< Esther 9 >

1 igitur duodecimi mensis quem adar vocari ante iam diximus tertiadecima die quando cunctis Iudaeis interfectio parabatur et hostes eorum inhiabant sanguini versa vice Iudaei superiores esse coeperunt et se de adversariis vindicare
Pa mwezi wa 12, mwezi wa Adara pa tsiku la 13 la mwezi womwewo, tsiku limene lamulo loyamba lija la mfumu linayembekezereka kuti litsatidwe, pamene adani a Ayuda anati awononge Ayudawo, zinthu zinasintha. Ayuda ndiwo anawononga adani awo.
2 congregatique sunt per singulas civitates oppida et loca ut extenderent manum contra inimicos et persecutores suos nullusque ausus est resistere eo quod omnes populos magnitudinis eorum formido penetrarat
Ayuda anasonkhana mʼmizinda ya zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero kuthira nkhondo onse amene anafuna kuwawononga. Palibe amene akanalimbana nawo chifukwa anthu onse a mitundu ina anachita nawo mantha.
3 nam et provinciarum iudices duces et procuratores omnisque dignitas quae singulis locis et operibus praeerat extollebant Iudaeos timore Mardochei
Ndipo akuluakulu onse a zigawo, akalonga, akazembe ndi ogwira ntchito za mfumu anathandiza Ayuda, chifukwa anachita mantha ndi Mordekai.
4 quem principem esse palatii et plurimum posse cognoverant fama quoque nominis eius crescebat cotidie et per cunctorum ora volitabat
Pajatu Mordekai anali munthu wamkulu mʼnyumba ya ufumu. Mbiri yake inafalikira zigawo zonse, ndipo mphamvu zake zinakulirakulirabe.
5 itaque percusserunt Iudaei inimicos suos plaga magna et occiderunt eos reddentes eis quod sibi paraverant facere
Motero Ayuda anakantha adani awo onse ndi lupanga, kuwapha ndi kuwawononga, ndipo anachita chimene chinawakomera kwa adani awo.
6 in tantum ut etiam in Susis quingentos viros interficerent et decem extra filios Aman Agagitae hostis Iudaeorum quorum ista sunt nomina
Ku likulu la mzinda wa Susa, Ayuda anapha ndi kuwononga anthu 500.
7 Pharsandatha et Delphon et Esphata
Ayuda anaphanso Parisandata, Dalifoni, Asipata,
8 et Phorata et Adalia et Aridatha
Porata, Adaliya, Aridata,
9 et Ephermesta et Arisai et Aridai et Vaizatha
Parimasita, Arisai, Aridai ndi Vaisata,
10 quos cum occidissent praedas de substantiis eorum agere noluerunt
ana khumi a Hamani, mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalande katundu wawo.
11 statimque numerus eorum qui occisi erant in Susis ad regem relatus est
Tsiku lomwelo anawuza mfumu chiwerengero cha anthu amene anaphedwa mu likulu la mzinda wa Susa.
12 qui dixit reginae in urbe Susis interfecere Iudaei quingentos viros et alios decem filios Aman quantam putas eos exercere caedem in universis provinciis quid ultra postulas et quid vis ut fieri iubeam
Mfumu inati kwa mfumukazi Estere, “Ayuda apha ndi kuwononga anthu 500 ndi ana khumi a Hamani mu likulu la mzinda wa Susa. Nanga ku zigawo zina zonse za mfumu achitako chiyani? Kodi tsopano ukupemphanso chiyani? Chimene ukupempha ndidzakupatsa. Kodi ukufuna chiyani? Chimene ukufuna ndidzakupatsa.”
13 cui illa respondit si regi placet detur potestas Iudaeis ut sicut hodie fecerunt in Susis sic et cras faciant et decem filii Aman in patibulis suspendantur
Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni mfumu, apatseni chilolezo Ayuda okhala mu Susa kuti achitenso zimene achita lerozi mawa, potsata lamulo ndipo mulole kuti ana khumi a Hamani aja mitembo yawo ipachikidwe pa mtanda.”
