< I Samuelis 9 >

1 Et erat vir de Beniamin nomine Cis, filius Abiel, filii Seor, filii Bechorath, filii Aphia, filii viri Iemini, fortis robore.
Panali munthu wina wa fuko la Benjamini, wotchuka, dzina lake Kisi, mwana wa Abieli, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya.
2 Et erat ei filius vocabulo Saul, electus et bonus: et non erat vir de filiis Israel melior illo. ab humero et sursum eminebat super omnem populum.
Iyeyu anali ndi mwana dzina lake Sauli, mnyamata wa maonekedwe abwino. Pakati pa Aisraeli onse panalibe wofanana naye. Anali wamtali kotero kuti anthu onse ankamulekeza mʼmapewa.
3 Perierant autem asinae Cis patris Saul: et dixit Cis ad Saul filium suum: Tolle tecum unum de pueris, et consurgens vade, et quaere asinas. Qui cum transissent per montem Ephraim,
Tsono abulu a Kisi, abambo ake a Sauli anasowa. Choncho Kisi anati kwa mwana wake Sauli, “Tenga wantchito mmodzi ndipo mupite mukafunefune abuluwo.”
4 et per terram Salisa, et non invenissent, transierunt etiam per Terram Salim, et non erant: sed et per Terram Iemini, et minime repererunt.
Choncho iwo anadutsa dziko la mapiri a Efereimu ndi dera la Salisa, koma sanawapeze. Anadutsa ku Saalimu koma abuluwo sanawapeze. Kenaka anadutsa dziko la Benjamini, koma osawapezabe.
5 Cum autem venissent in Terram Suph, dixit Saul ad puerum, qui erat cum eo: Veni et revertamur, ne forte dimiserit pater meus asinas, et solicitus sit pro nobis.
Atafika ku dera la Zufi, Sauli anawuza mnyamata wake kuti, “Tiye tibwerere, mwina abambo anga angasiye kudandaula za abulu ndipo adzayamba kudandaula za ife.”
6 Qui ait ei: Ecce vir Dei est in civitate hac, vir nobilis: omne, quod loquitur, sine ambiguitate venit. nunc ergo eamus illuc, si forte indicet nobis de via nostra, propter quam venimus.
Koma mnyamatayo anayankha kuti, “Taonani, mu mzinda uwo muli munthu wa Mulungu. Anthu amamupatsa ulemu kwambiri, ndipo zonse zimene amanena zimachitika. Tiyeni tipite kumeneko tsopano. Mwina adzatiwuza kumene tiyenera kulowera.”
7 Dixitque Saul ad puerum suum: Ecce ibimus: quid feremus ad virum Dei? panis defecit in sitachiis nostris: et sportulam non habemus, ut demus homini Dei, nec quidquam aliud.
Sauli anafunsa mnyamata wake kuti, “Tikapita tikamupatsa chiyani munthuyo pakuti chakudya chimene chinali mʼmatumba mwathu chatha? Tilibe mphatso iliyonse yoti timutengere munthu wa Mulungu. Nanga tili ndi chiyani?”
8 Rursum puer respondit Sauli, et ait: Ecce inventa est in manu mea, quarta pars stateris argenti, demus homini Dei, ut indicet nobis viam nostram.
Mnyamatayo anayankha kuti, “Onani, ndili ndi kandalama kakangʼono ka siliva. Ndikamupatsa munthu wa Mulunguyo ndipo akatidziwitsa kumene kuli abuluwo.”
9 (Olim in Israel sic loquebatur unusquisque vadens consulere Deum: Venite, et eamus ad Videntem. Qui enim Propheta dicitur hodie, vocabatur olim Videns.)
(Kale mu Israeli ngati munthu afuna kukapempha nzeru kwa Mulungu ankanena kuti, “Tiyeni tipite kwa mlosi.” Ndiye kuti munthu amene lero akutchedwa mneneri, kale ankatchedwa mlosi).
10 Et dixit Saul ad puerum suum: Optimus sermo tuus, Veni, eamus. Et ierunt in civitatem, in qua erat vir Dei.
Tsono Sauli anawuza mnyamata wake kuti, “Chabwino, tiye tipite.” Ndipo ananyamuka kupita ku mzinda umene kunali munthu wa Mulunguyo.
11 Cumque ascenderent clivum civitatis, invenerunt puellas egredientes ad hauriendam aquam, et dixerunt eis: Num hic est Videns?
Akukwera phiri kupita ku mzindawo anakumana ndi atsikana akutuluka mu mzindamo kukatunga madzi, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mlosi uja alipo?”
12 Quae respondentes, dixerunt illis: Hic est: ecce ante te, festina nunc: hodie enim venit in civitatem, quia sacrificium est hodie populi in excelso.
Iwo anayankha, “Inde alipo. Ali kutsogolo kwanuku, fulumirani tsopano, wangobwera kumene mu mzinda wathu uno lero, chifukwa lero anthu akupereka nsembe ku phiri.
13 Ingredientes urbem, statim invenietis eum antequam ascendat excelsum ad vescendum. neque enim comesurus est populus donec ille veniat: quia ipse benedicit hostiae, et deinceps comedunt qui vocati sunt. Nunc ergo conscendite, quia hodie reperietis eum.
Mukangolowa mu mzindawo mumupeza asanapite ku phiri kukadya. Anthu sangayambe kudya iye asanabwere chifukwa iyeyu ayenera kudalitsa nsembeyo. Kenaka anthu oyitanidwa adzayamba kudya. Pitani tsopano, chifukwa muyenera kumupeza nthawi ino.”
