< Exodus 12 >
1 dixit quoque Dominus ad Mosen et Aaron in terra Aegypti
Yehova anayankhula kwa Mose ndi Aaroni mʼdziko la Igupto kuti,
2 mensis iste vobis principium mensuum primus erit in mensibus anni
“Mwezi uno uzikhala mwezi wanu woyamba wa chaka.
3 loquimini ad universum coetum filiorum Israhel et dicite eis decima die mensis huius tollat unusquisque agnum per familias et domos suas
Muliwuze khamu lonse la Israeli kuti pa tsiku la khumi la mwezi uno, munthu aliyense asankhire banja lake mwana wankhosa mmodzi. Banja lililonse litenge mwana wankhosa mmodzi.
4 sin autem minor est numerus ut sufficere possit ad vescendum agnum adsumet vicinum suum qui iunctus est domui eius iuxta numerum animarum quae sufficere possunt ad esum agni
Ngati banja lili lochepa moti silingathe kudya nyama yonse ya nkhosa, ligawane ndi banja lomwe layandikana nalo nyumba. Mabanja adziwiretu chiwerengero cha anthu amene alipo pokonzekera zimenezi. Muwerengere kuchuluka kwa nyama imene anthu adzadye potengera mmene munthu mmodzi angadyere.
5 erit autem agnus absque macula masculus anniculus iuxta quem ritum tolletis et hedum
Ziweto zimene musankhe ziyenera kukhala zazimuna za chaka chimodzi, zopanda chilema, ndipo zikhale nkhosa kapena mbuzi.
6 et servabitis eum usque ad quartamdecimam diem mensis huius immolabitque eum universa multitudo filiorum Israhel ad vesperam
Muzisunge mpaka tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi, pamene gulu lonse la Aisraeli lidzaphe nyamazo madzulo.
7 et sument de sanguine ac ponent super utrumque postem et in superliminaribus domorum in quibus comedent illum
Ndipo adzatengeko magazi anyamazo ndi kuwaza pa mphuthu ziwiri za chitseko ndiponso pamwamba pa chitseko cha nyumba mmene adzadyeremo ana ankhosawo.
8 et edent carnes nocte illa assas igni et azymos panes cum lactucis agrestibus
Adzawotche nyamayo ndi kudya usiku womwewo, ndipo adzayidye ndi buledi wophikidwa popanda yisiti pamodzi ndi masamba wowawa.
9 non comedetis ex eo crudum quid nec coctum aqua sed assum tantum igni caput cum pedibus eius et intestinis vorabitis
Musadzadye yayiwisi kapena yophika, koma mudzawotche yonse, mutu, miyendo ndi zamʼmimba.
10 nec remanebit ex eo quicquam usque mane si quid residui fuerit igne conburetis
Musadzasiye nyama ina mpaka mmawa, ngati ina idzatsala mpaka mmawa, mudzayitenthe.
11 sic autem comedetis illum renes vestros accingetis calciamenta habebitis in pedibus tenentes baculos in manibus et comedetis festinantes est enim phase id est transitus Domini
Muzidzadya nyamayo mutavala chotere, pokonzekera ulendo: mudzazimangirire lamba mʼchiwuno, nsapato zanu kuphazi ndi ndodo yanu kumanja. Mudzadye mofulumira. Imeneyi ndi Paska ya Yehova.
12 et transibo per terram Aegypti nocte illa percutiamque omne primogenitum in terra Aegypti ab homine usque ad pecus et in cunctis diis Aegypti faciam iudicia ego Dominus
“Usiku umenewo Ine ndidzadutsa mʼdziko la Igupto ndipo ndidzapha chilichonse choyamba kubadwa kuyambira mwana wa munthu aliyense mpaka ana aziweto. Ndidzalanganso milungu yonse ya Igupto. Ine ndine Yehova.
13 erit autem sanguis vobis in signum in aedibus in quibus eritis et videbo sanguinem ac transibo vos nec erit in vobis plaga disperdens quando percussero terram Aegypti
Magazi amene mudzawaze pa mphuthu za zitseko ndi pamwamba pa zitseko aja adzakhala ngati chizindikiro. Ine ndikadzaona magaziwo ndidzakudutsani, ndipo ndikadzamakantha anthu a Igupto, mliri wosakazawu sudzakukhudzani.
