< Marcum 10 >
1 Et exiit inde exurgens venit in fines Iudaeae ultra Iordanem: et conveniunt iterum turbae ad eum: et sicut consueverat, iterum docebat illos.
Ndipo Yesu anachoka pamalowo ndi kupita kudera la Yudeya ndi kutsidya la mtsinje wa Yorodani. Magulu a anthu anabweranso kwa Iye, ndipo monga mwachizolowezi chake anawaphunzitsa.
2 Et accedentes Pharisaei interrogabant eum: Si licet viro uxorem dimittere: tentantes eum.
Afarisi ena anabwera kudzamuyesa pomufunsa kuti, “Kodi malamulo amalola kuti mwamuna asiye mkazi wake?”
3 At ille respondens, dixit eis: Quid vobis praecepit Moyses?
Iye anayankha kuti, “Kodi Mose anakulamulani chiyani?”
4 Qui dixerunt: Moyses permisit libellum repudii scribere, et dimittere.
Iwo anati, “Mose amaloleza mwamuna kulemba kalata ya chisudzulo ndi kumuchotsa mkazi.”
5 Quibus respondens Iesus, ait: Ad duritiam cordis vestri scripsit vobis praeceptum istud.
Yesu anayankha kuti, “Mose anakulemberani lamulo ili chifukwa chakuwuma kwa mitima yanu.
6 ab initio autem creaturae masculum, et feminam fecit eos Deus.
Koma pachiyambi cha chilengedwe, Mulungu ‘analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.’
7 Propter hoc relinquet homo patrem suum, et matrem, et adhaerebit ad uxorem suam:
‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake,
8 et erunt duo in carne una. Itaque iam non sunt duo, sed una caro.
ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ Potero sali awirinso, koma mmodzi.
9 Quod ergo Deus coniunxit, homo non separet.
Chifukwa chake chimene Mulungu wachilumikiza pamodzi, munthu wina asachilekanitse.”
10 Et in domo iterum discipuli eius de eodem interrogaverunt eum.
Pamene analinso mʼnyumba, ophunzira anamufunsa Yesu za izi.
11 Et ait illis: Quicumque dimiserit uxorem suam, et aliam duxerit, adulterium committit super eam.
Iye anayankha kuti, “Aliyense amene aleka mkazi wake ndi kukakwatira wina achita chigololo kulakwira mkaziyo.
12 Et si uxor dimiserit virum suum, et alii nupserit, moechatur.
Ndipo akasiya mwamuna wake ndi kukakwatiwa ndi wina, achita chigololo.”
13 Et offerebant illi parvulos ut tangeret illos. Discipuli autem comminabantur offerentibus.
Anthu anabweretsa ana kwa Yesu kuti awadalitse, koma ophunzira anawadzudzula.
14 Quos cum videret Iesus, indigne tulit, et ait illis: Sinite parvulos venire ad me, et ne prohibueritis eos: talium enim est regnum Dei.
Pamene Yesu anaona zimenezi anayipidwa. Anati kwa iwo, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse, pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa onga awa.
15 Amen dico vobis: Quisquis non receperit regnum Dei velut parvulus, non intrabit in illud.
Ndikukuwuzani choonadi, aliyense amene sadzalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana sadzalowamo.”
16 Et complexans eos, et imponens manus super illos, benedicebat eos.
Ndipo ananyamula ana mʼmanja ake, ndi kuyika manja ake pa iwo nawadalitsa.
17 Et cum egressus esset in via, procurrens quidam genu flexo ante eum, rogabat eum dicens: Magister bone, quid faciam ut vitam aeternam percipiam? (aiōnios )
Yesu atanyamuka, munthu wina anamuthamangira nagwa mogwada pamaso pake. Iye anafunsa kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?” (aiōnios )
18 Iesus autem dixit ei: Quid me dicis bonum: Nemo bonus, nisi unus Deus.
Yesu anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani ukunditchula wabwino? Palibe wabwino koma Mulungu yekha.
19 Praecepta nosti: Ne adulteres, Ne occidas, Ne fureris, Ne falsum testimonium dixeris, Ne fraudum feceris, Honora patrem tuum et matrem.
Iwe umadziwa malamulo: ‘Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni wonama, usachite chinyengo, lemekeza abambo ndi amayi ako.’”
20 At ille respondens, ait illi: Magister, haec omnia observavi a iuventute mea.
Iye anati, “Aphunzitsi zonsezi ndinazisunga kuyambira ndili mnyamata.”
