< Nehemiæ 2 >
1 Factum est autem in mense Nisan, anno vigesimo Artaxerxis regis: et vinum erat ante eum, et levavi vinum, et dedi regi: et eram quasi languidus ante faciem ejus.
Pa mwezi wa Nisani, mʼchaka cha makumi awiri cha ufumu wa Aritasasita, atabwera ndi vinyo pamaso pa mfumu ine ndinatenga vinyoyo ndi kupereka kwa mfumu. Koma ndinali ndisanakhalepo ndi nkhope yachisoni pamaso pake.
2 Dixitque mihi rex: Quare vultus tuus tristis est, cum te ægrotum non videam? non est hoc frustra, sed malum nescio quod in corde tuo est. Et timui valde, ac nimis:
Tsono mfumu inandifunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani nkhope yako ikuoneka yachisoni pamene iwe sukudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mu mtima.” Ine ndinachita mantha kwambiri.
3 et dixi regi: Rex, in æternum vive: quare non mœreat vultus meus, quia civitas domus sepulchrorum patris mei deserta est, et portæ ejus combustæ sunt igni?
Ndinawuza mfumu kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wamuyaya! Kodi nkhope yanga ilekerenji kuoneka yachisoni pamene mzinda umene kuli manda a makolo anga, wasanduka bwinja ndipo zipata zake zinawonongedwa ndi moto?”
4 Et ait mihi rex: Pro qua re postulas? Et oravi Deum cæli,
Apo mfumu inandifunsa kuti, “Tsono ukufuna kundipempha chiyani?” Ndipo ine ndinapemphera kwa Mulungu Wakumwamba.
5 et dixi ad regem: Si videtur regi bonum, et si placet servus tuus ante faciem tuam, ut mittas me in Judæam ad civitatem sepulchri patris mei, et ædificabo eam.
Ndipo ndinayankha kuti, “Ngati amfumu chingakukondweretseni, ngati mungakomere mtima mtumiki wanune, mundilole kuti ndipite ku Yuda, ku mzinda kumene kuli manda a makolo anga kuti ndikawumangenso.”
6 Dixitque mihi rex, et regina quæ sedebat juxta eum: Usque ad quod tempus erit iter tuum, et quando reverteris? Et placuit ante vultum regis, et misit me: et constitui ei tempus.
Tsono mfumu, mfumukazi itakhala pambali pake, anandifunsa kuti, “Kodi kumeneko ukakhalako masiku angati ndipo udzabwera liti?” Ndinayiwuza mfumu nthawi yake ndipo inandilola kuti ndipite.
7 Et dixi regi: Si regi videtur bonum, epistolas det mihi ad duces regionis trans flumen, ut traducant me, donec veniam in Judæam:
Ndipo ndinatinso kwa mfumu, “Ngati zikondweretse mfumu, mundipatse makalata oti ndikapereke kwa abwanamkubwa a ku chigawo cha Patsidya pa Yufurate, kuti akandilole kudutsa mwamtendere mpaka nditakafika ku Yuda.
8 et epistolam ad Asaph custodem saltus regis, ut det mihi ligna, ut tegere possim portas turris domus, et muros civitatis, et domum quam ingressus fuero. Et dedit mihi rex juxta manum Dei mei bonam mecum.
Mundipatsenso kalata yokapereka kwa Asafu woyangʼanira nkhalango ya mfumu, kuti akandipatse mitengo yokapangira mitanda ya zipata za nsanja yoteteza Nyumba ya Mulungu, mitanda ya khoma la mzinda ndi ya nyumba yokhalamo ine.” Mfumu indipatse zomwe ndinapempha popeza Yehova wokoma mtima anali nane.
9 Et veni ad duces regionis trans flumen, dedique eis epistolas regis. Miserat autem rex mecum principes militum, et equites.
Choncho ndinanyamuka ulendo wanga ndipo ndinafika kwa abwanamkubwa a chigawo cha Patsidya pa Yufurate ndipo ndinawapatsa makalata a mfumu. Mfumu nʼkuti itatumiza akulu ankhondo ndi okwera pa akavalo kuti atsagane nane.
10 Et audierunt Sanaballat Horonites, et Tobias servus Ammanites: et contristati sunt afflictione magna, quod venisset homo qui quæreret prosperitatem filiorum Israël.
Sanibalati wa ku Horoni ndi Tobiya wa ku Amoni atamva zimenezi, iwo anayipidwa kwambiri kuti wina wabwera kudzachitira zabwino Aisraeli.
