< Hiezechielis Prophetæ 27 >

1 Et factum est verbum Domini ad me, dicens:
Yehova anandiyankhula kuti:
2 Tu ergo fili hominis assume super Tyrum lamentum:
“Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira Turo.
3 Et dices Tyro, quæ habitat in introitu maris, negotiationi populorum ad insulas multas: Hæc dicit Dominus Deus: O Tyre, tu dixisti: Perfecti decoris ego sum,
Uza Turo, mzinda wokhala pa dooko la nyanja, wochita malonda ndi anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja kuti: Ambuye Yehova akuti, “Iwe Turo, umanena kuti, ‘Ndine wokongola kwambiri.’
4 et in corde maris sita. Finitimi tui, qui te ædificaverunt, impleverunt decorem tuum:
Malire ako anali mʼkati mwenimweni mwa nyanja; amisiri ako anakukongoletsa kwambiri.
5 abietibus de Sanir extruxerunt te cum omnibus tabulatis maris: cedrum de Libano tulerunt ut facerent tibi malum.
Anakupanga ndi matabwa a payini ochokera ku Seniri; anatenga mikungudza ya ku Lebanoni kupangira mlongoti wako.
6 Quercus de Basan dolaverunt in remos tuos: et transtra tua fecerunt tibi ex ebore Indico, et prætoriola de insulis Italiæ.
Ndi mitengo ya thundu ya ku Basani anapanga zopalasira zako; ndi matabwa a mitengo ya payini yochokera ku zilumba za Kitimu. Pakuti anapanga thandala lako pakati pa matabwawo panali minyanga ya njovu.
7 Byssus varia de Ægypto texta est tibi in velum ut poneretur in malo: hyacinthus, et purpura de insulis Elisa facta sunt operimentum tuum.
Nsalu yabafuta yopeta yochokera ku Igupto inali thanga yako, ndipo inakhala ngati mbendera. Nsalu zophimba matenti ako zinali za mtundu wamtambo ndi pepo zochokera ku zilumba za Elisa.
8 Habitatores Sidonis, et Aradii fuerunt remiges tui: sapientes tui, Tyre, facti sunt gubernatores tui.
Anthu a ku Sidoni ndi Arivadi ndi amene anali opalasa ako. Anthu aluso ako, iwe Turo, anali mwa iwe ndiwo amene ankakuyendetsa.
9 Senes Giblii, et prudentes eius habuerunt nautas ad ministerium variæ supellectilis tuæ: omnes naves maris, et nautæ earum fuerunt in populo negotiationis tuæ.
Akuluakulu ndi eni luso a ku Gebala anali mʼkati mwako, ngati okonza zibowo zako. Sitima za pa nyanja zonse, ndi oyendetsa ake ankabwera pamodzi ndi katundu kudzachita nawe malonda.
10 Persæ, et Lydii, et Libyes erant in exercitu tuo viri bellatores tui: clypeum, et galeam suspenderunt in te pro ornatu tuo.
“Anthu a ku Perisiya, a ku Ludi ndi Puti anali asilikali mʼgulu lako la nkhondo. Iwo ankapachika zishango ndi zipewa zawo zankhondo pa makoma ako, kubweretsa kwa iwe ulemerero.
11 Filii Aradii cum exercitu tuo erant super muros tuos in circuitu: sed et Pigmæi, qui erant in turribus tuis, pharetras suas suspenderunt in muris tuis per gyrum: ipsi compleverunt pulchritudinem tuam.
Anthu a ku Arivadi ndi Heleki ankalondera mbali zonse za mpanda wako; anthu a ku Gamadi anali mu nsanja zako, Iwo ankapachika zishango zawo pa makoma ako onse. Amenewo ndiwo anakukongoletsa kwambiri.
12 Carthaginenses negotiatores tui, a multitudine cunctarum divitiarum, argento, ferro, stanno, plumboque repleverunt nundinas tuas.
“Dziko la Tarisisi linachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa katundu wako wamtundumtundu. Iwo ankapereka siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.
