< Isaiæ 17 >
1 Onus Damasci. Ecce Damascus desinet esse civitas, et erit sicut acervus lapidum in ruina.
Uthenga wonena za Damasiko: “Taonani, mzinda wa Damasiko sudzakhalanso mzinda, koma udzasanduka bwinja.
2 Derelictae civitates Aroer gregibus erunt, et requiescent ibi, et non erit qui exterreat.
Mizinda ya Aroeri idzakhala yopanda anthu ndipo idzakhala ya ziweto, zimene zidzagona pansi popanda wina woziopseza.
3 Et cessabit adiutorium ab Ephraim, et regnum a Damasco: et reliquiae Syriae sicut gloria filiorum Israel erunt: dicit Dominus exercituum.
Ku Efereimu sikudzakhalanso linga, ndipo ku Damasiko sikudzakhalanso ufumu; Otsalira a ku Siriya adzachotsedwa ulemu monga anthu a ku Israeli,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
4 Et erit in die illa: attenuabitur gloria Iacob, et pinguedo carnis eius marcescet.
“Tsiku limenelo ulemerero wa Yakobo udzazimirira; ndipo chuma chake chidzasanduka umphawi.
5 Et erit sicut congregans in messe quod restiterit, et brachium eius spicas leget: et erit sicut quaerens spicas in valle Raphaim.
Israeli adzakhala ngati munda wa tirigu umene anatsiriza kukolola. Adzakhalanso ngati munda wa mʼchigwa cha Refaimu anthu atatha kukunkha ngala za tirigu.
6 Et relinquetur in eo sicut racemus, et sicut excussio oleae duarum vel trium olivarum in summitate rami, sive quattuor aut quinque in cacuminibus eius fructus eius: dicit Dominus Deus Israel.
Komabe Aisraeli ochepa okha ndiwo ati adzatsale monga mʼmene zimatsalira zipatso ziwiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipeni kapena zipatso zisanu pa nthambi za mʼmunsi mwa mtengo wa olivi akawugwedeza,” akutero Yehova, Mulungu wa Israeli.
7 In die illa inclinabitur homo ad Factorem suum, et oculi eius ad sanctum Israel respicient:
Tsiku limenelo anthu adzayangʼana Mlengi wawo ndipo adzatembenukira kwa Woyerayo wa Israeli.
8 et non inclinabitur ad altaria, quae fecerunt manus eius: et quae operati sunt digiti eius non respiciet, lucos et delubra.
Iwo sadzakhulupiriranso maguwa ansembe, ntchito ya manja awo, ndipo sadzadaliranso mitengo ya mafano a Asera, ndiponso maguwa ofukizirapo lubani amene manja awo anapanga.
9 In die illa erunt civitates fortitudinis eius derelictae sicut aratra, et segetes quae derelictae sunt a facie filiorum Israel, et eris deserta.
Tsiku limenelo mizinda yawo yamphamvu, imene anasiya chifukwa cha Aisraeli, idzakhala ngati malo osiyidwa kuti awirire ndi kumera ziyangoyango. Ndipo yonse idzakhala mabwinja.
10 Quia oblitus es Dei salvatoris tui, et fortis adiutoris tui non es recordata: propterea plantabis plantationem infidelem, et germen alienum seminabis.
Inu mwayiwalatu Mulungu Mpulumutsi wanu; simunakumbukire Thanthwe, linga lanu. Choncho, ngakhale munadzala mbewu zabwino, ndi kuyitanitsa kunja mitengo ya mpesa,
11 In die plantationis tuae labrusca, et mane semen tuum florebit: ablata est messis in die hereditatis, et dolebit graviter.
nimuyembekeza kuti zikule tsiku lomwelo ndi kuphukira maluwa mmawa mwake, komabe zimenezi sizidzakupindulirani pa tsiku la mavuto.
12 Vae multitudini populorum multorum, ut multitudo maris sonantis: et tumultus turbarum, sicut sonitus aquarum multarum.
Aa, mkokomo wa anthu a mitundu yambiri, akusokosa ngati kukokoma kwa nyanja! Aa, phokoso la anthu a mitundu ina, akusokosa ngati mkokomo wa madzi amphamvu!
13 Sonabunt populi sicut sonitus aquarum inundantium, et increpabit eum, et fugiet procul: et rapietur sicut pulvis montium a facie venti, et sicut turbo coram tempestate.
Ngakhale ankhondo a mitundu ina akubwera ndi mkokomo ngati wa madzi ambiri, koma adzathawira kutali Mulungu akadzawadzudzula. Yehova adzawapirikitsa ngati mankhusu owuluka ndi mphepo pa phiri, ndi ngati fumbi la kamvuluvulu asanayambe.
14 In tempore vespere, et ecce turbatio: in matutino, et non subsistet. haec est pars eorum, qui vastaverunt nos, et sors diripientium nos.
Pofika nthawi yamadzulo zoopsa zidzayamba kuchitika, ndipo zidzakhala zitatha pofika mmawa. Izi ndizo zidzachitikire anthu otilanda zinthu, gawo la amene amatibera zinthu zathu.