14 habebitis autem hanc diem in monumentum et celebrabitis eam sollemnem Domino in generationibus vestris cultu sempiterno
“Ili ndi tsiku la chikumbutso. Tsiku limeneli muzidzachita chikondwerero, kupembedza Yehova. Mibado yonse imene ikubwera izidzakumbukira tsiku limeneli ngati lamulo lamuyaya ndi kuti pa tsikuli azidzachita chikondwerero cholemekeza Yehova.
15 septem diebus azyma comedetis in die primo non erit fermentum in domibus vestris quicumque comederit fermentatum peribit anima illa de Israhel a primo die usque ad diem septimum
Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti. Tsiku loyamba muzichotsa yisiti mʼnyumba zanu, ngati aliyense adzadya kanthu kalikonse kali ndi yisiti kuyambira tsiku loyamba mpaka tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzayenera kuchotsedwa mʼgulu la Israeli.
16 dies prima erit sancta atque sollemnis et dies septima eadem festivitate venerabilis nihil operis facietis in eis exceptis his quae ad vescendum pertinent
Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika, ndipo winanso uzikhala pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Musamagwire ntchito masiku onsewa, koma ntchito yokonza chakudya yokha kuti aliyense adye. Izi ndi zimene muzichita.
17 et observabitis azyma in eadem enim ipsa die educam exercitum vestrum de terra Aegypti et custodietis diem istum in generationes vestras ritu perpetuo
“Muzichita chikondwerero cha buledi wopanda yisiti, chifukwa ndi pa tsiku limeneli ndinatulutsa magulu anu mʼdziko la Igupto. Muzikondwerera tsiku limeneli pa mibado yonse ngati lamulo lamuyaya.
18 primo mense quartadecima die mensis ad vesperam comedetis azyma usque ad diem vicesimam primam eiusdem mensis ad vesperam
Mwezi woyamba muzidzadya buledi wopanda yisiti kuyambira madzulo tsiku la 14 la mweziwo mpaka tsiku la 21 mwezi womwewo.
19 septem diebus fermentum non invenietur in domibus vestris qui comederit fermentatum peribit anima eius de coetu Israhel tam de advenis quam de indigenis terrae
Yisiti asamapezeka mʼnyumba zanu kwa masiku asanu ndi awiri. Ndipo aliyense amene adya chakudya chimene muli yisiti, munthu ameneyo ayenera kuchotsedwa mʼgulu la Aisraeli, kaya iyeyo ndi mlendo kapena mbadwa.
20 omne fermentatum non comedetis in cunctis habitaculis vestris edetis azyma
Musadye chilichonse chokhala ndi yisiti. Kulikonse kumene mukukhala, muyenera kudya buledi wopanda yisiti.”
21 vocavit autem Moses omnes seniores filiorum Israhel et dixit ad eos ite tollentes animal per familias vestras immolate phase
Ndipo Mose anasonkhanitsa akuluakulu onse a Israeli nati, “Pitani msanga kukasankha nkhosa zokwanira pa mabanja anu, ndipo muziphe ngati Paska.
22 fasciculumque hysopi tinguite sanguine qui est in limine et aspergite ex eo superliminare et utrumque postem nullus vestrum egrediatur ostium domus suae usque mane
Mutengenso nthambi ya chitsamba cha hisope, muchiviyike mʼmagazi amene mwawayika mʼbeseni ndipo muwaze ena mwa magaziwo pamwamba ndi mʼmbali mwa mphuthu za chitseko. Palibe aliyense wa inu amene adzatuluke mʼnyumba yake mpaka mmawa.