11 Et veni Jerusalem, et eram ibi tribus diebus.
Ndinafika ku Yerusalemu, ndipo ndinakhala kumeneko masiku atatu.
12 Et surrexi nocte ego, et viri pauci mecum, et non indicavi cuiquam quid Deus dedisset in corde meo ut facerem in Jerusalem: et jumentum non erat mecum, nisi animal cui sedebam.
Sindinawuze munthu aliyense za zimene Yehova anayika mu mtima mwanga kuti ndichitire mzinda wa Yerusalemu. Choncho ndinanyamuka usiku pamodzi ndi anthu ena owerengeka. Ndinalibe bulu wina aliyense kupatula amene ndinakwerapo.
13 Et egressus sum per portam vallis nocte, et ante fontem draconis, et ad portam stercoris, et considerabam murum Jerusalem dissipatum, et portas ejus consumptas igni.
Ndinatuluka usiku podzera ku Chipata cha ku Chigwa ndi kuyenda kupita ku Chitsime cha Chirombo Chamʼmadzi mpaka ku Chipata cha Zinyalala. Ndinayangʼana makoma a Yerusalemu, amene anagwetsedwa, ndi zipata zake, zimene zinawonongedwa ndi moto.
14 Et transivi ad portam fontis, et ad aquæductum regis, et non erat locus jumento cui sedebam ut transiret.
Kenaka ndinapita ku Chipata cha Kasupe ndi ku Dziwe la Mfumu. Koma panalibe malo okwanira akuti bulu wanga adutse.
15 Et ascendi per torrentem nocte, et considerabam murum, et reversus veni ad portam vallis, et redii.
Kotero usikuwo ndinapita ku chigwa, ndikuyangʼana khomalo. Pomaliza ndinabwerera ndi kukalowanso mu mzinda kudzera ku Chipata cha ku Chigwa.
16 Magistratus autem nesciebant quo abiissem, aut quid ego facerem: sed et Judæis, et sacerdotibus, et optimatibus, et magistratibus, et reliquis qui faciebant opus, usque ad id loci nihil indicaveram.
Akuluakulu sanadziwe kumene ndinapita kapena zimene ndimachita, chifukwa pa nthawiyi nʼkuti ndisananene kalikonse kwa Ayuda kapena ansembe, anthu olemekezeka kapena akuluakulu, kapena wina aliyense amene anali woyenera kugwira ntchitoyi.
17 Et dixi eis: Vos nostis afflictionem in qua sumus: quia Jerusalem deserta est, et portæ ejus consumptæ sunt igni: venite, et ædificemus muros Jerusalem, et non simus ultra opprobrium.
Ndinawawuza kuti, “Inu mukuona mavuto amene tili nawo. Mukuona kuti mzinda wa Yerusalemu wasanduka bwinja ndipo zipata zake zatenthedwa ndi moto. Tsono tiyeni timangenso makoma a Yerusalemu ndipo sitidzachitanso manyazi.”
18 Et indicavi eis manum Dei mei, quod esset bona mecum, et verba regis quæ locutus esset mihi, et aio: Surgamus, et ædificemus. Et confortatæ sunt manus eorum in bono.
Ndinawawuza za mmene Yehova Mulungu wanga anandichitira zabwino ndiponso mawu amene mfumu inandiwuza. Tsono anati, “Tiyeni tiyambenso kumanga.” Kotero analimbitsana mtima kuti ayambenso ntchito yabwinoyi.
19 Audierunt autem Sanaballat Horonites, et Tobias servus Ammanites, et Gosem Arabs, et subsannaverunt nos, et despexerunt, dixeruntque: Quæ est hæc res quam facitis? numquid contra regem vos rebellatis?
Koma Sanibalati wa ku Horoni, Tobiya wa ku Amoni ndi Gesemu Mwarabu atamva zimenezi, anatiseka ndi kutinyoza. Iwo anafunsa kuti, “Kodi muti ndi chiyani chimene mukuchitachi? Kodi mufuna kuwukira mfumu?”
20 Et reddidi eis sermonem, dixique ad eos: Deus cæli ipse nos juvat, et nos servi ejus sumus: surgamus et ædificemus: vobis autem non est pars, et justitia, et memoria in Jerusalem.
Koma ndinawayankha kuti, “Mulungu Wakumwamba atithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino. Ife antchito ake tiyambapo kumanga. Koma inu mulibe gawo lanu muno mu Yerusalemu. Mulibe chokuyenerezani kulandira malo ano. Mulibenso chilichonse muno chokumbutsa za inu.”