< Deuteronomii 32 >

1 audite caeli quae loquor audiat terra verba oris mei
Mverani, inu mayiko a mmwamba ndipo ine ndidzayankhula; imva, iwe dziko lapansi, mawu a pakamwa panga.
2 concrescat in pluvia doctrina mea fluat ut ros eloquium meum quasi imber super herbam et quasi stillae super gramina
Chiphunzitso changa chigwe ngati mvula ndipo mawu anga atsike ngati mame, ngati mvumbi pa udzu watsopano, ngati mvula yochuluka pa zomera zanthete.
3 quia nomen Domini invocabo date magnificentiam Deo nostro
Ndidzalalikira dzina la Yehova. Aa, tamandani ukulu wa Mulungu wathu!
4 Dei perfecta sunt opera et omnes viae eius iudicia Deus fidelis et absque ulla iniquitate iustus et rectus
Iye ndi Thanthwe, ntchito zake ndi zangwiro, njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika amene salakwitsa, Iye ndiye wolungama ndi wosalakwa.
5 peccaverunt ei non filii eius in sordibus generatio prava atque perversa
Koma iwo achita mosakhulupirika pamaso pake, iwo si ana akenso, koma iwo ndi mʼbado wachinyengo ndi wokhotakhota.
6 haecine reddis Domino popule stulte et insipiens numquid non ipse est pater tuus qui possedit et fecit et creavit te
Kodi mukumubwezera Yehova chotere, inu anthu opusa ndi opanda nzeru? Kodi Iye si Atate anu, Mlengi wanu, amene anakupangani ndi kukuwumbani?
7 memento dierum antiquorum cogita generationes singulas interroga patrem tuum et adnuntiabit tibi maiores tuos et dicent tibi
Kumbukirani masiku amakedzana; ganizirani za mibado yakalekale. Funsa abambo ako ndipo adzakuwuza, akuluakulu ako, ndipo adzakufotokozera.
8 quando dividebat Altissimus gentes quando separabat filios Adam constituit terminos populorum iuxta numerum filiorum Israhel
Pamene Wammwambamwamba anapereka mayiko kwa anthu a mitundu ina kukhala cholowa chawo, pamene analekanitsa anthu onse, anayikira malire anthu onse molingana ndi chiwerengero cha ana a Israeli.
9 pars autem Domini populus eius Iacob funiculus hereditatis eius
Pakuti gawo la Yehova ndi anthu ake, Yakobo ndiye cholowa chake.
10 invenit eum in terra deserta in loco horroris et vastae solitudinis circumduxit eum et docuit et custodivit quasi pupillam oculi sui
Anamupeza mʼchipululu, ku malo owuma ndi kopanda kanthu. Anamuteteza ndi kumusamalira; anamutchinjiriza ngati mwanadiso wake,
11 sicut aquila provocans ad volandum pullos suos et super eos volitans expandit alas suas et adsumpsit eum atque portavit in umeris suis
ngati chiwombankhanga chimene chimasasula chisa chake nʼkumazungulira pamwamba pa ana ake, chimene chimatambalalitsa mapiko ake kuti chigwire anawo ndi kuwanyamula pa mapiko ake otambalalawo.
12 Dominus solus dux eius fuit et non erat cum eo deus alienus
Yehova yekha ndiye anamutsogolera; popanda thandizo la mulungu wachilendo.
13 constituit eum super excelsam terram ut comederet fructus agrorum ut sugeret mel de petra oleumque de saxo durissimo
Anamuyendetsa pamwamba pa mapiri a mʼdziko ndi kumudyetsa zipatso za mʼminda. Anamudyetsa uchi wofula pa thanthwe, ndiponso mafuta ochokera mʼnthaka ya miyala,
14 butyrum de armento et lac de ovibus cum adipe agnorum et arietum filiorum Basan et hircos cum medulla tritici et sanguinem uvae biberet meracissimum
pamodzi ndi chambiko ndi mkaka wochokera ku ngʼombe ndi nkhosa, ndiponso ana ankhosa onenepa ndi mbuzi, pamodzinso ndi nkhosa zazimuna zabwino za ku Basani ndiponso tirigu wabwino kwambiri. Munamwa vinyo wa thovu lofiira.