23 transibit enim Dominus percutiens Aegyptios cumque viderit sanguinem in superliminari et in utroque poste transcendet ostium et non sinet percussorem ingredi domos vestras et laedere
Pamene Yehova adzadutsa mʼdziko kudzakantha Aigupto, nʼkuona magazi pamwamba ndi mʼmbali mwa mphuthu za chitseko, Iye adzadutsa khomo limenelo ndipo sadzalola woonongayo kuti alowe mʼnyumba zanu kuti akukantheni.
24 custodi verbum istud legitimum tibi et filiis tuis usque in aeternum
“Muzimvera malamulo amenewa kwa muyaya, inu ndi zidzukulu zanu.
25 cumque introieritis terram quam Dominus daturus est vobis ut pollicitus est observabitis caerimonias istas
Mukakalowa mʼdziko limene Yehova adzakupatseni monga analonjeza, mukasunge mwambo umenewu.
26 et cum dixerint vobis filii vestri quae est ista religio
Ndipo ana anu akakakufunsani kuti, ‘Mwambo umenewu ukutanthauza chiyani?’
27 dicetis eis victima transitus Domini est quando transivit super domos filiorum Israhel in Aegypto percutiens Aegyptios et domos nostras liberans incurvatusque populus adoravit
Inu mukawawuze kuti, ‘Ndi nsembe ya Paska ya Yehova, popeza pamene ankakantha nyumba za Aigupto anasiya nyumba zathu.’” Kenaka anthu anawerama napembedza.
28 et egressi filii Israhel fecerunt sicut praeceperat Dominus Mosi et Aaron
Aisraeli anachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aaroni.
29 factum est autem in noctis medio percussit Dominus omne primogenitum in terra Aegypti a primogenito Pharaonis qui sedebat in solio eius usque ad primogenitum captivae quae erat in carcere et omne primogenitum iumentorum
Pakati pa usiku Yehova anakantha ana onse oyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira woyamba kubadwa wa Farao, amene amakhala pa mpando waufumu wa Faraoyo, mpaka mwana woyamba kubadwa wa munthu amene anali mʼdzenje, pamodzinso ndi ana oyamba kubadwa a ziweto zawo.
30 surrexitque Pharao nocte et omnes servi eius cunctaque Aegyptus et ortus est clamor magnus in Aegypto neque enim erat domus in qua non iaceret mortuus
Farao ndi nduna zake zonse ndiponso Aigupto onse anadzuka pakati pa usiku, ndipo kunali kulira kwakukulu mʼdziko lonse la Igupto, pakuti panalibe nyumba imene munalibe munthu wakufa.
31 vocatisque Mosen et Aaron nocte ait surgite egredimini a populo meo et vos et filii Israhel ite immolate Domino sicut dicitis
Pakati pa usiku Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Nyamukani! Asiyeni anthu anga, inu ndi Aisraeli! Pitani, kapembedzeni Yehova monga munapempha.
32 oves vestras et armenta adsumite ut petieratis et abeuntes benedicite mihi
Tengani ziweto ndi ngʼombe zanu ndipo pitani kapembedzeni Mulungu wanu monga munanenera kuti ine ndidalitsike.”
33 urguebantque Aegyptii populum de terra exire velociter dicentes omnes moriemur
Aigupto anawawumiriza anthuwo kuti atuluke mofulumira ndi kusiya dziko lawo. Iwo anati, “Ngati sitiwalola kutero, tonse tidzafa.”
34 tulit igitur populus conspersam farinam antequam fermentaretur et ligans in palliis posuit super umeros suos
Motero anthuwo ananyamula ufa wawo wopangira buledi asanathiremo yisiti ndipo anasenza pa mapewa awo pamodzi ndi zokandiramo buledi atazikulunga mu nsalu.
35 feceruntque filii Israhel sicut praeceperat Moses et petierunt ab Aegyptiis vasa argentea et aurea vestemque plurimam
Aisraeli anachita monga anawawuzira Mose kuti apemphe kwa Aigupto zozikongoletsera zasiliva ndi zagolide ndi zovala.
36 dedit autem Dominus gratiam populo coram Aegyptiis ut commodarent eis et spoliaverunt Aegyptios
Yehova anafewetsa mtima Aigupto kuti akomere mtima Aisraeliwo ndipo anawapatsa zimene anawapempha. Motero Aisraeli anawalanda zinthu Aigupto.
