< Psalmorum 65 >

1 In finem. Psalmus David, canticum Jeremiæ et Ezechielis populo transmigrationis, cum inciperent exire. Te decet hymnus, Deus, in Sion, et tibi reddetur votum in Jerusalem.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Nyimbo. Matamando akudikira Inu Mulungu mu Ziyoni; kwa inu malumbiro athu adzakwaniritsidwa.
2 Exaudi orationem meam; ad te omnis caro veniet.
Inu amene mumamva pemphero, kwa inu anthu onse adzafika.
3 Verba iniquorum prævaluerunt super nos, et impietatibus nostris tu propitiaberis.
Pamene tinathedwa nzeru ndi machimo, Inu munakhululukira mphulupulu zathu.
4 Beatus quem elegisti et assumpsisti: inhabitabit in atriis tuis. Replebimur in bonis domus tuæ; sanctum est templum tuum,
Odala iwo amene inu muwasankha ndi kuwabweretsa pafupi kukhala mʼmabwalo anu! Ife tadzazidwa ndi zinthu zabwino za mʼNyumba mwanu, za mʼNyumba yanu yoyera.
5 mirabile in æquitate. Exaudi nos, Deus, salutaris noster, spes omnium finium terræ, et in mari longe.
Mumatiyankha ife ndi ntchito zodabwitsa zachilungamo, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, chiyembekezo cha mathero onse a dziko lapansi ndi cha nyanja zomwe zili kutali kwambiri,
6 Præparans montes in virtute tua, accinctus potentia;
amene munapanga mapiri ndi mphamvu zanu, mutadziveka nokha ndi mphamvu.
7 qui conturbas profundum maris, sonum fluctuum ejus. Turbabuntur gentes,
Amene munakhalitsa bata nyanja kukokoma kwa mafunde ake, ndi phokoso la anthu a mitundu ina.
8 et timebunt qui habitant terminos a signis tuis; exitus matutini et vespere delectabis.
Iwo amene akukhala kutali amaopa zizindikiro zozizwitsa zanu; kumene dzuwa limatulukira ndi kumene dzuwa limalowera. Inu mumafuna nyimbo zachimwemwe.
9 Visitasti terram, et inebriasti eam; multiplicasti locupletare eam. Flumen Dei repletum est aquis; parasti cibum illorum: quoniam ita est præparatio ejus.
Inu mumasamalira dziko lapansi ndi kulithirira; Inuyo mumalilemeretsa kwambiri. Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi kuti upereke tirigu kwa anthu, pakuti Inu munakhazikitsa zimenezi.
10 Rivos ejus inebria; multiplica genimina ejus: in stillicidiis ejus lætabitur germinans.
Mwadzaza nthaka yake ndi madzi ndi kusalaza migula yake, mwayifewetsa ndi mvula yamawawa ndi kudalitsa mbewu zake.
11 Benedices coronæ anni benignitatis tuæ, et campi tui replebuntur ubertate.
Inu mumaveka chaka ndi zinthu zochuluka, ndipo ngolo zanu zimasefukira ndi zinthu zochuluka.
12 Pinguescent speciosa deserti, et exsultatione colles accingentur.
Malo a udzu a mʼchipululu amasefukira; mapiri avekedwa ndi chisangalalo.
13 Induti sunt arietes ovium, et valles abundabunt frumento; clamabunt, etenim hymnum dicent.
Madambo akutidwa ndi zoweta ndi zigwa zavekedwa ndi tirigu; izo pamodzi zikufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe.

< Psalmorum 65 >