< Iohannem 9 >

1 Et praeteriens Iesus vidit hominem caecum a nativitate:
Iye akuyendabe, anaona munthu wosaona chibadwire.
2 et interrogaverunt eum discipuli eius: Rabbi, quis peccavit, hic, aut parentes eius, ut caecus nasceretur?
Ophunzira ake anamufunsa Iye kuti, “Rabi anachimwa ndani, munthuyu kapena makolo ake, kuti iye abadwe wosaona?”
3 Respondit Iesus: Neque hic peccavit, neque parentes eius: sed ut manifestentur opera Dei in illo.
Yesu anayankha kuti, “Sikuti iyeyu anachimwa kapena makolo ake, koma izi zinachitika kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iyeyu.
4 Me oportet operari opera eius, qui misit me, donec dies est: venit nox, quando nemo potest operari.
Ife tiyenera kugwira ntchito za Iye amene anandituma kukanali masana. Usiku ukubwera, pamene wina aliyense sadzagwira ntchito.
5 quamdiu sum in mundo, lux sum mundi.
Pamene Ine ndili mʼdziko lapansi, Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi.”
6 Haec cum dixisset, expuit in terram, et fecit lutum ex sputo, et linivit lutum super oculos eius,
Atanena izi, Iye anathira malovu pansi ndi kukanda dothi, napaka matopewo mʼmaso a munthuyo.
7 et dixit ei: Vade et lava in natatoria Siloe (quod interpretatur Missus.) Abiit ergo, et lavit, et venit videns.
Yesu anamuwuza iye kuti, “Pita kasambe mʼdziwe la Siloamu” (mawu awa akutanthauza Wotumidwa). Choncho munthuyo anapita ndi kukasamba ndipo anabwerako akupenya.
8 Itaque vicini, et qui viderant eum prius quia mendicus erat, dicebant: Nonne hic est, qui sedebat, et mendicabat? Alii dicebant: Quia hic est.
Anzake ndi iwo amene anamuona iye poyamba akupempha anafunsa kuti, “Kodi uyu si munthu amene amapemphapempha uja?”
9 Alii autem: Nequaquam, sed similis est ei. Ille vero dicebat: Quia ego sum.
Ena ananena kuti anali yemweyo. Ena anati, “Ayi, sakuoneka ngati yemweyo.” Koma iye mwini ananenetsa kuti, “Munthuyo ndine.”
10 Dicebant ergo ei: Quomodo aperti sunt tibi oculi?
Iwo anafunsitsa kuti, “Kodi nanga maso ako anatsekuka bwanji?”
11 Respondit: Ille homo, qui dicitur Iesus, lutum fecit: et unxit oculos meos, et dixit mihi: Vade ad natatoria Siloe, et lava. Et abii, et lavi, et video.
Iye anayankha kuti, “Munthu wina wotchedwa Yesu anakanda dothi ndi kupaka mʼmaso anga. Iye anandiwuza kuti ndipite ku Siloamu ndi kukasamba. Choncho ndinapita kukasamba, ndipo ndikuona.”
12 Et dixerunt ei: Ubi est ille? Ait: Nescio.
Iwo anamufunsa iye kuti, “Ali kuti munthu ameneyu?” Iye anati, “Ine sindikudziwa.”
13 Adducunt eum ad Pharisaeos, qui caecus fuerat.
Iwo anabwera naye munthu amene poyamba anali wosaona kwa Afarisi.
14 Erat autem sabbatum quando lutum fecit Iesus, et aperuit oculos eius.
Tsono linali la Sabata tsiku limene Yesu anakanda dothi ndi kutsekula maso a munthuyu.
15 Iterum ergo interrogabant eum Pharisaei quomodo vidisset. Ille autem dixit eis: Lutum mihi posuit super oculos, et lavi, et video.
Choncho Afarisi anamufunsanso iye momwe analandirira kuona kwake. Munthuyo anayankha kuti, “Iye anapaka matope mʼmaso anga, ndipo ine ndinakasamba, ndipo ndikuona.”