14 Et ascenderunt in civitatem. Cumque illi ambularent in medio urbis, apparuit Samuel egrediens obviam eis, ut ascenderet in excelsum.
Choncho anapita ku mzinda kuja. Akulowa mu mzindamo, anaona Samueli akutuluka mu mzindamo akubwera kumene kunali iwo, koma amapita ku phiri, ku malo wopatulika.
15 Dominus autem revelaverat auriculam Samuelis ante unam diem quam veniret Saul, dicens:
Koma chadzulo lake Sauli asanafike, Yehova anali atamuwuza kale Samueli za zimenezi kuti,
16 Hac ipsa hora, quae nunc est, cras mittam virum ad te de Terra Beniamin, et unges eum ducem super populum meum Israel: et salvabit populum meum de manu Philisthinorum: quia respexi populum meum, venit enim clamor eorum ad me.
“Mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini. Udzamudzoze kuti akhale mtsogoleri wa anthu anga, Aisraeli. Iye adzawapulumutsa mʼdzanja la Afilisti. Ine ndaona kuzunzika kwawo ndipo ndamva kulira kwawo.”
17 Cumque aspexisset Samuel Saulem, Dominus dixit ei: Ecce, vir, quem dixeram tibi, iste dominabitur populo meo.
Samueli atamuona Sauli, Yehova anamuwuza kuti, “Munthu ndinakuwuza uja ndi uyu. Iyeyu adzalamulira anthu anga.”
18 Accessit autem Saul ad Samuelem in medio portae, et ait: Indica, oro, mihi, ubi est domus Videntis.
Tsono Sauli anayandikira Samueli pa chipata ndipo anamufunsa, “Kodi mungandiwuze kumene kuli nyumba ya mlosi?”
19 Et respondit Samuel Sauli dicens: Ego sum Videns. ascende ante me in excelsum, ut comedatis mecum hodie, et dimittam te mane: et omnia, quae sunt in corde tuo, indicabo tibi.
Samueli anayankha, “Ine ndine mlosiyo. Tsogolani kupita ku phiri pakuti lero mudya ndi ine, ndipo mawa mmawa ndidzakuwuzani zonse zimene zili mu mtima mwanu.
20 Et de asinis, quas nudiustertius perdidisti, ne solicitus sis, quia inventae sunt. Et cuius erunt optima quaeque Israel? nonne tibi et omni domui patris tui?
Musadere nkhawa za abulu anu amene akhala akusowa masiku atatu apitawa, poti apezeka kale. Kodi Aisraeli onse akufunitsitsa ndani? Kodi si ndiwe ndi nyumba yonse ya abambo ako?”
21 Respondens autem Saul, ait: Numquid non filius Iemini ego sum de minima tribu Israel, et cognatio mea novissima inter omnes familias de tribu Beniamin? quare ergo locutus es mihi sermonem istum?
Sauli anayankha, “Inetu ndine Mbenjamini, fuko lalingʼono la mafuko onse a Israeli, ndipo banja langa ndi lalingʼono pakati pa mabanja a fuko la Benjamini. Nanga nʼchifukwa chiyani mukunena zimenezi kwa ine?”
22 Assumens itaque Samuel Saulem, et puerum eius, introduxit eos in triclinium, et dedit eis locum in capite eorum, qui fuerant invitati. erant enim quasi triginta viri.
Ndipo Samueli anatenga Sauli ndi mnyamata wake uja ndi kulowa nawo mʼchipinda chachikulu ndipo anawakhazika kutsogolo kwa anthu oyitanidwa. Onse pamodzi analipo anthu makumi atatu.
23 Dixitque Samuel coco: Da partem, quam dedi tibi, et praecepi ut reponeres seorsum apud te.
Tsono Samueli anati kwa wophika, “Bwera nayo nyama imene ndinakupatsa, imene ndinakuwuza kuti uyisunge pambali.”
24 Levavit autem cocus armum, et posuit ante Saul. Dixitque Samuel: Ecce quod remansit, pone ante te, et comede: quia de industria servatum est tibi, quando populum vocavi. Et comedit Saul cum Samuele in die illa.
Kotero wophikayo anatenga mwendo wa nyama ndipo anawuyika patsogolo pa Sauli. Samueli anati “Nayi nyama imene ndinakusungira kuti pa nthawi yake udye pamodzi ndi anthu amene ndawayitana.” Ndipo Sauli anadya tsiku limenelo ndi Samueli.
25 Et descenderunt de excelso in oppidum, et locutus est cum Saule in solario: stravitque Saul in solario, et dormivit.
Atatsika kuchoka ku phiri kuja, Samueli anamukonzera Sauli malo ogona pa denga la nyumba yake, ndipo Sauli anagona pamenepo.
26 Cumque mane surrexissent, et iam elucesceret, vocavit Samuel Saulem in solario, dicens: Surge, ut dimittam te. Et surrexit Saul: egressique sunt ambo, ipse videlicet, et Samuel.
Tsono mʼbandakucha Samueli anayitana Sauli pa dengapo nati, “Konzeka ndipo ine ndikuperekeza.” Choncho Sauli anadzuka ndipo onse awiri, Samueli ndi Sauli anakalowa mu msewu.
27 Cumque descenderent in extrema parte civitatis, Samuel dixit ad Saul: Dic puero ut antecedat nos, et transeat: tu autem subsiste paulisper, ut indicem tibi verbum Domini.
Atakafika ku mathero a mzindawo, Samueli anati kwa Sauli, “Muwuzeni mnyamata wanu kuti atsogole, koma inuyo muyime pangʼono kuti ndikuwuzeni mawu ochokera kwa Mulungu.”

< I Samuelis 9 >