< I Samuelis 30 >

1 Cumque venissent David et viri ejus in Siceleg die tertia, Amalecitæ impetum fecerant ex parte australi in Siceleg, et percusserant Siceleg, et succenderant eam igni.
Pa tsiku lachitatu, Davide ndi anthu ake anakafika ku Zikilagi. Tsono anapeza Aamaleki atawononga kale dera la Negevi ndi Zikilagi. Anathira nkhondo mzinda wa Zikilagi ndi kuwutentha ndi moto.
2 Et captivas duxerant mulieres ex ea, a minimo usque ad magnum: et non interfecerant quemquam, sed secum duxerant, et pergebant itinere suo.
Anatenga akazi ndi onse amene anali mʼmenemo akuluakulu ndi angʼono omwe kuti akakhale akapolo. Sanaphe aliyense koma anawatenga amoyo napita nawo.
3 Cum ergo venissent David et viri ejus ad civitatem, et invenissent eam succensam igni, et uxores suas, et filios suos et filias, ductas esse captivas,
Davide ndi anthu ake atafika ku Zikilagi anapeza kuti mzindawo watenthedwa ndi moto ndipo akazi awo, ana awo, amuna ndi akazi atengedwa ukapolo.
4 levaverunt David et populus qui erat cum eo voces suas, et planxerunt donec deficerent in eis lacrimæ.
Kotero Davide ndi anthu ake analira mofuwula mpaka analibenso mphamvu zolirira.
5 Siquidem et duæ uxores David captivæ ductæ fuerant, Achinoam Jezrahelites, et Abigail uxor Nabal Carmeli.
Akazi awiri a Davide, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli mkazi wa Nabala wa ku Karimeli anatengedwanso.
6 Et contristatus est David valde: volebat enim eum populus lapidare, quia amara erat anima uniuscujusque viri super filiis suis et filiabus: confortatus est autem David in Domino Deo suo.
Davide anavutika kwambiri mu mtima mwake chifukwa anthu amakamba zoti amuponye miyala popeza aliyense anali ndi chisoni pokumbukira ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anapeza mphamvu mwa Yehova Mulungu wake.
7 Et ait ad Abiathar sacerdotem filium Achimelech: Applica ad me ephod. Et applicavit Abiathar ephod ad David.
Kenaka Davide anawuza wansembe Abiatara, mwana wa Ahimeleki kuti, “Ndipatse efodi ija.” Abiatara anabwera nayo efodiyo.
8 Et consuluit David Dominum, dicens: Persequar latrunculos hos, et comprehendam eos, an non? Dixitque ei Dominus: Persequere: absque dubio enim comprehendes eos, et excuties prædam.
Tsono Davide anapempha nzeru kwa Yehova nati, “Kodi ndilitsatire gulu lankhondoli? Kodi ndidzawapambana?” Yehova anayankha kuti, “Litsatire, iwe udzawapambana ndithu ndipo udzapulumutsa anthu ako.”
9 Abiit ergo David, ipse et sexcenti viri qui erant cum eo, et venerunt usque ad torrentem Besor: et lassi quidam substiterunt.
Davide pamodzi ndi anthu ake 600 aja ananyamuka nafika ku mtsinje wa Besori. Kumeneko anasiyako anthu ena.
10 Persecutus est autem David ipse, et quadringenti viri: substiterant enim ducenti, qui lassi transire non poterant torrentem Besor.
Davide ndi anthu ake 400 anapitirira kuwalondola Aamaleki aja. Koma anthu ena 200 anatsala popeza anatopa moti sakanatha kuwoloka mtsinje wa Besori uja.
11 Et invenerunt virum ægyptium in agro, et adduxerunt eum ad David: dederuntque ei panem ut comederet, et biberet aquam,
Anthu amene anali ndi Davide anapeza Mwigupto mʼmunda wina ndipo anabwera naye kwa Davide. Iwo anamupatsa madzi kuti amwe ndi chakudya kuti adye.
12 sed et fragmen massæ caricarum, et duas ligaturas uvæ passæ. Quæ cum comedisset, reversus est spiritus ejus, et refocillatus est: non enim comederat panem, neque biberat aquam, tribus diebus et tribus noctibus.
Anamupatsanso chidutswa cha keke yankhuyu ndi makeke awiri a mphesa zowumika kuti adye. Atadya anapezanso mphamvu popeza anakhala masiku atatu wosadya kapena kumwa kanthu kalikonse.
13 Dixit itaque ei David: Cujus es tu? vel unde? et quo pergis? Qui ait: Puer ægyptius ego sum, servus viri Amalecitæ: dereliquit autem me dominus meus, quia ægrotare cœpi nudiustertius.
Davide anafunsa kuti, “Kodi ndiwe yani, ndipo ukuchokera kuti?” Iye anayankha kuti, “Ine ndine Mwigupto, kapolo wa Mwamaleki. Mbuye wanga anandisiya nditayamba kudwala masiku atatu apitawo.
14 Siquidem nos erupimus ad australem plagam Cerethi, et contra Judam, et ad meridiem Caleb, et Siceleg succendimus igni.
Ife tinathira nkhondo dera la kummwera kwa mayiko a Akereti, dera la Yuda, ndi dera la kummwera kwa mayiko a Kalebe. Mzinda wa Zikilagi tinawutentha ndi moto.”
15 Dixitque ei David: Potes me ducere ad cuneum istum? Qui ait: Jura mihi per Deum quod non occidas me, et non tradas me in manus domini mei, et ego ducam te ad cuneum istum. Et juravit ei David.
