< Hiezechielis Prophetæ 21 >

1 Et factus est sermo Domini ad me, dicens:
Yehova anandiyankhula nati:
2 Fili hominis, pone faciem tuam ad Jerusalem, et stilla ad sanctuaria, et propheta contra humum Israël.
“Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyangʼane ku Yerusalemu ndipo ulalike mawu odzudzula malo ake opatulika. Unenere zodzudzula anthu a ku Yerusalemu.
3 Et dices terræ Israël: Hæc dicit Dominus Deus: Ecce ego ad te, et ejiciam gladium meum de vagina sua, et occidam in te justum et impium.
Uwawuze kuti, Ambuye Yehova akuti, ‘Taona, Ine ndidzalimbana nawe. Ndidzasolola lupanga langa mʼchimake ndi kuwononga anthu olungama ndi ochimwa omwe.
4 Pro eo autem quod occidi in te justum et impium, idcirco egredietur gladius meus de vagina sua ad omnem carnem, ab austro usque ad aquilonem:
Motero ndidzapha aliyense kuchokera kummawa mpaka kumpoto.
5 ut sciat omnis caro quia ego Dominus, eduxi gladium meum de vagina sua irrevocabilem.
Pamenepo anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndasolola lupanga langa mʼchimake; sindidzalilowetsanso mʼchimakemo.’
6 Et tu, fili hominis, ingemisce in contritione lumborum, et in amaritudinibus ingemisce coram eis.
“Tsono iwe mwana wa munthu, buwula. Buwula pamaso pawo ndi mtima wosweka ndi wachisoni chachikulu.
7 Cumque dixerint ad te: Quare tu gemis? dices: Pro auditu: quia venit, et tabescet omne cor, et dissolventur universæ manus, et infirmabitur omnis spiritus, et per cuncta genua fluent aquæ: ecce venit, et fiet, ait Dominus Deus.
Ndipo akadzakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukubuwula?’ Iwe udzayankhe kuti, ‘Ndikubuwula chifukwa cha nkhani imene ndamva. Zikadzachitika zimenezi, mitima yonse idzangoti fumu, manja onse adzangolefuka, mpweya wawo udzawathera, ndipo mawondo onse adzangoti zii.’ Izi zikubwera! Ndipo zidzachitika ndithu, akutero Ambuye Yehova.”
8 Et factus est sermo Domini ad me, dicens:
Yehova anandiyankhulanso kuti,
9 Fili hominis, propheta, et dices: Hæc dicit Dominus Deus: loquere: Gladius, gladius exacutus est, et limatus:
“Iwe mwana wa munthu, unenere ndipo unene kuti, Ambuye Yehova akuti, “Izi ndi zimene Yehova akunena: Lupanga, lupanga, lanoledwa ndipo lapukutidwa.
10 ut cædat victimas, exacutus est: ut splendeat, limatus est: qui moves sceptrum filii mei, succidisti omne lignum.
Lanoledwa kuti likaphe, lapukutidwa kuti lingʼanime ngati mphenzi! “‘Kodi tingakondwere bwanji? Wanyoza ndodo, mwana wanga ndi chilichonse cha mtengo.
11 Et dedi eum ad levigandum, ut teneatur manu: iste exacutus est gladius, et iste limatus est, ut sit in manu interficientis.
“‘Lupanga laperekedwa kuti lipukutidwe, ndi kuti linyamulidwe, lanoledwa ndi kupukutidwa, kuti liperekedwe mʼmanja mwa munthu amene amapha.
12 Clama et ulula, fili hominis, quia hic factus est in populo meo, hic in cunctis ducibus Israël qui fugerant: gladio traditi sunt cum populo meo: idcirco plaude super femur,
Fuwula ndi kulira, iwe mwana wa munthu, pakuti zimenezi zidzagwera anthu anga; zidzagweranso akalonga onse a Israeli. Adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi anthu anga. Chifukwa chake udzigugude pa chifuwa ndi chisoni.
