< Ii Paralipomenon 26 >
1 omnis autem populus Iuda filium eius Oziam annorum sedecim constituit regem pro patre suo Amasia
Kenaka anthu onse a ku Yuda anatenga Uziya amene anali wa zaka 16, namuyika kukhala mfumu mʼmalo mwa Amaziya abambo ake.
2 ipse aedificavit Ahilath et restituit eam dicioni Iudae postquam dormivit rex cum patribus suis
Iye anamanganso mzinda wa Eloti ndi kuwubwezeranso ku Yuda abambo ake atamwalira.
3 sedecim annorum erat Ozias cum regnare coepisset et quinquaginta duobus annis regnavit in Hierusalem nomen matris eius Hiechelia de Hierusalem
Uziya anali wa zaka 16 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 70. Dzina la amayi ake linali Yekoliya wa ku Yerusalemu.
4 fecitque quod erat rectum in oculis Domini iuxta omnia quae fecerat Amasias pater eius
Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Amaziya abambo ake.
5 et exquisivit Deum in diebus Zacchariae intellegentis et videntis Deum cumque requireret Dominum direxit eum in omnibus
Iye anapembedza Mulungu nthawi ya Zekariya, amene ankamulangiza za kuopa Mulungu amene anamupatsa chipambano.
6 denique egressus est et pugnavit contra Philisthim et destruxit murum Geth et murum Iabniae murumque Azoti aedificavit quoque oppida in Azoto et in Philisthim
Iyeyo anapita kukachita nkhondo ndi Afilisti ndipo anagwetsa makoma a Gati, Yabine ndi Asidodi. Ndipo kenaka anamanganso mizinda ya pafupi ndi Asidodi ndi malo ena pafupi ndi Afilisti.
7 et adiuvit eum Deus contra Philisthim et contra Arabas qui habitabant in Gurbaal et contra Ammanitas
Mulungu anamuthandiza polimbana ndi Afilisti ndi Aarabu amene amakhala ku Guri-Baala ndiponso polimbana ndi Ameuni.
8 pendebantque Ammanitae munera Oziae et divulgatum est nomen eius usque ad introitum Aegypti propter crebras victorias
Aamoni ankabweretsa msonkho kwa Uziya ndipo mbiri yake inamveka mpaka ku malire a dziko la Igupto chifukwa anali wamphamvu kwambiri.
9 aedificavitque Ozias turres in Hierusalem super portam Anguli et super portam Vallis et reliquas in eodem muri latere firmavitque eas
Uziya anamanga nsanja ku Yerusalemu ku Chipata Chapangodya, ku Chigwa cha Chipata ndi pokhotera mpanda, ndipo anayikamo chitetezo.
10 extruxit etiam turres in solitudine et fodit cisternas plurimas eo quod haberet multa pecora tam in campestribus quam in heremi vastitate vineas quoque habuit et vinitores in montibus et in Carmelo erat quippe homo agriculturae deditus
Iye anamanganso nsanja ku chipululu ndi kukumbanso zitsime zambiri chifukwa anali ndi ziweto zambiri mʼmbali mwa phiri ndi ku zigwa. Iye anali ndi anthu amene ankagwira ntchito mʼminda yake ndiponso mʼminda yake ya mphesa mʼphiri ndi malo achonde, pakuti ankakonda nthaka.
11 fuit autem exercitus bellatorum eius qui procedebant ad proelia sub manu Hiehihel scribae Maasiaeque doctoris et sub manu Ananiae qui erat de ducibus regis
Uziya anali ndi gulu lankhondo lophunzitsidwa bwino, lokonzekera kupita ku nkhondo mʼmagulu monga mwa chiwerengero chawo chimene mlembi Yeiyeli ndi Maaseya anasonkhanitsa motsogozedwa ndi Hananiya mmodzi mwa akuluakulu a mfumu.
12 omnisque numerus principum per familias virorum fortium duum milium sescentorum
Chiwerengero chonse cha atsogoleri a mʼmabanja oyangʼanira anthu ochita nkhondo chinali 2,600.
13 et sub eis universus exercitus trecentorum et septem milium quingentorum qui erant apti ad bella et pro rege contra adversarios dimicabant
Pansi pa ulamuliro wawo panali asilikali 307,500 ophunzitsidwa nkhondo, gulu lamphamvu lothandiza mfumu kulimbana ndi adani ake.