15 incrassatus est dilectus et recalcitravit incrassatus inpinguatus dilatatus dereliquit Deum factorem suum et recessit a Deo salutari suo
Yesuruni ananenepa ndi kuyamba kuwukira; atakhuta, ananenepa ndi kukula thupi. Anasiya Mulungu amene anamulenga ndipo anakana Thanthwe ndi Mpulumutsi wake.
16 provocaverunt eum in diis alienis et in abominationibus ad iracundiam concitaverunt
Anamuchititsa nsanje ndi milungu yawo yachilendo ndiponso anamukwiyitsa ndi mafano awo onyansa.
17 immolaverunt daemonibus et non Deo diis quos ignorabant novi recentesque venerunt quos non coluerunt patres eorum
Anapereka nsembe kwa ziwanda zimene si Mulungu, milungu imene sankayidziwa nʼkale lomwe, milungu yongobwera kumene, milungu imene makolo anu sankayiopa.
18 Deum qui te genuit dereliquisti et oblitus es Domini creatoris tui
Inu munasiya Thanthwe limene linakulerani; munayiwala Mulungu amene anakubalani.
19 vidit Dominus et ad iracundiam concitatus est quia provocaverunt eum filii sui et filiae
Yehova anaona zimenezi ndipo anawakana chifukwa ana ake aamuna ndi aakazi anamukwiyitsa.
20 et ait abscondam faciem meam ab eis et considerabo novissima eorum generatio enim perversa est et infideles filii
Iye anati, “Ndidzawabisira nkhope yanga, ndi kuona kuti mathero awo adzakhala otani; pakuti ndi mʼbado wopotoka, ana amene ndi osakhulupirika.
21 ipsi me provocaverunt in eo qui non erat Deus et inritaverunt in vanitatibus suis et ego provocabo eos in eo qui non est populus et in gente stulta inritabo illos
Anandichititsa kukhala wansanje pamene ankapembedza chimene si mulungu ndi kundikwiyitsa chifukwa cha mafano awo achabechabe. Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake; ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.
22 ignis succensus est in furore meo et ardebit usque ad inferni novissima devorabitque terram cum germine suo et montium fundamenta conburet (Sheol h7585)
Pakuti mkwiyo wanga wayaka ngati moto, umene umayaka mpaka ku dziko la anthu akufa. Motowo udzanyeketsa dziko lapansi ndi zokolola zake ndipo udzapsereza maziko a mapiri. (Sheol h7585)
23 congregabo super eos mala et sagittas meas conplebo in eis
“Ndidzawawunjikira masautso ndipo mivi yanga yonse idzathera pa iwo.
24 consumentur fame et devorabunt eos aves morsu amarissimo dentes bestiarum inmittam in eos cum furore trahentium super terram atque serpentium
Ndidzawatumizira njala yoopsa, malungo woopsa ndi nthenda zofa nazo; ndidzawatumizira zirombo zakuthengo zowavuta, ululu wa njoka ya mʼphiri imene imakwawa pa fumbi.
25 foris vastabit eos gladius et intus pavor iuvenem simul ac virginem lactantem cum homine sene
Mʼmisewu lupanga lidzawasandutsa kukhala wopanda ana; mantha adzalamulira nyumba zawo. Anyamata ndi atsikana adzafa, ngakhalenso makanda ndi okalamba.
