< Deuteronomii 30 >

1 Cum ergo venerint super te omnes sermones isti, benedictio sive maledictio, quam proposui in conspectu tuo: et ductus pœnitudine cordis tui in universis gentibus, in quas disperserit te Dominus Deus tuus,
Madalitso ndi matemberero awa onse amene ndawayika pamaso panu akadzafika pa inu, inu nʼkukumbukira kulikonse kumene Yehova Mulungu wanu wakubalalitsirani pakati pa mitundu ya anthu,
2 et reversus fueris ad eum, et obedieris ejus imperiis, sicut ego hodie præcipio tibi, cum filiis tuis, in toto corde tuo, et in tota anima tua:
ndipo inu pamodzi ndi ana anu nʼkudzatembenukira kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumumvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse molingana ndi chilichonse chimene ndakulamulani lero lino,
3 reducet Dominus Deus tuus captivitatem tuam, ac miserebitur tui, et rursum congregabit te de cunctis populis, in quos te ante dispersit.
pamenepo Yehova Mulungu wanu adzakukhalitsani monga kale ndi kukuchitirani chifundo, ndipo adzakusonkhanitsani kukuchotsani ku mitundu ina ya anthu kumene anakubalalitsirani.
4 Si ad cardines cæli fueris dissipatus, inde te retrahet Dominus Deus tuus,
Ngakhale atakupirikitsirani ku malekezero a dziko lapansi, adzakusonkhanitsani kuchokera kumeneko ndi kukubweretsaninso.
5 et assumet, atque introducet in terram, quam possederunt patres tui, et obtinebis eam: et benedicens tibi, majoris numeri te esse faciat quam fuerunt patres tui.
Adzakubweretsani ku dziko limene linali la makolo anu, ndipo lidzakhala lanu. Iye adzakulemeretsani ndi kukuchulukitsani kupambana makolo anu.
6 Circumcidet Dominus Deus tuus cor tuum, et cor seminis tui, ut diligas Dominum Deum tuum in toto corde tuo, et in tota anima tua, ut possis vivere.
Yehova Mulungu wanu adzasintha mitima yanu pamodzi ndi mitima ya zidzukulu zanu, kotero kuti mudzamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, ndipo mudzakhala ndi moyo.
7 Omnes autem maledictiones has convertet super inimicos tuos, et eos qui oderunt te et persequuntur.
Yehova Mulungu wanu adzayika matemberero awa onse pa adani anu amene amadana nanu ndi kukuzunzani.
8 Tu autem reverteris, et audies vocem Domini Dei tui, faciesque universa mandata quæ ego præcipio tibi hodie:
Inu mudzamveranso Yehova ndi kutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino.
9 et abundare te faciet Dominus Deus tuus in cunctis operibus manuum tuarum, in sobole uteri tui, et in fructu jumentorum tuorum, in ubertate terræ tuæ, et in rerum omnium largitate. Revertetur enim Dominus, ut gaudeat super te in omnibus bonis, sicut gavisus est in patribus tuis:
Pamenepo Yehova Mulungu wanu adzakulemeretsani pa zochita zanu zonse ndipo adzakupatsani ana ambiri, zoweta zambiri, ndiponso mudzakhala ndi zokolola zambiri za mʼdziko lanu. Yehova adzakondwera nanunso ndi kukulemeretsani monga momwe anakondwera ndi makolo anu,
10 si tamen audieris vocem Domini Dei tui, et custodieris præcepta ejus et cæremonias, quæ in hac lege conscripta sunt: et revertaris ad Dominum Deum tuum in toto corde tuo, et in tota anima tua.
ngati mudzamvera Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo ake ndi mawu ake amene alembedwa Mʼbuku ili la Malamulo ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
11 Mandatum hoc, quod ego præcipio tibi hodie, non supra te est, neque procul positum,
Tsopano zimene ndikukulamulirani leroli sizovuta kapena zapatali.
12 nec in cælo situm, ut possis dicere: Quis nostrum valet ad cælum ascendere, ut deferat illud ad nos, et audiamus atque opere compleamus?
Sizili kumwamba, kuti muzichita kufunsa kuti, “Kodi ndani amene akwere kumwamba kuti akazitenge ndi kudzatilalikira kuti timvere?”
13 neque trans mare positum: ut causeris, et dicas: Quis ex nobis poterit transfretare mare, et illud ad nos usque deferre, ut possimus audire et facere quod præceptum est?
Komanso sizili pa tsidya la nyanja, kuti muzichita kufunsa kuti, “Kodi ndani amene adzawoloke nyanja kuti akatenge ndi kudzatilalikira kuti timvere?”
14 sed juxta te est sermo valde, in ore tuo, et in corde tuo, ut facias illum.
Ayi, mawu ali pafupi ndi inu; ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu kuti muwamvere.
15 Considera quod hodie proposuerim in conspectu tuo, vitam et bonum, et e contrario mortem et malum:
Taonani, lero ine ndayika pamaso panu moyo ndi zokoma, imfa ndi chiwonongeko.
16 ut diligas Dominum Deum tuum, et ambules in viis ejus, et custodias mandata illius ac cæremonias atque judicia: et vivas, atque multiplicet te, benedicatque tibi in terra, ad quam ingredieris possidendam.
Pakuti lero ndikukulamulani kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kuti muyende mʼnjira zake, ndi kusunga malamulo ake, malangizo ake. Mukatero mudzakhala ndi moyo ndi kuchulukana, ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene mukulowa kukakhalamo.
17 Si autem aversum fuerit cor tuum, et audire nolueris, atque errore deceptus adoraveris deos alienos, et servieris eis:
Koma ngati mtima wanu udzatembenuka, inu nʼkukhala osandimvera, ndipo ngati mudzatengeka ndi kupita kukagwadira milungu ina ndi kuyipembedza,
18 prædico tibi hodie quod pereas, et parvo tempore moreris in terra, ad quam, Jordane transmisso, ingredieris possidendam.
lero ndikulengeza kwa inu kuti mudzawonongeka ndithu. Simudzakhala nthawi yayitali mʼdziko limene mukulowamo pamene mukuwoloka Yorodani kuti mulitenge.
19 Testes invoco hodie cælum et terram, quod proposuerim vobis vitam et mortem, benedictionem et maledictionem. Elige ergo vitam, ut et tu vivas, et semen tuum:
Lero kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni zodzakutsutsani pakuti ndayika pamaso panu moyo ndi imfa, madalitso ndi matemberero. Tsopano sankhani moyo kuti inu ndi ana anu mukhale ndi moyo.
20 et diligas Dominum Deum tuum, atque obedias voci ejus, et illi adhæreas (ipse est enim vita tua, et longitudo dierum tuorum), ut habites in terra, pro qua juravit Dominus patribus tuis, Abraham, Isaac, et Jacob, ut daret eam illis.
Ndi kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kukhulupirika kwa Iye. Pakuti Yehova ndiye moyo wanu, ndipo mudzakhala zaka zambiri mʼdziko limene analumbira kulipereka kwa makolo anu, Abrahamu, Isake ndi Yakobo.

< Deuteronomii 30 >