13 quia probatus est: et hoc, cum sceptrum subverterit, et non erit, dicit Dominus Deus.
“‘Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Ndikuwayesa anthu anga, ndipo ngati satembenuka mtima, ndiye kuti zimenezi sizidzalephera kuwagwera.’
14 Tu ergo, fili hominis, propheta, et percute manu ad manum: et duplicetur gladius, ac triplicetur gladius interfectorum: hic est gladius occisionis magnæ, qui obstupescere eos facit
“Tsono mwana wa munthu, nenera ndipo uwombe mʼmanja. Lupanga likanthe kawiri ngakhale katatu. Limenelo ndilo lupanga lophera anthu. Inde ndilodi lupanga lophera anthu koopsa limene likuwazungulira.
15 et corde tabescere, et multiplicat ruinas. In omnibus portis eorum dedi conturbationem gladii acuti, et limati ad fulgendum, amicti ad cædem.
Ndawayikira pa zipata zawo zonse lupanga laphuliphuli kuti ataye mtima ndiponso kuti anthu ambiri agwe. Aa! Lapangidwa lupanga kuti lizingʼanima ngati mphenzi ndi kuti azilisolola kuphera anthu.
16 Exacuere, vade ad dexteram sive ad sinistram, quocumque faciei tuæ est appetitus.
Iwe lupanga, ipha anthu kumanja, kenaka kumanzere, kulikonse kumene msonga yako yaloza.
17 Quin et ego plaudam manu ad manum, et implebo indignationem meam: ego Dominus locutus sum.
Inenso ndidzawomba mʼmanja mwanga, ndipo ndidzaziziritsa ukali wanga Ine Yehova ndayankhula.”
18 Et factus est sermo Domini ad me, dicens:
Yehova anandiyankhulanso kuti,
19 Et tu, fili hominis, pone tibi duas vias, ut veniat gladius regis Babylonis: de terra una egredientur ambæ: et manu capiet conjecturam; in capite viæ civitatis conjiciet.
“Iwe mwana wa munthu, ulembe zizindikiro za misewu iwiri imene lupanga la mfumu ya ku Babuloni lingathe kudzeramo. Misewu yonse ikhale yochokera mʼdziko limodzi. Ika chikwangwani pa mphambano yopita mu mzinda.
20 Viam pones ut veniat gladius ad Rabbath filiorum Ammon, et ad Judam in Jerusalem munitissimam.
Ulembe chizindikiro pa msewu umene lupanga lidzadzere popita ku Raba wa ku Amoni, ndiponso ku Yuda ndi ku Yerusalemu, mzinda wotetezedwa.
21 Stetit enim rex Babylonis in bivio, in capite duarum viarum, divinationem quærens, commiscens sagittas: interrogavit idola, exta consuluit.
Pakuti mfumu ya ku Babuloni yayima pa msewu, pa mphambano ya misewu iwiriyo. Ikuwombeza ndi mivi yake kuti idziwe njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake ndipo ikuyangʼana chiwindi cha nyama yoperekedwa ku nsembe.
22 Ad dexteram ejus facta est divinatio super Jerusalem, ut ponat arietes, ut aperiat os in cæde, ut elevet vocem in ululatu, ut ponat arietes contra portas, ut comportet aggerem, ut ædificet munitiones.
Mʼdzanja lake lamanja muli muvi waula wolembedwa Yerusalemu. Kumeneko mfumuyo idzayika zida zogumulira, idzalamula kupha anthu ndiponso kufuwula mfuwu wa nkhondo. Mfumuyo idzapanga zida zogumulira makoma, kuwunda mitumbira ya nkhondo ndi kumanga nsanja za nkhondo.
23 Eritque quasi consulens frustra oraculum in oculis eorum, et sabbatorum otium imitans: ipse autem recordabitur iniquitatis ad capiendum.