26 dixi ubinam sunt cessare faciam ex hominibus memoriam eorum
Ine ndinanena kuti ndidzawamwaza ndi kuwafafaniza kuti anthu asawakumbukirenso,
27 sed propter iram inimicorum distuli ne forte superbirent hostes eorum et dicerent manus nostra excelsa et non Dominus fecit haec omnia
koma sindinafune kuti adani anga adzandinyoze, mwina adani anga sadzandimvetsetsa ndipo adzanena kuti, ‘Tagonjetsa anthuwa ndife; Yehova sanachite zonsezi.’”
28 gens absque consilio est et sine prudentia
Iwo ndi mtundu wopanda maganizo, iwo alibe nzeru nʼpangʼono pomwe.
29 utinam saperent et intellegerent ac novissima providerent
Ngati iwo akanakhala anzeru akanamvetsetsa izi ndi kuzindikira kuti mathero awo adzakhala otani!
30 quomodo persequatur unus mille et duo fugent decem milia nonne ideo quia Deus suus vendidit eos et Dominus conclusit illos
Kodi munthu mmodzi akanathamangitsa bwanji anthu 1,000 kapena anthu awiri kuthamangitsa anthu 10,000, kuti awagonjetse, Thanthwe lawo likanapanda kuwagulitsa, Yehova akanapanda kuwataya?
31 non enim est Deus noster ut deus eorum et inimici nostri sunt iudices
Pakuti thanthwe lawo silofanana ndi Thanthwe lathu, ngakhale adani athu amavomereza zimenezi.
32 de vinea Sodomorum vinea eorum et de suburbanis Gomorrae uva eorum uva fellis et botri amarissimi
Mpesa wawo umachokera ku mpesa wa ku Sodomu ndiponso ku minda ya ku Gomora. Mphesa zawo zili ndi ululu wakupha ndipo maphava ake ndi owawa.
33 fel draconum vinum eorum et venenum aspidum insanabile
Vinyo wawo ndi wa ululu wa njoka, ululu woopsa wa mphiri.
34 nonne haec condita sunt apud me et signata in thesauris meis
“Kodi zimenezi sindinazisunge ndi kuzitsekera mʼkatikati mwa chuma changa?
35 mea est ultio et ego retribuam in tempore ut labatur pes eorum iuxta est dies perditionis et adesse festinant tempora
Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine. Pa nthawi yake phazi lawo lidzaterera; tsiku lawo la masautso layandikira ndipo chiwonongeko chawo chikubwera pa iwo mofulumira.”
36 iudicabit Dominus populum suum et in servis suis miserebitur videbit quod infirmata sit manus et clausi quoque defecerint residuique consumpti sint
Yehova adzaweruza anthu ake ndipo adzachitira atumiki ake chifundo pamene adzaona kuti mphamvu zawo zatha ndipo kuti palibe amene watsala, kapolo kapena mfulu.
37 et dicet ubi sunt dii eorum in quibus habebant fiduciam
Iye adzanena kuti, “Nanga ili kuti milungu yawo, thanthwe limene ankabisalamo,
38 de quorum victimis comedebant adipes et bibebant vinum libaminum surgant et opitulentur vobis et in necessitate vos protegant
milungu imene inkadya mafuta a nsembe zawo ndi kumwa vinyo wa chopereka chawo cha chakumwa?” Iwuzeni ibwere kuti idzakuthandizeni! Ibwere kuti idzakutetezenitu!
39 videte quod ego sim solus et non sit alius deus praeter me ego occidam et ego vivere faciam percutiam et ego sanabo et non est qui de manu mea possit eruere
“Onani tsopano kuti Ine ndine Iyeyo! Palibe mulungu wina koma Ine ndekha. Ine ndimapha ndiponso kupereka moyo, ndavulaza ndipo ndidzachiritsa, ndipo palibe angathe kupulumutsa munthu mʼmanja mwanga.
40 levabo ad caelum manum meam et dicam vivo ego in aeternum
Ndikweza dzanja langa kumwamba ndi kulumbira kuti, ‘Pali Ine wamoyo wamuyaya,
41 si acuero ut fulgur gladium meum et arripuerit iudicium manus mea reddam ultionem hostibus meis et his qui oderunt me retribuam
pamene ndidzanola lupanga langa lonyezimira ndipo dzanja liligwira pakubweretsa chiweruzo, ndidzabwezera chilango adani anga ndi kulanga onse odana nane.