16 Dicebant ergo ex Pharisaeis quidam: Non est hic homo a Deo, qui sabbatum non custodit. Alii autem dicebant: Quomodo potest homo peccator haec signa facere? Et schisma erat inter eos.
Ena a Afarisi anati, “Munthu uyu siwochokera kwa Mulungu, pakuti sasunga Sabata.” Koma enanso anafunsa kuti, “Kodi munthu wochimwa angachite bwanji zizindikiro zodabwitsa ngati izi?” Choncho iwo anagawanika.
17 Dicunt ergo caeco iterum: Tu quid dicis de illo, qui aperuit oculos tuos? Ille autem dixit: Quia propheta est.
Pomaliza iwo anatembenukiranso kwa munthu amene anali wosaona uja nati, “Kodi iwe unena chiyani za Iye poti ndi maso ako amene watsekula?” Munthuyo anayankha kuti, “Iye ndi mneneri.”
18 Non crediderunt ergo Iudaei de illo, quia caecus fuisset et vidisset, donec vocaverunt parentes eius, qui viderat:
Ayuda sanakhulupirirebe kuti iye anali wosaona ndi kuti anayamba kuona kufikira atayitana makolo ake.
19 et interrogaverunt eos, dicentes: Hic est filius vester, quem vos dicitis quia caecus natus est? Quomodo ergo nunc videt?
Iwo anafunsa kuti, “Kodi uyu ndi mwana wanu? Kodi iyeyu ndi amene mukunena kuti anabadwa wosaona? Nanga zikutheka bwanji kuti akuona?”
20 Responderunt eis parentes eius, et dixerunt: Scimus quia hic est filius noster, et quia caecus natus est:
Makolo anayankha kuti, “Ife tikudziwa kuti ndi mwana wathu, ndipo tikudziwa kuti anabadwa wosaona.
21 quomodo autem nunc videat, nescimus: aut quis eius aperuit oculos, nos nescimus: ipsum interrogate: aetatem habet, ipse de se loquatur.
Koma sitidziwa zimene zachitika kuti tsopano azipenya. Amenenso wamupenyetsa sitikumudziwa. Mufunseni ndi wamkulu; iye adziyankhira yekha.”
22 Haec dixerunt parentes eius, quoniam timebant Iudaeos: iam enim conspiraverunt Iudaei, ut si quis eum confiteretur esse Christum, extra synagogam fieret.
Makolo ake ananena izi chifukwa amaopa Ayuda, popeza Ayuda anatsimikiza kale kuti aliyense amene adzamuvomereza Yesu kuti anali Khristu adzatulutsidwa mʼsunagoge.
23 Propterea parentes eius dixerunt: Quia aetatem habet, ipsum interrogate.
Ichi ndi chifukwa chake makolo ake anati, “Mufunseni iye ndi wamkulu.”
24 Vocaverunt ergo rursum hominem, qui fuerat caecus, et dixerunt ei: Da gloriam Deo. nos scimus quia hic homo peccator est.
Iwo anamuyitanitsa kachiwiri munthu amene anali wosaonayo. Iwo anati, “Lemekeza Mulungu. Ife tikudziwa kuti munthu uyu ndi wochimwa.”
25 Dixit ergo eis ille: Si peccator est, nescio: unum scio, quia caecus cum essem, modo video.
Iye anayankha kuti, “Zakuti Iye ndi wochimwa kapena ayi, ine sindikudziwa. Ine ndikudziwa chinthu chimodzi. Ndinali wosaona koma tsopano ndikuona!”
26 Dixerunt ergo illi: Quid fecit tibi? quomodo aperuit tibi oculos?
Kenaka anamufunsa kuti, “Kodi Iye anachita chiyani kwa iwe? Iye anatsekula motani maso ako?”
