< Zaccharias Propheta 7 >

1 Et factum est in anno quarto Darii regis, factum est verbum Domini ad Zachariam, in quarta mensis noni, qui est Casleu.
Pa chaka chachinayi cha Mfumu Dariyo, pa tsiku lachinayi la Kisilevi, mwezi wachisanu ndi chinayi, Yehova anayankhula ndi Zekariya.
2 Et miserunt ad domum Dei Sarasar, et Rogommelech, et viri, qui erant cum eo ad deprecandam faciem Domini:
Anthu a ku Beteli anali atatuma Sarezeri ndi Regemu-Meleki pamodzi ndi anthu awo, kuti akapemphe chifundo kwa Yehova
3 ut dicerent sacerdotibus domus Domini exercituum, et prophetis loquentes: numquid flendum est mihi in quinto mense, vel sanctificare me debeo, sicut iam feci multis annis?
pokafunsa kwa ansembe a ku Nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse ndi aneneri kuti, “Kodi ine ndizilira ndi kusala zakudya pa mwezi wachisanu, monga mmene ndakhala ndikuchitira pa zaka zambiri?”
4 Et factum est verbum Domini exercituum ad me, dicens:
Pamenepo Yehova Wamphamvuzonse anayankhula nane kuti,
5 Loquere ad omnem populum terræ, et ad sacerdotes, dicens: Cum ieiunaretis, et plangeretis in quinto et septimo per hos septuaginta annos: numquid ieiunium ieiunastis mihi?
“Funsa anthu onse a mʼdziko ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala zakudya pa mwezi wachisanu ndi wachisanu ndi chiwiri pa zaka 70 zapitazi, kodi munkasala chifukwa cha Ine?
6 et cum comedistis, et bibistis, numquid non vobis comedistis, et vobismetipsis bibistis?
Ndipo pamene munkadya ndi kumwa, kodi simunkachita zimenezi podzisangalatsa nokha?
7 Numquid non sunt verba, quæ locutus est Dominus in manu prophetarum priorum, cum adhuc Ierusalem habitaretur, ut esset opulenta, ipsa et urbes in circuitu eius, et ad Austrum, et in campestribus habitaretur?
Kodi awa si mawu amene Yehova ankanena kudzera mwa aneneri oyamba aja pamene Yerusalemu ndi mizinda yake yozungulira anali pa mtendere ndi pa ulemerero, ndi pamene Negevi ndi ku madera akumadzulo a mʼmbali mwa phiri munali anthu?’”
8 Et factum est verbum Domini ad Zachariam, dicens:
Ndipo Yehova anayankhulanso ndi Zekariya kuti,
9 Hæc ait Dominus exercituum, dicens: Iudicium verum iudicate, et misericordiam, et miserationes facite, unusquisque cum fratre suo.
“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Muziweruza molungama; muzichitirana chifundo ndi kumverana chisoni.
10 Et viduam, et pupillum, et advenam, et pauperem nolite calumniari: et malum vir fratri suo non cogitet in corde suo.
Musamazunze akazi amasiye kapena ana amasiye, alendo kapena osauka. Musamaganizirane zoyipa mʼmitima mwanu.’
11 Et noluerunt attendere, et averterunt scapulam recedentem, et aures suas aggravaverunt ne audirent.
“Koma makolo anu anakana kumvera uthenga umenewu; anawumitsa mtima nandifulatira, natseka makutu awo kuti asamve.
12 Et cor suum posuerunt ut adamantem, ne audirent legem, et verba quæ misit Dominus exercituum in spiritu suo per manum prophetarum priorum: et facta est indignatio magna a Domino exercituum.
Anawumitsa mitima yawo ngati mwala wa sangalabwi ndipo sanamvere lamulo kapena mawu amene Yehova Wamphamvuzonse anawatumiza mwa Mzimu wake kudzera mwa aneneri oyamba aja. Kotero Yehova Wamphamvuzonse anakwiya kwambiri.
13 Et factum est sicut locutus est, et non audierunt: sic clamabunt, et non exaudiam, dicit Dominus exercituum.
“‘Pamene ndinawayitana, iwo sanamvere; choncho pamene iwo anandiyitana, Ine sindinamverenso,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.
14 Et dispersi eos per omnia regna, quæ nesciunt: et terra desolata est ab eis, eo quod non esset transiens et revertens: et posuerunt terram desiderabilem in desertum.
‘Ndinawamwaza ndi kamvuluvulu pakati pa mitundu yonse ya anthu, kumene anali alendo. Dziko lawo linatsala litasakazidwa kwambiri kotero kuti palibe amene amabwera kapena kupitamo. Umu ndi mmene anasandutsira dziko labwino kukhala chipululu.’”

< Zaccharias Propheta 7 >