsono anazitcha mayina omwewo amene abambo ake anazitcha.
19 foderunt in torrente et reppererunt aquam vivam
Antchito a Isake anakumba mʼchigwamo ndipo anapezamo kasupe wa madzi.
20 sed et ibi iurgium fuit pastorum Gerarae adversum pastores Isaac dicentium nostra est aqua quam ob rem nomen putei ex eo quod acciderat vocavit Calumniam
Koma abusa a ku Gerari anakangana ndi abusa a Isake nati, “Madziwa ndi athu.” Motero iye anachitcha chitsimecho Mkangano chifukwa anakangana naye.
21 foderunt et alium et pro illo quoque rixati sunt appellavitque eum Inimicitias
Kenaka iwo anakumba chitsime china, koma anakangananso chifukwa cha chitsimecho. Choncho anachitcha dzina lakuti Chidani.
22 profectus inde fodit alium puteum pro quo non contenderunt itaque vocavit nomen illius Latitudo dicens nunc dilatavit nos Dominus et fecit crescere super terram
Anachokapo pamenepo nakakumba china. Koma apa sanakanganiranenso ndi munthu. Iye anachitcha Kutakasuka, nati, “Tsopano Yehova watipatsa ife malo otakasukirako ndipo tilemera muno.”
23 ascendit autem ex illo loco in Bersabee
Kenaka Isake anachoka ku malo kuja kupita ku Beeriseba.
24 ubi apparuit ei Dominus in ipsa nocte dicens ego sum Deus Abraham patris tui noli metuere quia tecum sum benedicam tibi et multiplicabo semen tuum propter servum meum Abraham
Usiku umenewo Yehova anadza kwa Isake nati, “Ine ndine Mulungu wa abambo ako Abrahamu. Usachite mantha popeza Ine ndili ndi iwe. Ndidzakudalitsa ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri chifukwa cha mtumiki wanga Abrahamu.”
25 itaque aedificavit ibi altare et invocato nomine Domini extendit tabernaculum praecepitque servis suis ut foderent puteum
Isake anamanga guwa lansembe pamenepo ndipo anapembedza Yehova. Pomwepo anamanga tenti yake, ndipo antchito ake anakumba chitsime.
26 ad quem locum cum venissent de Geraris Abimelech et Ochozath amicus illius et Fichol dux militum
Abimeleki pamodzi ndi Ahuzati mlangizi wake ndi Fikolo mkulu wa ankhondo ake anabwera kwa Isake kuchokera ku Gerari.
27 locutus est eis Isaac quid venistis ad me hominem quem odistis et expulistis a vobis
Tsopano Isake anawafunsa kuti, “Bwanji mwabwera kwa ine, popeza munandichitira nkhanza ndi kundithamangitsa?”
28 qui responderunt vidimus tecum esse Dominum et idcirco nunc diximus sit iuramentum inter nos et ineamus foedus
Iwo anayankha, “Tsopano tadziwa kuti Yehova anali ndi iwe; ndiye taganiza kuti inu ndi ife tichite lumbiro. Ife tichite pangano ndi inu
29 ut non facias nobis quicquam mali sicut et nos nihil tuorum adtigimus nec fecimus quod te laederet sed cum pace dimisimus auctum benedictione Domini
kuti inu simudzatichitira zoyipa monga ifenso sitinakuchitireni nkhondo. Ife tinakuchitirani zabwino zokhazokha, ndipo tinakulolani kuti musamuke kuchoka kwathu mu mtendere. Tsopano Yehova wakudalitsani.”
30 fecit ergo eis convivium et post cibum et potum
Tsono Isake anawakonzera phwando, ndipo anadya ndi kumwa.
31 surgentes mane iuraverunt sibi mutuo dimisitque eos Isaac pacifice in locum suum
Mmawa wake aliyense analumbira pangano kwa mnzake. Tsono Isake anawalola kuti anyamuke ndipo anamusiya mu mtendere.
32 ecce autem venerunt in ipso die servi Isaac adnuntiantes ei de puteo quem foderant atque dicentes invenimus aquam
Tsiku limenelo, antchito a Isake anabwera namuwuza za chitsime chimene anakumba. Iwo anati, “Tawapeza madzi!”
33 unde appellavit eum Abundantiam et nomen urbi inpositum est Bersabee usque in praesentem diem
Iye chitsimecho anachitcha Pangano. Nʼchifukwa chake mzindawu umatchedwa Beeriseba mpaka lero.
34 Esau vero quadragenarius duxit uxores Iudith filiam Beeri Hetthei et Basemath filiam Helon eiusdem loci
Pamene Esau anali ndi zaka 40, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Mhiti. Anakwatiranso Basemati mwana wa mkazi wa Eloni Mhiti.
35 quae ambae offenderant animum Isaac et Rebeccae
Akazi awiriwa anasandutsa Isake ndi Rebeka kukhala ndi moyo wa madandawulo nthawi zonse.