21 Iesus autem intuitus eum, dilexit eum, et dixit ei: Unum tibi deest: vade, quaecumque habes vende, et da pauperibus, et habebis thesaurum in caelo: et veni, sequere me.
Yesu anamuyangʼana ndi kumukonda nati, “Ukusowa chinthu chimodzi. Pita, kagulitse zonse zimene uli nazo ndipo kapereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ndipo ukabwere ndi kunditsata Ine.”
22 Qui contristatus in verbo, abiit moerens: erat enim habens multas possessiones.
Pa chifukwa ichi nkhope yake inagwa. Anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi chuma chambiri.
23 Et circumspiciens Iesus, ait discipulis suis: Quam difficile qui pecunias habent, in regnum Dei introibunt!
Yesu anayangʼanayangʼana ndipo anati kwa ophunzira ake, “Nʼkovutadi kuti achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu!”
24 Discipuli autem obstupescebant in verbis eius. At Iesus rursus respondens ait illis: Filioli, quam difficile est, confidentes in pecuniis, in regnum Dei introire!
Ophunzira anadabwa ndi mawu ake. Koma Yesu anatinso, “Ananu, nʼkovutadi kulowa mu ufumu wakumwamba!
25 Facilius est, camelum per foramen acus transire, quam divitem intrare in regnum Dei.
Ndi kwapafupi kwa ngamira kuti idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kuti alowe mu ufumu wa Mulungu.”
26 Qui magis admirabantur, dicentes ad semetipsos: Et quis potest salvus fieri?
Ophunzira anadabwa kwambiri, ndipo anati kwa wina ndi mnzake, “Nanga ndani amene angapulumuke?”
27 Et intuens illos Iesus, ait: Apud homines impossibile est, sed non apud Deum: omnia enim possibilia sunt apud Deum.
Yesu anawayangʼana ndipo anati, “Kwa munthu zimenezi nʼzosatheka, koma osati ndi Mulungu; zinthu zonse zimatheka ndi Mulungu.”
28 Et coepit ei Petrus dicere: Ecce nos dimisimus omnia, et secuti sumus te.
Petro anati kwa Iye, “Ife tasiya zonse ndi kukutsatani!”
29 Respondens Iesus, ait: Amen dico vobis: Nemo est, qui reliquerit domum, aut fratres, aut sorores, aut patrem, aut matrem, aut filios, aut agros propter me, et propter Evangelium,
Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe aliyense amene wasiya nyumba kapena abale kapena alongo kapena amayi kapena abambo kapena ana kapena minda chifukwa cha Ine ndi Uthenga Wabwino
30 qui non accipiat centies tantum, nunc in tempore hoc: domos, et fratres, et sorores, et matres, et filios, et agros, cum persecutionibus, et in saeculo futuro vitam aeternam. (aiōn , aiōnios )
adzalephera kulandira 100 (nyumba, abale, alongo, amayi, ana ndi minda, pamodzi ndi mazunzo) mʼbado uno ndi moyo wosatha nthawi ya mʼtsogolo. (aiōn , aiōnios )
31 Multi autem erunt primi novissimi, et novissimi primi.
Koma ambiri amene ndi woyambirira adzakhala omalizira, ndipo omalizira adzakhala oyambirira.”
32 Erant autem in via ascendentes Ierosolymam: et praecedebat illos Iesus, et stupebant: et sequentes timebant. Et assumens iterum duodecim, coepit illis dicere quae essent ei eventura.
Ali pa ulendo wawo wopita ku Yerusalemu, Yesu ali patsogolo, ophunzira ake anadabwa, ndipo amene amamutsatira amachita mantha. Anatenganso ophunzira ake khumi ndi awiri pa mbali ndipo anawawuza zimene zikamuchitikire Iye.
33 Quia ecce ascendimus Ierosolymam, et Filius hominis tradetur principibus sacerdotum, et Scribis, et senioribus, et damnabunt eum morte, et tradent eum gentibus:
Iye anati, “Ife tikupita ku Yerusalemu ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Adzamuweruza kuti aphedwe ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina,
34 et illudent ei, et conspuent eum, et flagellabunt eum, et interficient eum: et tertia die resurget.
amene adzamuchita chipongwe ndi kumuthira malovu, kumukwapula ndi kumupha. Patatha masiku atatu adzauka.”
35 Et accedunt ad eum Iacobus, et Ioannes filii Zebedaei, dicentes: Magister, volumus ut quodcumque petierimus, facias nobis.