Davide anamupempha kuti, “Kodi unganditsogolere kumene kuli gulu lankhondoli?” Iye anayankha kuti, “Mukandilonjeza molumbira kuti simudzandipha kapena kundipereka kwa mbuye wanga, ine ndikulondolerani kumene kuli gululo.”
16 Qui cum duxisset eum, ecce illi discumbebant super faciem universæ terræ comedentes et bibentes, et quasi festum celebrantes diem, pro cuncta præda et spoliis quæ ceperant de terra Philisthiim et de terra Juda.
Mwigupto uja anaperekeza Davide. Tsono Aamaleki anali atamwazikana ponseponse. Iwo ankadya, kumwa ndi kuvina chifukwa cha zofunkha zambiri zimene anatenga ku dziko la Afilisti ndi ku dziko la Ayuda.
17 Et percussit eos David a vespere usque ad vesperam alterius diei, et non evasit ex eis quisquam, nisi quadringenti viri adolescentes, qui ascenderant camelos et fugerant.
Tsono Davide anawakantha kuyambira madzulo atsikulo mpaka madzulo a tsiku linalo. Palibe anapulumuka kupatula anyamata 400 amene anakwera pa ngamira nʼkuthawa.
18 Eruit ergo David omnia quæ tulerant Amalecitæ, et duas uxores suas eruit.
Choncho Davide analanditsa zinthu zonse zimene Aamaleki aja anatenga. Anapulumutsanso akazi ake awiri aja.
19 Nec defuit quidquam a parvo usque ad magnum, tam de filiis quam de filiabus, et de spoliis, et quæcumque rapuerant: omnia reduxit David.
Palibe chimene chinasowa anthu onse, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, mnyamata mpaka mtsikana anapulumutsidwa. Davide anapulumutsa chilichonse chimene anafunkha Aamaleki aja.
20 Et tulit universos greges et armenta, et minavit ante faciem suam: dixeruntque: Hæc est præda David.
Anapulumutsanso nkhosa ndi ngʼombe zonse. Tsono anthu ankakusa ziwetozo namati, “Izi ndizo zofunkha za Davide.”
21 Venit autem David ad ducentos viros qui lassi substiterant, nec sequi potuerant David, et residere eos jusserat in torrente Besor: qui egressi sunt obviam David et populo qui erat cum eo. Accedens autem David ad populum, salutavit eos pacifice.
Davide anafika ku malo kumene kunali anthu 200 otopa kwambiri aja amene sanathe kutsagana naye koma anangokhala ku mtsinje wa Besori. Tsono ananyamuka kuti akumane ndi Davide pamodzi ndi anthu amene anali naye. Davide anawayandikira nawalonjera.
22 Respondensque omnis vir pessimus et iniquus de viris qui ierant cum David, dixit: Quia non venerunt nobiscum, non dabimus eis quidquam de præda quam eruimus: sed sufficiat unicuique uxor sua et filii: quos cum acceperint, recedant.
Tsono anthu ena oyipa mtima achabechabe mwa amene anatsagana ndi Davide aja anati, “Popeza awa sanapite nafe, sitiwapatsako zofunkha zimene tapulumutsazi, kupatula kuti aliyense atenge mkazi wake ndi ana ake azipita.”
23 Dixit autem David: Non sic facietis, fratres mei, de his quæ tradidit nobis Dominus, et custodivit nos, et dedit latrunculos qui eruperant adversum nos, in manus nostras:
Koma Davide anawayankha kuti, “Ayi, abale anga, musachite zimenezi ndi zinthu zimene Yehova watipatsa. Iye watisunga ndi kupereka mʼmanja mwathu gulu la ankhondo limene linabwera kudzalimbana nafe.
24 nec audiet vos quisquam super sermone hoc: æqua enim pars erit descendentis ad prælium, et remanentis ad sarcinas, et similiter divident.
Ndani angakumvereni zimene mukunenazi? Gawo la munthu amene anapita kukamenya nkhondo likhale lofanana ndi la munthu amene anatsala pano kuyangʼanira katundu wathu. Pasakhale kusiyana kulikonse.”
25 Et factum est hoc ex die illa et deinceps, constitutum et præfinitum, et quasi lex in Israël usque in diem hanc.
Choncho Davide anakhazikitsa ngati lamulo mʼchitidwe woterewu pakati pa Aisraeli kuyambira tsiku limenelo mpaka lero.
26 Venit ergo David in Siceleg, et misit dona de præda senioribus Juda proximis suis, dicens: Accipite benedictionem de præda hostium Domini:
Davide atafika ku Zikilagi, anatumiza zina mwa zofunkhazo kwa akuluakulu a Yuda, amene anali abwenzi ake. Anati, “Nayi mphatso yanu yochokera pa zofunkha za adani a Yehova.”
27 his qui erant in Bethel, et qui in Ramoth ad meridiem, et qui in Jether,
Iye anatumiza mphatsozo kwa anthu a ku Beteli, Ramoti-Negavi, Yatiri,
28 et qui in Aroër, et qui in Sephamoth, et qui in Esthamo,
Aroeri, Sifimoti, Esitemowa
29 et qui in Rachal, et qui in urbibus Jerameel, et qui in urbibus Ceni,
Rakala, mizinda ya fuko la Ayerahimeeli, mizinda ya fuko la Akeni,
30 et qui in Arama, et qui in lacu Asan, et qui in Athach,
a ku Horima, Borasani, Ataki,
31 et qui in Hebron, et reliquis qui erant in his locis in quibus commoratus fuerat David, ipse et viri ejus.
Hebroni pamodzi ndi onse a kumalo kumene Davide ndi anthu ake anakhala akuyendayendako.

< I Samuelis 30 >