14 praecepitque rex ut ita fieret statimque in Susis pependit edictum et decem Aman filii suspensi sunt
Choncho mfumu inalamula kuti izi zichitike. Anapereka lamulo mu Susa ndipo mitembo ya ana khumi a Hamani anayipachika pa mtanda.
15 congregatis Iudaeis quartadecima adar mensis die interfecti sunt in Susis trecenti viri nec eorum ab illis direpta substantia est
Ayuda a mu mzinda wa Susa anasonkhana pamodzi pa tsiku la 14 la mwezi wa Adara ndipo anapha anthu 300 mu Susa, koma sanatenge katundu wawo.
16 sed et per omnes provincias quae dicioni regis subiacebant pro animabus suis stetere Iudaei interfectis hostibus ac persecutoribus suis in tantum ut septuaginta quinque milia occisorum implerentur et nullus de substantiis eorum quicquam contingeret
Tsono Ayuda ena onse amene anali mu zigawo za mfumu anasonkhananso kudziteteza ndipo sanasautsidwenso ndi adani popeza anapha anthu 75,000 koma sanalande zofunkha zawo.
17 dies autem tertiusdecimus mensis adar unus apud omnes interfectionis fuit et quartodecimo die caedere desierunt quem constituerunt esse sollemnem ut in eo omni deinceps tempore vacarent epulis gaudio atque conviviis
Zonsezi zinachitika pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara ndipo pa tsiku la 14 anapumula ndi kupanga tsikuli kuti likhale la madyerero ndi chikondwerero.
18 at hii qui in urbe Susis caedem exercuerant tertiodecimo et quartodecimo eiusdem mensis die in caede versati sunt quintodecimo autem die percutere desierunt et idcirco eandem diem constituere sollemnem epularum atque laetitiae
Koma Ayuda okhala mu Susa anasonkhana pa tsiku la 13 ndi la 14 ndipo anakonza tsiku la 15 kuti likhale tsiku la madyerero ndi chikondwerero.
19 hii vero Iudaei qui in oppidis non muratis ac villis morabantur quartumdecimum diem mensis adar conviviorum et gaudii decreverunt ita ut exultent in eo et mittant sibi mutuo partes epularum et ciborum
Ichi ndi chifukwa chake Ayuda a ku midzi, amene amakhala mʼzithando amasunga tsiku la 14 la mwezi wa Adara ngati la madyerero ndi chikondwerero, tsiku lopatsana mphatso.
20 scripsit itaque Mardocheus omnia haec et litteris conprehensa misit ad Iudaeos qui in omnibus regis provinciis morabantur tam in vicino positis quam procul
Mordekai analemba mawu awa mʼmakalata ndipo anawatumiza kwa Ayuda onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero, a pafupi ndi a kutali:
21 ut quartamdecimam et quintamdecimam diem mensis adar pro festis susciperent et revertente semper anno sollemni honore celebrarent
Anati chaka chilichonse, Ayudawo azisunga tsiku la 14 ndi 15 la mwezi wa Adara,
22 quia in ipsis diebus se ulti sunt Iudaei de inimicis suis et luctus atque tristitia in hilaritatem gaudiumque conversa sint essentque istae dies epularum atque laetitiae et mitterent sibi invicem ciborum partes et pauperibus munuscula largirentur
ngati masiku amene Ayuda anapulumutsidwa kwa adani awo, ndiponso ngati mwezi umene chisoni chawo chinasandulika chimwemwe ndi kulira kwawo kunasandulika chikondwerero. Anawalembera kuti azisunga masikuwa ngati masiku a madyerero ndi chikondwerero, masiku opatsana mphatso zachakudya kwa wina ndi mnzake komanso opereka mphatso kwa osauka.
23 susceperuntque Iudaei in sollemnem ritum cuncta quae eo tempore facere coeperant et quae Mardocheus litteris facienda mandaverat
Choncho Ayuda anavomereza kusunga masikuwa ngati a chikondwerero monga analembera Mordekai.