Koma kwa anthu a ku Yerusalemu zidzaoneka ngati zowombeza zabodza chifukwa cha malumbiro amene anachita kwa mfumuyo. Koma mfumuyo idzawakumbutsa za zolakwa zawo kuti atengedwe ku ukapolo.
24 Idcirco hæc dicit Dominus Deus: Pro eo quod recordati estis iniquitatis vestræ, et revelastis prævaricationes vestras, et apparuerunt peccata vestra in omnibus cogitationibus vestris, pro eo, inquam, quod recordati estis, manu capiemini.
“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Popeza mwandikumbutsa zolakwa, moti kundiwukira kwanu kwaonekera poyera ndi kuti mu zochita zanu zonse mukuonetsa machimo anu, nʼchifukwa chake mudzagwidwa ndi kutengedwa ukapolo.
25 Tu autem, profane, impie dux Israël, cujus venit dies in tempore iniquitatis præfinita:
“‘Tsono iwe kalonga wonyozedwa ndi woyipa wa Israeli, amene tsiku lako lafika, amene nthawi yako yolangidwa yafika penipeni,
26 hæc dicit Dominus Deus: Aufer cidarim, tolle coronam: nonne hæc est quæ humilem sublevavit, et sublimem humiliavit?
Ambuye Yehova akuti: Vula nduwira, chotsa chipewa chaufumu. Zinthu sizidzakhala monga zinalili: anthu wamba adzakwezedwa ndipo okwezedwa adzatsitsidwa.
27 Iniquitatem, iniquitatem, iniquitatem ponam eam: et hoc non factum est, donec veniret cujus est judicium, et tradam ei.
Chipasupasu! Chipasupasu! Ine ndidzawupasula mzindawo! Ndipo sadzawumanganso mpaka atafika amene ali woyenera kuwulandira; Ine ndidzawupereka kwa iyeyo.’
28 Et tu, fili hominis, propheta, et dic: Hæc dicit Dominus Deus ad filios Ammon, et ad opprobrium eorum: et dices: Mucro, mucro, evaginate ad occidendum: limate ut interficias et fulgeas:
“Ndipo iwe mwana wa munthu, nenera kuti, ponena za Aamoni ndi zonyoza zawo, Ambuye Yehova akuti, “‘Lupanga, lupanga, alisolola kuti liphe anthu, alipukuta kuti liwononge ndi kuti lingʼanime ngati mphenzi.
29 cum tibi viderentur vana, et divinarentur mendacia, ut dareris super colla vulneratorum impiorum, quorum venit dies in tempore iniquitatis præfinita.
Zimene akuti akuona mʼmasomphenya zokhudza inu ndi zabodza. Mawula awo okhudza inu ndi abodzanso. Mudzakhala pamodzi ndi anthu oyipa amene tsiku lawo lafika, ndiye kuti nthawi ya kulangidwa kwawo komaliza.
30 Revertere ad vaginam tuam, in loco in quo creatus es: in terra nativitatis tuæ judicabo te.
“‘Bwezerani lupanga mʼchimake. Ku malo kumene inu munabadwira, mʼdziko la makolo anu, ndidzakuweruzani.
31 Et effundam super te indignationem meam; in igne furoris mei sufflabo in te: daboque te in manus hominum insipientium, et fabricantium interitum.
Ndidzakhuthula ukali wanga pa inu, ndipo mkwiyo wanga udzakuyakirani. Ndidzakuperekani mʼmanja mwa anthu ankhanza; anthu odziwa bwino kuwononga zinthu.
32 Igni eris cibus; sanguis tuus erit in medio terræ; oblivioni traderis: quia ego Dominus locutus sum.
Mudzakhala ngati nkhuni pa moto. Ena adzakhetsa magazi anu mʼdziko lanu lomwe. Simudzakumbukiridwanso pakuti Ine Yehova ndayankhula.’”

< Hiezechielis Prophetæ 21 >