< Exodus 40 >

1 locutusque est Dominus ad Mosen dicens
Kenaka Yehova anati kwa Mose,
2 mense primo die prima mensis eriges tabernaculum testimonii
“Imika chihema, tenti ya msonkhano, tsiku loyamba la mwezi.
3 et pones in eo arcam dimittesque ante illam velum
Uyikemo bokosi la umboni ndipo uphimbe bokosilo ndi katani.
4 et inlata mensa pones super eam quae rite praecepta sunt candelabrum stabit cum lucernis suis
Ulowetsemo tebulo ndi kuyika zimene zimakhala pamenepo. Kenaka ulowetse choyikapo nyale ndipo uyikepo nyale zake.
5 et altare aureum in quo adoletur incensum coram arca testimonii tentorium in introitu tabernaculi pones
Uyike guwa lofukiza la golide patsogolo pa bokosi la umboni ndipo uyike katani ya pa chipata cha chihema.
6 et ante illud altare holocausti
“Uyike guwa lansembe yopsereza patsogolo pa chipata cha chihema, tenti ya msonkhano.
7 labrum inter altare et tabernaculum quod implebis aqua
Uyike beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo uyikemo madzi.
8 circumdabisque atrium tentoriis et ingressum eius
Upange bwalo lozungulira chihemacho ndipo uyike katani ya pa chipata cha bwalolo.
9 et adsumpto unctionis oleo ungues tabernaculum cum vasis suis ut sanctificentur
“Utenge mafuta wodzozera ndipo udzoze chihema ndi chilichonse chili mʼmenemo ndipo zidzakhala zoyeretsedwa.
10 altare holocausti et omnia vasa eius
Kenaka udzoze guwa lansembe lopsereza ndi ziwiya zake zonse. Ulipatule guwalo ndipo lidzakhala loyera kwambiri.
11 labrum cum basi sua omnia unctionis oleo consecrabis ut sint sancta sanctorum
Udzoze beseni ndi miyendo yake ndipo uzipatule.
12 adplicabisque Aaron et filios eius ad fores tabernaculi testimonii et lotos aqua
“Ubwere ndi Aaroni ndi ana ake pa chipata cha tenti ya msonkhano ndipo uwasambitse ndi madzi.
Kenaka umuveke Aaroni zovala zopatulika, umudzoze ndi kumupatula kotero kuti athe kunditumikira monga wansembe.
Ubweretse ana ake ndipo uwaveke minjiro.
15 indues sanctis vestibus ut ministrent mihi et unctio eorum in sacerdotium proficiat sempiternum
Uwadzoze monga momwe unadzozera abambo awo, kotero kuti anditumikire monga ansembe. Kudzozedwako kudzakhala unsembe wawo pa mibado ndi mibado”
16 fecitque Moses omnia quae praeceperat Dominus
Mose anachita zonse monga Yehova anamulamulira.
17 igitur mense primo anni secundi in prima die mensis conlocatum est tabernaculum
Kotero anayimika chihema tsiku loyamba la mwezi woyamba mʼchaka chachiwiri.
18 erexitque illud Moses et posuit tabulas ac bases et vectes statuitque columnas
Nthawi imene Mose anayimika chihema, anayika matsinde mʼmalo ake, kuyimitsa maferemu, kulowetsa mitanda ndi kuyika nsichi.
19 et expandit tectum super tabernaculum inposito desuper operimento sicut Dominus imperarat
Kenaka anayika tenti pamwamba pa chihema ndipo anayika chophimba pa tenti monga momwe Yehova analamulira Mose.
20 posuit et testimonium in arca subditis infra vectibus et oraculum desuper
Iye anatenga miyala ya umboni nayika mʼbokosi lija ndi kuyika chivundikiro pamwamba pake.
21 cumque intulisset arcam in tabernaculum adpendit ante eam velum ut expleret Domini iussionem
Kenaka analowetsa bokosilo mʼchihema ndipo anapachika katani ndi kubisa bokosi la umboni monga momwe Yehova analamulira iye.
22 posuit et mensam in tabernaculo testimonii ad plagam septentrionalem extra velum
Mose anayika tebulo mu tenti ya msonkhano kumpoto kwa chihema, kunja kwa katani,
23 ordinatis coram propositionis panibus sicut praeceperat Dominus Mosi
ndipo anayikapo buledi pamaso pa Yehova, monga momwe Yehova analamulira Mose.
24 posuit et candelabrum in tabernaculum testimonii e regione mensae in parte australi
Iye anayikanso choyikapo nyale mu tenti ya msonkhano moyangʼanana ndi tebulo mbali yakummwera kwa chihema.
25 locatis per ordinem lucernis iuxta praeceptum Domini
Ndipo anayikapo nyale zija pamaso pa Yehova, monga Yehova analamulira Mose.
26 posuit et altare aureum sub tecto testimonii contra velum
Mose anayika guwa la golide mu tenti ya msonkhano patsogolo pa katani
27 et adolevit super eo incensum aromatum sicut iusserat Dominus
ndipo anapserezapo lubani wonunkhira monga Yehova anamulamulira.
28 posuit et tentorium in introitu tabernaculi
Kenaka anayika katani ya pa chipata cha chihema.
29 et altare holocausti in vestibulo testimonii offerens in eo holocaustum et sacrificia ut Dominus imperarat
Iye anayika guwa lansembe yopsereza pafupi ndi chipata cha chihema, tenti ya msonkhano, ndipo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe ya ufa monga Yehova anamulamulira.
30 labrum quoque statuit inter tabernaculum testimonii et altare implens illud aqua
Iye anayika beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo anathiramo madzi wosamba,
31 laveruntque Moses et Aaron ac filii eius manus suas et pedes
ndipo Mose, Aaroni ndi ana ake amasamba manja ndi mapazi awo.
32 cum ingrederentur tectum foederis et accederent ad altare sicut praeceperat Dominus
Iwo amasamba nthawi zonse akamalowa mu tenti ya msonkhano kapena kuyandikira guwa lansembe monga Yehova analamulira Mose.
33 erexit et atrium per gyrum tabernaculi et altaris ducto in introitu eius tentorio postquam cuncta perfecta sunt
Kenaka Mose anamanga bwalo kuzungulira chihema ndi guwa lansembe ndipo anayika katani ya pa chipata cha bwalo. Kotero Mose anamaliza ntchito.
34 operuit nubes tabernaculum testimonii et gloria Domini implevit illud
Kenaka mtambo unaphimba tenti ya msonkhano, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.
35 nec poterat Moses ingredi tectum foederis nube operiente omnia et maiestate Domini coruscante quia cuncta nubes operuerat
Mose sanathe kulowa mu tenti ya msonkhano chifukwa mtambo unali utakhazikika pa chihemacho, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.
36 si quando nubes tabernaculum deserebat proficiscebantur filii Israhel per turmas suas
Pa maulendo awo onse, mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso pamene analipo.
37 si pendebat desuper manebant in eodem loco
Koma ngati mtambo sunachoke, iwo sankasamukanso mpaka tsiku limene udzachoke.
38 nubes quippe Domini incubabat per diem tabernaculo et ignis in nocte videntibus populis Israhel per cunctas mansiones suas
Kotero mtambo wa Yehova unkakhala pamwamba pa chihema usana, ndi mtambo wamoto umakhala usiku, pamaso pa nyumba yonse ya Israeli pa masiku onse aulendo wawo.

< Exodus 40 >