< Deuteronomii 19 >

1 Cum disperdiderit Dominus Deus tuus gentes, quarum tibi traditurus est terram, et possederis eam, habitaverisque in urbibus eius et in aedibus:
Yehova Mulungu wanu akadzawononga anthu amene dziko lawo akukupatsani, ndipo inu mukawapirikitsa ndi kukhazikika mʼmizinda ndi mʼnyumba zawo,
2 tres civitates separabis tibi in medio Terrae, quam Dominus Deus tuus dabit tibi in possessionem,
mukapatule mizinda itatu imene ili pakati pa dziko lomwe Yehova Mulungu akukupatsani kukhala lanu.
3 sternens diligenter viam: et in tres aequaliter partes totam Terrae tuae provinciam divides: ut habeat e vicino qui propter homicidium profugus est, quo possit evadere.
Mudzakonze misewu ndi kuligawa patatu dzikolo limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, kuti aliyense wopha munthu akhoza kuthawirako.
4 Haec erit lex homicidae fugientis, cuius vita servanda est: Qui percusserit proximum suum nesciens, et qui heri et nudiustertius nullum contra eum odium habuisse comprobatur:
Ili ndi lamulo lokhudza munthu amene wapha mnzake mosazindikira osati mwadala, nathawira kumeneko kupulumutsa moyo wake. Ndi munthu amene wapha mnzake mosazindikira, popanda maganizo oyipa.
5 sed abiisse cum eo simpliciter in silvam ad ligna caedenda, et in succisione lignorum securis fugerit manu, ferrumque lapsum de manubrio amicum eius percusserit, et occiderit: hic ad unam supradictarum urbium confugiet, et vivet:
Mwachitsanzo, munthu atapita ku nkhalango ndi mnzake kukadula mitengo, ndiye posamula nkhwangwa kuti adule mtengo, nkhwangwa ikhoza kuguluka nʼkukagwera mnzake uja nʼkumupha. Munthu ameneyo akhoza kuthawira ku umodzi mwa mizindayo napulumutsa moyo wake.
6 ne forsitan proximus eius, cuius effusus est sanguis, dolore stimulatus, persequatur, et apprehendat eum si longior via fuerit, et percutiat animam eius, qui non est reus mortis: quia nullum contra eum, qui occisus est, odium prius habuisse monstratur.
Kupanda kutero ndiye kuti wolipsira akhoza kumuthamangitsa mwaukali ndi kumugwira ngati mtunda utalika, ndipo akhoza kumupha ngakhale kuti sanayenera kufa popeza sanaphe mnzake mwadala.
7 Idcirco praecipio tibi, ut tres civitates aequalis inter se spatii dividas.
Ichi ndi chifukwa chake ndikukulamulani kuti mudzipatulire nokha mizinda itatu.
8 Cum autem dilataverit Dominus Deus tuus terminos tuos, sicut iuravit patribus tuis, et dederit tibi cunctam Terram, quam eis pollicitus est
Ngati Yehova Mulungu wanu akulitsa malire anu monga analonjezera pa malumbiro ndi makolo anu, nakupatsani dziko lonse monga analonjezera,
9 (si tamen custodieris mandata eius, et feceris quae hodie praecipio tibi, ut diligas Dominum Deum tuum, et ambules in viis eius omni tempore) addes tibi tres alias civitates, et supradictarum trium urbium numerum duplicabis:
chifukwa chotsatira bwino malamulo onse amene ndikukuwuzani lero, kukonda Yehova Mulungu wanu ndi kuyenda mʼnjira zake nthawi zonse, ndiye kuti mukuyenera kupatula mizinda itatu yowonjezera.
10 ut non effundatur sanguis innoxius in medio Terrae, quam Dominus Deus tuus dabit tibi possidendam, ne sis sanguinis reus.
Muchite zimenezi kuti musakhetse magazi wosalakwa mʼdziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa, ndipo kuti musapezeke ndi mlandu wokhetsa magazi.
11 Si quis autem odio habens proximum suum, insidiatus fuerit vitae eius, surgensque percusserit illum, et mortuus fuerit, fugeritque ad unam de supradictis urbibus,
Koma ngati munthu adana ndi mnzake namubisalira panjira nʼkumuvulaza mpaka kumupha, nathawira ku umodzi mwa mizindayi,
12 mittent seniores civitatis illius, et arripient eum de loco effugii, tradentque in manu proximi, cuius sanguis effusus est, et morietur.
akuluakulu a mu mzinda wake akamugwire ndi kumubwezera ku mzinda wake namupereka kwa wolipsira kuti aphedwe.
13 Non miseraberis eius, et auferes innoxium sanguinem de Israel, ut bene sit tibi.
Osamumvera chisoni. Muyenera kuchotsa tchimo lokhetsa magazi wosalakwa mu Israeli kuti zinthu zizikuyenderani bwino.
14 Non assumes, et transferes terminos proximi tui, quos fixerunt priores in possessione tua, quam Dominus Deus tuus dabit tibi in Terra, quam acceperis possidendam.
Musamasunthe mwala wa malire anu ndi mnzanu amene anayikidwa ndi makolo anu pa cholowa chimene mulandire mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
15 Non stabit testis unus contra aliquem, quidquid illud peccati, et facinoris fuerit: sed in ore duorum aut trium testium stabit omne verbum.
Mboni imodzi siyokwanira kupeza munthu kuti ndi wolakwa pa mlandu uliwonse umene wapalamula. Nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.
16 Si steterit testis mendax contra hominem, accusans eum praevaricationis,
Ngati mboni yonama ifuna kunamizira munthu mlandu,
17 stabunt ambo, quorum causa est, ante Dominum in conspectu sacerdotum et iudicum qui fuerint in diebus illis.
anthu awiri okhudzidwa ndi mlanduwo ayenera kuyima pamaso pa Yehova pali ansembe ndi oweruza amene ali pa ntchito pa nthawiyo.
18 Cumque diligentissime perscrutantes, invenerint falsum testem dixisse contra fratrem suum mendacium:
Oweruza afufuze bwinobwino, ndipo ngati zatsimikizika kuti mboniyo ndi yabodza, yopereka umboni wonama pa mʼbale wake,
19 reddent ei sicut fratri suo facere cogitavit, et auferes malum de medio tui:
ndiye kuti amuchitire iyeyo zimene anafuna kuchitira mʼbale wakezo. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu.
20 ut audientes ceteri timorem habeant, et nequaquam talia audeant facere.
Anthu ena onse adzamva zimenezi nachita mantha, ndipo choyipa choterechi sichidzachitikanso pakati panu.
21 Non misereberis eius, sed animam pro anima, oculum pro oculo, dentem pro dente, manum pro manu, pedem pro pede exiges.
Osachita chisoni, moyo uzilipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja ndi phazi kulipira phazi.

< Deuteronomii 19 >