< Thessalonicenses Ii 2 >
1 rogamus autem vos fratres per adventum Domini nostri Iesu Christi et nostrae congregationis in ipsum
Pa za kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu ndiponso za kusonkhana kwathu kuti tikumane naye, abale, tikukupemphani
2 ut non cito moveamini a sensu neque terreamini neque per spiritum neque per sermonem neque per epistulam tamquam per nos quasi instet dies Domini
kuti musagwedezeke msanga mʼmaganizo kapena kuopsezedwa ndi uneneri, mbiri kapena kalata yokhala ngati yachokera kwa ife, yonena kuti tsiku lija la Ambuye linafika kale.
3 ne quis vos seducat ullo modo quoniam nisi venerit discessio primum et revelatus fuerit homo peccati filius perditionis
Musalole kuti wina aliyense akunamizeni mwa njira ina iliyonse. Pakuti tsikulo lisanafike, kudzakhala mpatuko waukulu kwambiri, ndipo kudzaoneka munthu woyipitsitsa uja, munthu woyenera kuwonongedwayo.
4 qui adversatur et extollitur supra omne quod dicitur Deus aut quod colitur ita ut in templo Dei sedeat ostendens se quia sit Deus
Iyeyo adzatsutsa ndi kudziyika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza. Iyeyo adzadzikhazika mʼNyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.
5 non retinetis quod cum adhuc essem apud vos haec dicebam vobis
Kodi simukukumbukira kuti pamene ndinali nanu pamodzi ndinkakuwuzani zimenezi?
6 et nunc quid detineat scitis ut reveletur in suo tempore
Ndipo tsopano mukudziwa chimene chikumuletsa kuonekera, koma adzawululika pa nthawi yake yoyenera.
7 nam mysterium iam operatur iniquitatis tantum ut qui tenet nunc donec de medio fiat
Pakuti mphamvu yobisika yoyipitsitsa ikugwira ntchito ngakhale tsopano; koma amene akutchinga mphamvuyo adzapitiriza kutero mpaka pamene wotchingayo adzachotsedwe.
8 et tunc revelabitur ille iniquus quem Dominus Iesus interficiet spiritu oris sui et destruet inlustratione adventus sui
Ndipo kenaka woyipitsitsayo adzaonekera, amene Ambuye Yesu adzamugonjetsa ndi mpweya otuluka mʼkamwa mwake ndi kumuwononga ndi ulemerero wa kubwera kwake.
9 eum cuius est adventus secundum operationem Satanae in omni virtute et signis et prodigiis mendacibus
Woyipitsitsayo adzabwera ndi mphamvu za Satana. Adzaonetsa mphamvu zake pochita zizindikiro ndi zodabwitsa zachinyengo.
10 et in omni seductione iniquitatis his qui pereunt eo quod caritatem veritatis non receperunt ut salvi fierent
Iye adzagwiritsa ntchito mtundu uliwonse wachinyengo kupusitsa amene akuwonongeka. Iwo akuwonongeka chifukwa akukana kukonda choonadi ndi kuti apulumutsidwe.
11 ideo mittit illis Deus operationem erroris ut credant mendacio
Chifukwa cha chimenechi, Mulungu akuwatumizira chinyengo chachikulu kuti akhulupirire bodza.
12 ut iudicentur omnes qui non crediderunt veritati sed consenserunt iniquitati
Choncho adzalangidwa onse amene sanakhulupirire choonadi, koma anakondwera mu zoyipa.
13 nos autem debemus gratias agere Deo semper pro vobis fratres dilecti a Deo quod elegerit nos Deus primitias in salutem in sanctificatione Spiritus et fide veritatis
Koma tiyenera kuyamika Mulungu chifukwa cha inu abale okondedwa mwa Ambuye, pakuti Mulungu anakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke chifukwa cha ntchito yoyeretsa ya Mzimu ndi chikhulupiriro chanu mʼchoonadi.
14 ad quod et vocavit vos per evangelium nostrum in adquisitionem gloriae Domini nostri Iesu Christi
Iye anakuyitanirani zimenezi kudzera mwa uthenga wathu wabwino, kuti mulandire nawo ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu.
15 itaque fratres state et tenete traditiones quas didicistis sive per sermonem sive per epistulam nostram
Kotero tsono, abale, imani mwamphamvu ndi kugwiritsa ziphunzitso zimene tinakupatsani kudzera mʼmawu apakamwa kapena kudzera mʼkalata.
16 ipse autem Dominus noster Iesus Christus et Deus et Pater noster qui dilexit nos et dedit consolationem aeternam et spem bonam in gratia (aiōnios )
Ambuye athu Yesu Khristu mwini ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ife ndipo mwachisomo chake anatipatsa kulimba mtima kwamuyaya ndi chiyembekezo chabwino, (aiōnios )
17 exhortetur corda vestra et confirmet in omni opere et sermone bono
akulimbikitseni ndi kukupatsani mphamvu yogwirira ntchito ndi kuyankhula zabwino zilizonse.