27 Respondit eis: Dixi vobis iam, et audistis: quod iterum vultis audire? numquid et vos vultis discipuli eius fieri?
Iye anayankha kuti, “Ine ndakuwuzani kale ndipo inu simunamvetsetse. Chifukwa chiyani mukufuna mumvenso? Mukufuna kuti inu mukhale ophunzira akenso?”
28 Maledixerunt ergo ei, et dixerunt: Tu discipulus illius sis: nos autem Moysi discipuli sumus.
Pamenepo anamunyoza ndipo anati, “Iwe ndiye ophunzira wa munthuyu! Ife ndife ophunzira a Mose!
29 Nos scimus quia Moysi locutus est Deus: hunc autem nescimus unde sit.
Ife tikudziwa kuti Mulungu anayankhula kwa Mose, koma za munthu uyu, ife sitikudziwa ngakhale kumene akuchokera.”
30 Respondit ille homo, et dixit eis: In hoc enim mirabile est quia vos nescitis unde sit, et aperuit meos oculos:
Munthuyo anayankha kuti, “Tsopano izi ndi zodabwitsa! Inu simukudziwa kumene akuchokera, komabe iye watsekula maso anga.
31 scimus autem quia peccatores Deus non audit: sed si quis Dei cultor est, et voluntatem eius facit, hunc exaudit.
Ife tikudziwa kuti Mulungu samvera wochimwa. Iye amamvera munthu woopa Mulungu amene amachita chifuniro chake.
32 A saeculo non est auditum quia quis aperuit oculos caeci nati. (aiōn g165)
Palibe amene anamvapo za kutsekula maso a munthu wobadwa wosaona. (aiōn g165)
33 Nisi esset hic a Deo, non poterat facere quidquam.
Ngati munthu uyu akanakhala wosachokera kwa Mulungu, palibe chimene Iye akanachita.”
34 Responderunt, et dixerunt ei: In peccatis natus es totus, et tu doces nos? Et eiecerunt eum foras.
Pamenepo anayankha kuti, “Iwe unabadwa mu uchimo kotheratu; bwanji ukuyesa kutiphunzitsa ife!” Ndipo anamutulutsa kunja.
35 Audivit Iesus quia eiecerunt eum foras: et cum invenisset eum, dixit ei: Tu credis in Filium Dei?
Yesu anamva kuti anamutulutsa kunja ndipo pamene anamupeza anati, “Kodi ukukhulupirira Mwana wa Munthu?”
36 Respondit ille, et dixit: Quis est, Domine, ut credam in eum?
Munthuyo anafunsa kuti, “Kodi, Ambuye, ameneyo ndi ndani? Ndiwuzeni kuti ndimukhulupirire Iye?”
37 Et dixit ei Iesus: Et vidisti eum, et qui loquitur tecum, ipse est.
Yesu anati, “Iwe wamuona tsopano. Zoonadi ndiye amene akuyankhula nawe.”
38 At ille ait: Credo Domine. Et procidens adoravit eum.
Pamenepo munthuyo anati, “Ambuye, ndikukhulupirira,” ndipo anamulambira Iye.
39 Et dixit ei Iesus: In iudicium ego in hunc mundum veni: ut qui non vident videant, et qui vident caeci fiant.
Yesu anati, “Ndinabwera pansi pano kudzaweruza kuti osaona aone ndi openya asaone.”
40 Et audierunt quidam ex Pharisaeis, qui cum ipso erant, et dixerunt ei: Numquid et nos caeci sumus?
Afarisi ena amene anali pafupi naye anamva akunena izi ndipo anafunsa kuti, “Chiyani? Kodi ndife osaonanso?”
41 Dixit eis Iesus: Si caeci essetis, non haberetis peccatum. nunc vero dicitis: Quia videmus. Peccatum vestrum manet.
Yesu anati, “Mukanakhala osaona, simukanachimwa; koma tsopano popeza mukuti mumaona, ndinu ochimwabe.”

< Iohannem 9 >