14 praeparavit quoque eis Ozias id est cuncto exercitui clypeos et hastas et galeas et loricas arcusque et fundas ad iaciendos lapides
Uziya anawapangira asilikaliwo zishango, mikondo, zipewa zankhondo, malaya ankhondo achitsulo, mauta ndi miyala yogendera.
15 et fecit in Hierusalem diversi generis machinas quas in turribus conlocavit et in angulis murorum ut mitterent sagittas et saxa grandia egressumque est nomen eius procul eo quod auxiliaretur ei Dominus et corroborasset illum
Mu Yerusalemu anapanga makina okonzedwa ndi anthu aluso amene amagwiritsidwa ntchito pa malo otetezera a pa nsanja ndi pa ngodya kuponyera mivi ndi kugubuduzira miyala. Mbiri yake inamveka kutali ndi ponseponse pakuti anathandizidwa kwambiri mpaka anakhala wamphamvu kwambiri.
16 sed cum roboratus esset elevatum est cor eius in interitum suum et neglexit Dominum Deum suum ingressusque templum Domini adolere voluit incensum super altare thymiamatis
Koma pamene Uziya anakhala wamphamvu kwambiri, kunyada kwake kunamuwononga. Iye sanakhulupirike kwa Yehova Mulungu wake, ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova kukafukiza lubani pa guwa lofukizira.
17 statimque ingressus post eum Azarias sacerdos et cum eo sacerdotes Domini octoginta viri fortissimi
Wansembe Azariya pamodzi ndi ansembe a Yehova ena 80 olimba mtima anamutsatira.
18 restiterunt regi atque dixerunt non est tui officii Ozia ut adoleas incensum Domino sed sacerdotum hoc est filiorum Aaron qui consecrati sunt ad huiuscemodi ministerium egredere de sanctuario ne contempseris quia non reputabitur tibi in gloriam hoc a Domino Deo
Iwo anatsutsana naye ndipo anati, “Sibwino kuti inu mfumu muzifukiza lubani koma zidzukulu za Aaroni, zimene zinapatulidwa kuti zizifukiza lubani. Chokani pa malo opatulika ano, pakuti inu mwakhala osakhulupirika, ndipo simudzalemekezedwa ndi Yehova Mulungu.”
19 iratusque est Ozias et tenens in manu turibulum ut adoleret incensum minabatur sacerdotibus statimque orta est lepra in fronte eius coram sacerdotibus in domo Domini super altare thymiamatis
Uziya, amene anali ndi chofukizira mʼmanja mwake wokonzeka kuti afukize lubani, anapsa mtima. Iye anakwiyira ansembewo. Ndipo ansembe aja akuona patsogolo pa guwa lofukizira lubani mʼNyumba ya Mulungu, khate linayamba pamphumi pake.
20 cumque respexisset eum Azarias pontifex et omnes reliqui sacerdotes viderunt lepram in fronte eius et festinato expulerunt eum sed et ipse perterritus adceleravit egredi eo quod sensisset ilico plagam Domini
Azariya, mkulu wa ansembe pamodzi ndi ansembe ena onse atamuyangʼana anaona kuti anali ndi khate pamphumi pake, ndipo anamutulutsa mofulumira. Ndipo iye mwini anafulumira kutuluka, chifukwa Yehova anamulanga.
21 fuit igitur Ozias rex leprosus usque ad diem mortis suae et habitavit in domo separata plenus lepra ob quam et eiectus fuerat de domo Domini porro Ioatham filius eius rexit domum regis et iudicabat populum terrae
Mfumu Uziya anali ndi khate mpaka tsiku limene anamwalira. Iye amakhala mʼnyumba ya yekha ngati wakhate, ndipo samalowa mʼNyumba ya Yehova. Yotamu mwana wake ndiye amayangʼanira nyumba yaufumu ndipo ankalamulira anthu a mʼdzikomo.
22 reliqua autem sermonum Oziae priorum et novissimorum scripsit Esaias filius Amos propheta
Ntchito zina za mfumu Uziya, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zinalembedwa ndi mneneri Yesaya mwana wa Amozi.
23 dormivitque Ozias cum patribus suis et sepelierunt eum in agro regalium sepulchrorum eo quod esset leprosus regnavitque Ioatham filius eius pro eo
Uziya analondola makolo ake, ndipo anamuyika pamodzi ndi makolo ake ku malo a manda a mafumu, koma osati mʼmanda mwawomo poti anthu anati, “Iyeyu anali ndi khate.” Ndipo Yotamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.