42 inebriabo sagittas meas sanguine et gladius meus devorabit carnes de cruore occisorum et de captivitate nudati inimicorum capitis
Mivi yanga idzakhuta magazi awo pamene lupanga langa lidzawononga mnofu: magazi a anthu ophedwa ndi ogwidwa ukapolo, mitu ya atsogoleri a adani.’”
43 laudate gentes populum eius quia sanguinem servorum suorum ulciscetur et vindictam retribuet in hostes eorum et propitius erit terrae populi sui
Kondwerani, inu mitundu yonse ya anthu pamodzi ndi anthu ake, pakuti Iye adzabwezera chilango anthu amene anapha atumiki ake; adzabwezera chilango adani ake ndipo adzakhululukira dziko lake ndi la anthu ake.
44 venit ergo Moses et locutus est omnia verba cantici huius in auribus populi ipse et Iosue filius Nun
Mose anabwera ndi Yoswa mwana wa Nuni ndipo anayankhula mawu onsewa mʼnyimbo anthu akumva.
45 conplevitque omnes sermones istos loquens ad universum Israhel
Mose atatsiriza kunena mawu onsewa pamtima kwa Aisraeli,
46 et dixit ad eos ponite corda vestra in omnia verba quae ego testificor vobis hodie ut mandetis ea filiis vestris custodire et facere et implere universa quae scripta sunt legis huius
iye anawawuza kuti, “Muwasunge bwino mu mtima mwanu, mawu onse amene lero lino ndikukuwuzani kuti mudzawuze ana anu, kuti adzamvere mosamalitsa mawu onse a malamulo amenewa.
47 quia non in cassum praecepta sunt vobis sed ut singuli in eis viverent quae facientes longo perseveretis tempore in terra ad quam Iordane transmisso ingredimini possidendam
Mawuwa sikuti ndi mawu achabe kwa inu. Mawuwa ndi moyo wanu. Mukawamvera mudzakhala ndi moyo wautali mʼdziko limene mukukalitenga kukhala lanu mukawoloka Yorodani.”
48 locutusque est Dominus ad Mosen in eadem die dicens
Tsiku lomwelo Yehova anawuza Mose kuti,
49 ascende in montem istum Abarim id est transituum in montem Nebo qui est in terra Moab contra Hiericho et vide terram Chanaan quam ego tradam filiis Israhel obtinendam et morere in monte
“Pita ku mapiri a ku Abarimu ukakwere pa Phiri la Nebo ku Mowabu, moyangʼanana ndi Yeriko, ndipo ukaone dziko la Kanaani, dziko limene ndikulipereka kwa Aisraeli kukhala lawo.
50 quem conscendens iungeris populis tuis sicut mortuus est Aaron frater tuus in monte Hor et adpositus populis suis
Iwe udzafera pa phiri limenelo ndipo udzapita kumene makolo ako anapita, monga mʼbale wako Aaroni anafera pa phiri la Hori ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake.
51 quia praevaricati estis contra me in medio filiorum Israhel ad aquas Contradictionis in Cades deserti Sin et non sanctificastis me inter filios Israhel
Chifukwa chake nʼchakuti inu nonse awiri simunakhulupirike kwa Ine pamaso pa Aisraeli pa madzi a Meriba ku Kadesi mʼchipululu cha Zini chifukwa simunandilemekeze kokwanira pakati pa Aisraeli.
52 e contra videbis terram et non ingredieris in eam quam ego dabo filiis Israhel
Choncho udzalionera kutali dziko limene ndikupereka kwa Aisraeli. Sudzalowa mʼdziko limene ndi kulipereka kwa Aisraeli.”

< Deuteronomii 32 >