37 profectique sunt filii Israhel de Ramesse in Soccoth sescenta ferme milia peditum virorum absque parvulis
Aisraeli anayenda ulendo kuchokera ku Ramesesi mpaka kukafika ku Sukoti. Anthu aamuna oyenda pansi analipo 600,000 osawerengera akazi ndi ana.
38 sed et vulgus promiscuum innumerabile ascendit cum eis oves et armenta et animantia diversi generis multa nimis
Anthu enanso ambiri anapita nawo, kuphatikizanso gulu lalikulu la ziweto, mbuzi, nkhosa pamodzi ndi ngʼombe.
39 coxeruntque farinam quam dudum conspersam de Aegypto tulerant et fecerunt subcinericios panes azymos neque enim poterant fermentari cogentibus exire Aegyptiis et nullam facere sinentibus moram nec pulmenti quicquam occurrerant praeparare
Iwo anapanga buledi wopanda yisiti ndi ufa umene anachoka nawo ku Igupto. Ufawo unalibe yisiti chifukwa anachita kuthamangitsidwa ku Igupto ndipo analibe nthawi yokonzera chakudya chawo.
40 habitatio autem filiorum Israhel qua manserant in Aegypto fuit quadringentorum triginta annorum
Ndipo Aisraeli anakhala ku Igupto kwa zaka 430.
41 quibus expletis eadem die egressus est omnis exercitus Domini de terra Aegypti
Pa tsiku lomwelo limene anakwanitsa zaka 430, magulu onse a Yehova anatuluka mʼdziko la Igupto.
42 nox est ista observabilis Domini quando eduxit eos de terra Aegypti hanc observare debent omnes filii Israhel in generationibus suis
Usiku wonse Yehova anachezera kutulutsa ana a Israeli mʼdziko la Igupto. Nʼchifukwa chake pa tsiku limeneli Aisraeli onse azichezera usiku wonse kulemekeza Mulungu kamba ka mibado yonse ya mʼtsogolo.
43 dixitque Dominus ad Mosen et Aaron haec est religio phase omnis alienigena non comedet ex eo
Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Malamulo a Paska ndi awa: “Mlendo asadye Paska.
44 omnis autem servus empticius circumcidetur et sic comedet
Kapolo aliyense amene munagula angadye ngati atayamba wachita mdulidwe.
45 advena et mercennarius non edent ex eo
Koma amene mukukhala naye kwa kanthawi kapena waganyu asadye Paska.
46 in una domo comedetur nec efferetis de carnibus eius foras nec os illius confringetis
“Muzidyera Paska mʼnyumba imodzi. Musatulutse nyama iliyonse kunja kwa nyumba. Musaswe mafupa aliwonse.
47 omnis coetus filiorum Israhel faciet illud
Gulu lonse la Israeli lizichita mwambo wachikondwererochi.
48 quod si quis peregrinorum in vestram voluerit transire coloniam et facere phase Domini circumcidetur prius omne masculinum eius et tunc rite celebrabit eritque sicut indigena terrae si quis autem circumcisus non fuerit non vescetur ex eo
“Ngati mlendo wokhala pakati panu angafune kuchita nawo mwambo wa chikondwerero cha Paska, cha Yehovachi, amuna onse a mʼnyumba mwake ayenera kuchita mdulidwe. Akatero muzimutenga ngati mbadwa pakati panu. Koma aliyense wosachita mdulidwe asadye Paska.
49 eadem lex erit indigenae et colono qui peregrinatur apud vos
Lamulo limeneli likhudza mbadwa ngakhalenso alendo wochita mdulidwe wokhala pakati panu.
50 fecerunt omnes filii Israhel sicut praeceperat Dominus Mosi et Aaron
“Aisraeli onse anachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aaroni.
51 et in eadem die eduxit Dominus filios Israhel de terra Aegypti per turmas suas
Ndipo tsiku lomwelo Yehova anatulutsa gulu lonse la ana a Israeli mʼdziko la Igupto.”