< I Samuelis 16 >

1 dixitque Dominus ad Samuhel usquequo tu luges Saul cum ego proiecerim eum ne regnet super Israhel imple cornu tuum oleo et veni ut mittam te ad Isai Bethleemitem providi enim in filiis eius mihi regem
Yehova anati kwa Samueli, “Kodi udzamulira Sauli mpaka liti, popeza Ine ndamukana kuti akhale mfumu ya Israeli? Dzaza mafuta mʼbotolo lako ndipo unyamuke kupita kwa Yese wa ku Betelehemu popeza ndadzisankhira mmodzi mwa ana ake kukhala mfumu.”
2 et ait Samuhel quomodo vadam audiet enim Saul et interficiet me et ait Dominus vitulum de armento tolles in manu tua et dices ad immolandum Domino veni
Koma Samueli anati, “Kodi ndingapite bwanji? Sauli akamva zimenezi adzandipha.” Yehova anayankha, “Tenga ngʼombe yayikazi ndipo ukanene kuti, ‘Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova.
3 et vocabis Isai ad victimam et ego ostendam tibi quid facias et ungues quemcumque monstravero tibi
Ukamuyitane Yese ku mwambo wa nsembe, ndipo ine ndidzakuwuza choti ukachite. Ukandidzozere amene ndikakulozere.’”
4 fecit ergo Samuhel sicut locutus est ei Dominus venitque in Bethleem et admirati sunt seniores civitatis occurrentes ei dixeruntque pacificus ingressus tuus
Samueli anachita zimene Yehova ananena, ndipo anabweradi ku Betelehemu kuja. Akuluakulu a mu mzindawo anamuchingamira ali njenjenje ndi mantha ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mwabwera mwa mtendere?”
5 et ait pacificus ad immolandum Domino veni sanctificamini et venite mecum ut immolem sanctificavit ergo Isai et filios eius et vocavit eos ad sacrificium
Samueli anayankha kuti, “Inde, kwabwino. Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova. Mudzipatule ndipo mubwere kudzapereka nsembe pamodzi nane.” Kenaka iye anamupatula Yese ndi ana ake aamuna ndipo anawayitana kudzapereka nsembe.
6 cumque ingressi essent vidit Heliab et ait num coram Domino est christus eius
Pamene anafika, Samueli anaona Eliabu ndipo anaganiza “Ndithu wodzozedwa wa Yehova uja ndi uyu wayima pamaso pakeyu.”
7 et dixit Dominus ad Samuhel ne respicias vultum eius neque altitudinem staturae eius quoniam abieci eum nec iuxta intuitum hominis iudico homo enim videt ea quae parent Dominus autem intuetur cor
Koma Yehova anati kwa Samueli, “Usaone maonekedwe ake kapena msinkhu wake, pakuti ndamukana iyeyu. Yehova sapenya zimene munthu amapenya. Anthu amapenya zakunja, koma Mulungu amapenya za mu mtima.”
8 et vocavit Isai Abinadab et adduxit eum coram Samuhel qui dixit nec hunc elegit Dominus
Kenaka Yese anayitana Abinadabu namubweretsa pamaso pa Samueli. Koma Samueli anati, “Yehova sanamusankhenso ameneyu.”
9 adduxit autem Isai Samma de quo ait etiam hunc non elegit Dominus
Ndipo Yese anayitana Sama, koma Samueli anati, “Ngakhale uyu Yehova sanamusankhe.”
10 adduxit itaque Isai septem filios suos coram Samuhel et ait Samuhel ad Isai non elegit Dominus ex istis
Pambuyo pake, Yese anayitana ana ake amuna asanu ndi awiri kuti apite kwa Samueli. Koma Samueli anati, “Yehova sanasankhe amenewa.”
11 dixitque Samuhel ad Isai numquid iam conpleti sunt filii qui respondit adhuc reliquus est parvulus et pascit oves et ait Samuhel ad Isai mitte et adduc eum nec enim discumbemus priusquam ille huc venerit
Tsono Samueli anafunsa Yese kuti, “Kodi awa ndi ana ako onse aamuna?” Yese anayankha kuti, “Ayi, alipo wina wamngʼono amene watsala, koma akuweta nkhosa.” Samueli anati, “Apite munthu akamutenge popeza sitipereka nsembe mpaka iye atabwera.”
