< Apocalypsis 1 >

1 Apocalypsis Iesu Christi, quam dedit illi Deus palam facere servis suis, quæ oportet fieri cito: et significavit, mittens per Angelum suum servo suo Ioanni,
Vumbulutso lochokera kwa Yesu Khristu, limene Mulungu anamupatsa kuti aonetse atumiki ake zimene zinayenera kuchitika posachedwa. Iye anatuma mngelo wake kuti adziwitse mtumiki wake Yohane,
2 qui testimonium perhibuit Verbo Dei, et testimonium Iesu Christi, quæcumque vidit.
amene akuchitira umboni chilichonse chimene anachiona. Awa ndi Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu Khristu.
3 Beatus, qui legit, et audit verba Prophetiæ huius: et servat ea, quæ in ea scripta sunt: tempus enim prope est.
Ngodala munthu amene awerenga mawu oneneratu zamʼtsogolo ndi iwo amene amamva ndi kusunga zolembedwa mʼbukuli pakuti nthawi yayandikira.
4 Ioannes septem Ecclesiis, quæ sunt in Asia. Gratia vobis, et pax ab eo, qui est, et qui erat, et qui venturus est: et a septem Spiritibus, qui in conspectu throni eius sunt:
Ndine Yohane, Kupita ku mipingo isanu ndi iwiri ya mʼchigawo cha Asiya. Chisomo ndi mtendere kwa inu, kuchokera kwa Iye amene ali, amene analipo ndi amene akubwera ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala patsogolo pa mpando wake waufumu,
5 et a Iesu Christo, qui est testis fidelis, primogenitus mortuorum, et princeps regum terræ, qui dilexit nos, et lavit nos a peccatis nostris in sanguine suo,
ndiponso kuchokera kwa Yesu Khristu mboni yokhulupirika, woyamba kuukitsidwa, ndi wolamulira mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene amatikonda ndipo watimasula ku machimo athu ndi magazi ake,
6 et fecit nos regnum, et sacerdotes Deo et Patri suo: ipsi gloria, et imperium in sæcula sæculorum: Amen. (aiōn g165)
ndipo watisandutsa mafumu ndi ansembe kuti tizitumikira Mulungu ndi Atate ake. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu ku nthawi zosatha, Ameni. (aiōn g165)
7 Ecce venit cum nubibus, et videbit eum omnis oculus, et qui eum pupugerunt. Et plangent se super eum omnes tribus terræ: Etiam: Amen.
“Onani akubwera ndi mitambo,” ndipo “Aliyense adzamuona, ndi amene anamubaya omwe.” Ndipo anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi “adzalira chingʼangʼadza chifukwa cha Iye.”
8 Ego sum α, et ω, principium, et finis, dicit Dominus Deus: qui est, et qui erat, et qui venturus est, omnipotens.
“Ine ndine Alefa ndi Omega,” akutero Ambuye Mulungu Wamphamvuzonseyo “amene muli, amene munalipo, ndi amene mudzakhalapo.”
9 Ego Ioannes frater vester, et particeps in tribulatione, et regno et patientia in Christo Iesu: fui in insula, quæ appellatur Patmos propter Verbum Dei, et testimonium Iesu:
Ine Yohane mʼbale wanu ndi mnzanu mʼmasautso ndi mu ufumu ndi mukupirira kwambiri, zomwe ndi zathu mwa Yesu, ndinali pa chilumba cha Patimo chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu.
10 Fui in Spiritu in Dominica die, et audivi post me vocem magnam tamquam tubæ,
Pa tsiku la Ambuye ndinanyamulidwa ndi Mzimu ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mawu ofuwula ngati lipenga,
11 dicentis: Quod vides, scribe in libro: et mitte septem Ecclesiis, quæ sunt in Asia, Epheso, et Smyrnæ, et Pergamo, et Thyatiræ, et Sardis, et Philadelphiæ, et Laodiciæ:
amene anati, “Lemba mʼbuku zimene ukuziona ndipo uzitumize ku mipingo isanu ndi iwiri ya ku Efeso, Simurna, Pergamo, Tiyatira, Sarde, Filadefiya ndi ku Laodikaya.”
12 Et conversus sum ut viderem vocem, quæ loquebatur mecum: Et conversus vidi septem candelabra aurea:
Nditatembenuka kuti ndione amene amandiyankhulayo, ndinaona zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide.
13 et in medio septem candelabrorum aureorum, similem Filio hominis, vestitum podere, et præcinctum ad mamillas zona aurea:
Pakati pa zoyikapo nyalezo ndinaona wina wooneka ngati Mwana wa Munthu atavala mkanjo wofika kumapazi ake ndipo anamangirira lamba wagolide pa chifuwa pake.
14 caput autem eius, et capilli erant candidi tamquam lana alba, et tamquam nix, et oculi eius tamquam flamma ignis,
Tsitsi lake linali loyera ngati thonje, kuyera ngati matalala, ndipo maso ake amawala ngati malawi amoto.
15 et pedes eius similes aurichalco, sicut in camino ardenti, et vox illius tamquam vox aquarum multarum:
Mapazi ake anali ngati chitsulo choti chili mʼngʼanjo yamoto, ndipo mawu ake anali ngati mkokomo wamadzi othamanga.
16 et habebat in dextera sua stellas septem: et de ore eius gladius utraque parte acutus exibat: et facies eius sicut sol lucet in virtute sua.
Mʼdzanja lake lamanja ananyamula nyenyezi zisanu ndi ziwiri, ndipo mʼkamwa mwake munali lupanga lakuthwa konsekonse. Nkhope yake imawala ngati dzuwa lowala kwambiri.
17 Et cum vidissem eum, cecidi ad pedes eius tamquam mortuus. Et posuit dexteram suam super me, dicens: Noli timere: ego sum primus, et novissimus,
Nditamuona ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa. Kenaka Iye anasanjika dzanja lake lamanja pa ine nati, “Usachite mantha. Ndine Woyamba ndi Wotsiriza.
18 et vivus, et fui mortuus, et ecce sum vivens in sæcula sæculorum, et habeo claves mortis, et inferni. (aiōn g165, Hadēs g86)
Ine ndine Wamoyo; ndinali wakufa ndipo taona ndine wamoyo mpaka muyaya! Ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi Hade. (aiōn g165, Hadēs g86)
19 Scribe ergo quæ vidisti, et quæ sunt, et quæ oportet fieri post hæc.
“Chomwecho, lemba zimene waona, zimene zilipo panopa ndi zimene zidzachitike mʼtsogolo.
20 Sacramentum septem stellarum, quas vidisti in dextera mea, et septem candelabra aurea: septem stellæ Angeli sunt septem Ecclesiarum: et candelabra septem, septem Ecclesiæ sunt.
Tanthauzo la nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene waziona mʼdzanja langa lamanja ndi la zoyikapo nyale zagolide zisanu ndi ziwiri ndi ili: Nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndi angelo a mipingo isanu ndi iwiri ija, ndipo zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zija ndi mipingo isanu ndi iwiri ija.”

< Apocalypsis 1 >