24 Aman enim filius Amadathi stirpis Agag hostis et adversarius Iudaeorum cogitavit contra eos malum ut occideret illos atque deleret et misit phur quod nostra lingua vertitur in sortem
Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, mdani wa Ayuda onse, anakonza chiwembu chakupha ndi kuwononga Ayuda ndipo anachita maere otchedwa Purimu kuti awaphe ndi kuwawononga.
25 et postea ingressa est Hester ad regem obsecrans ut conatus eius litteris regis irriti fierent et malum quod contra Iudaeos cogitaverat reverteretur in caput eius denique et ipsum et filios eius adfixerunt cruci
Koma mfumu itazindikira za chiwembuchi, inalamula kuti zilembedwe mʼmakalata kuti chiwembu chimene Hamani anakonzera Ayuda chigwere pa iye mwini, ndi kuti iye pamodzi ndi ana ake apachikidwe pa mtanda.
26 atque ex illo tempore dies isti appellati sunt Phurim id est Sortium eo quod phur id est sors in urnam missa fuerit et cuncta quae gesta sunt epistulae id est libri huius volumine continentur
Ndi chifukwa chake masiku amenewa amatchedwa masiku a Purimu potsata dzina lakuti Purimu. Chifukwa cha kalata ya Mordekai ndiponso chifukwa cha zimene anaziona ndi kuwachitikira,
27 quaeque sustinuerint et quae deinceps inmutata sint suscepere Iudaei super se et semen suum et super cunctos qui religioni eorum voluerint copulari ut nulli liceat duos hos dies absque sollemnitate transigere quam scriptura testatur et certa expetunt tempora annis sibi iugiter succedentibus
Ayuda onse anagwirizana kukhazikitsa lamulo lokhudza iwo, zidzukulu zawo ndi onse amene adzapanga nawo ubale kuti asalephere kusunga masiku awiri amenewa chaka chilichonse monga zinalembedweramo ndiponso potsata nthawi imene anayika.
28 isti sunt dies quos nulla umquam delebit oblivio et per singulas generationes cunctae in toto orbe provinciae celebrabunt nec est ulla civitas in qua dies Phurim id est Sortium non observentur a Iudaeis et ab eorum progenie quae his caerimoniis obligata est
Azisunga ndi kukumbukira masiku amenewa mu mʼbado uliwonse ndi banja lililonse, mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse. Ndipo Ayuda asadzasiye kukondwerera masiku a Purimuwa ndiponso zidzukulu zawo zisadzaleke kuwakumbukira.
29 scripseruntque Hester regina filia Abiahil et Mardocheus Iudaeus etiam secundam epistulam ut omni studio dies ista sollemnis sanciretur in posterum
Choncho mfumukazi Estere, mwana wa mkazi wa Abihaili, pamodzi ndi Mordekai Myuda analemba ndi ulamuliro onse kutsimikizira kalata iyi yachiwiri yokhudza Purimu.
30 et miserunt ad omnes Iudaeos qui in centum viginti septem regis Asueri provinciis versabantur ut haberent pacem et susciperent veritatem
Ndipo Mordekai anatumiza makalata kwa Ayuda onse ku zigawo 127 za ufumu wa Ahasiwero. Kalatayi inali ya mawu a mtendere ndiponso a kukhulupirika
31 observantes dies Sortium et suo tempore cum gaudio celebrarent sicut constituerat Mardocheus et Hester et illi observanda susceperant a se et a semine suo ieiunia atque clamores et Sortium dies
kuti azisunga masiku a Purimu pa nyengo imene inavomerezeka monga mmene Mordekai Myuda ndi mfumukazi Estere anawalamulira ndiponso monga anadziyikira eni okha ndi zidzukulu zawo zonena za nthawi zawo za kusala zakudya ndi kulira.
32 et omnia quae libri huius qui vocatur Hester historia continentur
Lamulo la Estere linakhazikitsa mwambo wa Purimuwu ndipo zinalembedwa mʼmabuku.

< Esther 9 >