12 misit ergo et adduxit eum erat autem rufus et pulcher aspectu decoraque facie et ait Dominus surge ungue eum ipse est enim
Choncho anatuma munthu kukamutenga ndipo anabwera naye. Iye anali wofiirira, wa maonekedwe abwino ochititsa kaso. Ndipo Yehova anati, “Mudzoze popeza ndi ameneyu.”
13 tulit igitur Samuhel cornu olei et unxit eum in medio fratrum eius et directus est spiritus Domini in David a die illa et in reliquum surgensque Samuhel abiit in Ramatha
Samueli anatenga botolo la mafuta ndi kumudzoza pamaso pa abale ake, ndipo Mzimu wa Yehova unabwera mwamphamvu pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo. Pambuyo pake Samueli anabwerera ku Rama.
14 spiritus autem Domini recessit a Saul et exagitabat eum spiritus nequam a Domino
Nthawi imeneyo Mzimu wa Yehova unamuchokera Sauli, ndipo mzimu woyipa wochokera kwa Yehova unayamba kumuzunza.
15 dixeruntque servi Saul ad eum ecce spiritus Dei malus exagitat te
Atumiki a Sauli anati, “Taonani mzimu woyipa wochokera kwa Mulungu ukukuzunzani.
16 iubeat dominus noster et servi tui qui coram te sunt quaerant hominem scientem psallere cithara ut quando arripuerit te spiritus Dei malus psallat manu sua et levius feras
Ndiyetu, inu mbuye wathu titumeni ife antchito anu kuti tikafune munthu wodziwa bwino kuyimba zeze. Tsono pamene mzimu woyipa wochokera kwa Mulungu wakufikirani, iye azidzayimba ndipo mudzakhala bwino.”
17 et ait Saul ad servos suos providete mihi aliquem bene psallentem et adducite eum ad me
Choncho Sauli anati kwa atumiki ake, “Chabwino, kandipezereni munthu wodziwa bwino kuyimba ndipo mubwere naye kuno.”
18 et respondens unus de pueris ait ecce vidi filium Isai Bethleemitem scientem psallere et fortissimum robore et virum bellicosum et prudentem in verbis et virum pulchrum et Dominus est cum eo
Mmodzi mwa antchito ake anati, “Ine ndinaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu. Ndiye munthu wodziwa bwino kuyimba, wolimba mtima, ngwazi pa nkhondo, wodziwa kuyankhula ndi wokongola. Ndipotu Yehova ali ndi iye.”
19 misit ergo Saul nuntios ad Isai dicens mitte ad me David filium tuum qui est in pascuis
Ndipo Sauli anatumiza amithenga kwa Yese kukanena kuti, “Nditumizireni mwana wanu Davide, amene amaweta nkhosa.”
20 tulitque Isai asinum plenum panibus et lagoenam vini et hedum de capris unum et misit per manum David filii sui Saul
Choncho Yese anatenga bulu namunyamulitsa buledi, thumba la vinyo ndi mwana wambuzi mmodzi. Zonsezi anamupatsa mwana wake Davide kuti akapereke kwa Sauli.
21 et venit David ad Saul et stetit coram eo at ille dilexit eum nimis et factus est eius armiger
Davide anafika kwa Sauli ndipo anayamba ntchito. Sauli anamukonda kwambiri Davide ndipo anamusandutsa wonyamula zida zake za nkhondo.
22 misitque Saul ad Isai dicens stet David in conspectu meo invenit enim gratiam in oculis meis
Kenaka Sauli anatumiza mawu kwa Yese ndi kuti, “Mulole kuti Davide azinditumikira, pakuti ndamukonda kwambiri.”
23 igitur quandocumque spiritus Dei arripiebat Saul tollebat David citharam et percutiebat manu sua et refocilabatur Saul et levius habebat recedebat enim ab eo spiritus malus
Nthawi zonse mzimu woyipa wochokera kwa Mulungu umati ukamufikira Sauli, Davide ankatenga zeze wake nʼkumamuyimbira. Choncho Sauli ankapeza bwino, ndipo mzimu woyipa uja unkamusiya.

< I Samuelis 16 >