Ndipo Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anabwera kwa Iye ndipo anati, “Aphunzitsi, tikufuna kuti mutichitire ife chilichonse chimene tipemphe.”
36 At ille dixit eis: Quid vultis ut faciam vobis?
Iye anafunsa kuti, “Kodi mukufuna ndikuchitireni chiyani?”
37 Et dixerunt: Da nobis ut unus ad dexteram tuam, et alius ad sinistram tuam sedeamus in gloria tua.
Iwo anayankha kuti, “Timafuna kuti mmodzi wa ife adzakhale kumanja ndi wina kumanzere mu ulemerero wanu.”
38 Iesus autem ait eis: Nescitis quid petatis: potestis bibere calicem, quem ego bibo: aut baptismo, quo ego baptizor, baptizari?
Yesu anati, “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungamwere chikho chimene ndidzamwera kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndibatizidwe nawo?”
39 At illi dixerunt ei: Possumus. Iesus autem ait eis: Calicem quidem, quem ego bibo, bibetis; et baptismo, quo ego baptizor, baptizabimini:
Iwo anayankha kuti, “Tikhoza.” Yesu anawawuza kuti, “Mudzamweradi chikho chimene Ine ndidzamwera, ndi kubatizidwa ndi ubatizo umene Ine ndidzabatizidwe nawo,
40 sedere autem ad dexteram meam, vel ad sinistram, non est meum dare vobis, sed quibus paratum est.
koma kukhala kumanja kapena kumanzere si Ine wopereka. Malo awa ndi a amene anasankhidwiratu.”
41 Et audientes decem indignati sunt de Iacobo, et Ioanne.
Ophunzira khumiwo otsalawo atamva izi anapsera mtima Yakobo ndi Yohane.
42 Iesus autem vocans eos, ait illis: Scitis quia hi, qui videntur principari gentibus, dominantur eis: et principes eorum potestatem habent ipsorum.
Yesu anawayitana pamodzi nati, “Inu mukudziwa kuti iwo amene amadziyesa ngati atsogoleri a anthu amitundu ina amadyera anthu awo masuku pamutu. Akuluakulu awonso amaonetsadi mphamvu zawo pa iwo.
43 Non ita est autem in vobis, sed quicumque voluerit fieri maior, erit vester minister:
Sizili choncho ndi inu. Mʼmalo mwake, amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala wotumikira,
44 et quicumque voluerit in vobis primus esse, erit omnium servus.
ndipo aliyense amene akufuna kukhala wamkulu akhale kapolo wa onse.
45 Nam et Filius hominis non venit ut ministraretur ei, sed ut ministraret, et daret animam suam redemptionem pro multis.
Pakuti ngakhale Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kuti ukhale dipo la anthu ambiri.”
46 Et veniunt Iericho: et proficiscente eo de Iericho, et discipulis eius, et plurima multitudine, filius Timaei Bartimaeus caecus, sedebat iuxta viam mendicans.
Ndipo anafika ku Yeriko. Pamene Yesu ndi ophunzira ake, pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu, ankatuluka mu mzinda, munthu wosaona, Bartumeyu (mwana wa Tumeyu), amakhala mʼmbali mwa msewu ali kupempha.
47 Qui cum audisset quia Iesus Nazarenus est, coepit clamare, et dicere: Iesu fili David, miserere mei.
Pamene anamva kuti anali Yesu wa ku Nazareti, anayamba kufuwula kuti, “Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”
48 Et comminabantur ei multi ut taceret. At ille multo magis clamabat: Fili David miserere mei.
Ambiri anamukalipira ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulitsabe kuti, “Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”
49 Et stans Iesus praecepit illum vocari. Et vocant caecum dicentes ei: Animaequior esto: surge, vocat te.
Yesu anayima nati, “Muyitaneni.” Ndipo anamuyitana kuti, “Kondwera! Imirira! Akukuyitana.”
50 Qui proiecto vestimento suo exiliens, venit ad eum.
Anaponya mkanjo wake kumbali, analumpha nabwera kwa Yesu.
51 Et respondens Iesus dixit illi: Quid tibi vis faciam? Caecus autem dixit ei: Rabboni, ut videam.
Yesu anamufunsa kuti, “Ukufuna ndikuchitire chiyani?” Wosaonayo anayankha kuti, “Aphunzitsi, ndikufuna ndione.”
52 Iesus autem ait illi: Vade, fides tua te salvum fecit. Et confestim vidit, et sequebatur eum in via.
Yesu anati, “Pita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa!” Nthawi yomweyo anapenya, nʼkumatsatira Yesu pa ulendowo.