13 Græcia, Thubal, et Mosoch, ipsi institores tui: mancipia, et vasa ærea advexerunt populo tuo.
“Yavani, Tubala ndi Mesaki ankachita nawe malonda; iwo ankapereka akapolo ndi ziwiya za mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.
14 De domo Thogorma, equos, et equites, et mulos adduxerunt ad forum tuum.
“Anthu a ku Beti Togarima ankapereka akavalo antchito, akavalo ankhondo ndi abulu mosinthanitsa ndi katundu wako.
15 Filii Dedan negotiatores tui: insulæ multæ negotiatio manus tuæ: dentes eburneos, et hebeninos commutaverunt in pretio tuo.
“Anthu a ku Dedani ankachita nawe malonda, ndipo anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja anali ogula malonda ako. Ankakupatsa minyanga ya njovu ndi phingo.
16 Syrus negotiator tuus propter multitudinem operum tuorum, gemmam, et purpuram, et scutulata, et byssum, et sericum, et chodchod proposuerunt in mercatu tuo.
“Anthu a ku Aramu ankachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa zinthu zako. Iwo ankapereka miyala ya emeradi, nsalu zapepo, nsalu zopetapeta, nsalu zabafuta, korali ndi miyala ya rubi mosinthanitsa ndi katundu wako.
17 Iuda et terra Israel ipsi institores tui in frumento primo, balsamum, et mel, et oleum, et resinam proposuerunt in nundinis tuis.
“Yuda ndi Israeli ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka tirigu ochokera ku Miniti ndi zokometsera zakudya, uchi, mafuta ndi mankhwala mosinthanitsa ndi katundu wako.
18 Damascenus negotiator tuus in multitudine operum tuorum, in multitudine diversarum opum, in vino pingui, in lanis coloris optimi.
“Anthu a ku Damasiko, chifukwa cha zinthu zako za malonda zambiri ndi katundu wako wosiyanasiyana, ankachita nawe malonda a vinyo wochokera ku Heliboni ndi ubweya wankhosa ochokera ku Zahari.
19 Dan, et Græcia, et Mosel in nundinis tuis proposuerunt ferrum fabrefactum: stacte, et calamus in negotiatione tua.
Adani ndi Agriki ochokera ku Uzala ankagula katundu wako. Iwo ankapereka chitsulo chosalala, kasiya ndi bango lonunkhira mosinthanitsa ndi katundu wako.
20 Dedan institores tui in tapetibus ad sedendum.
“Anthu a ku Dedani ankakugulitsa nsalu zoyika pa zishalo za akavalo.
21 Arabia, et universi principes Cedar, ipsi negotiatores manus tuæ: cum agnis, et arietibus, et hœdis venerunt ad te negotiatores tui.
“Arabiya ndi mafumu onse a ku Kedara anali ogula malonda ako. Iwo ankachita nawe malonda a ana ankhosa onenepa, nkhosa zazimuna ndi mbuzi.
22 Venditores Saba, et Reema, ipsi negotiatores tui: cum universis primis aromatibus, et lapide pretioso, et auro, quod proposuerunt in mercatu tuo.
“Anthu amalonda a ku Seba ndi Raama ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka zonunkhira zosiyanasiyana zabwino kwambiri, miyala yokongola ndi golide mosinthanitsa ndi katundu wako.
23 Haran, et Chene, et Eden negotiatores tui: Saba, Assur, et Chelmad venditores tui.
“Amalonda a ku Harani, Kane, Edeni, Seba, Asuri ndi Kilimadi ankachita nawe malonda.
24 Ipsi negotiatores tui multifariam involucris hyacinthi, et polymitorum, gazarumque pretiosarum, quæ obvolutæ, et astrictæ erant funibus: cedros quoque habebant in negotiationibus tuis.
Iwowa ankasinthanitsana nawe zovala zokongola, nsalu zopetapeta, zoyala pansi za mawangamawanga, atazimanga bwino ndi zingwe zolimba.
25 Naves maris, principes tui in negotiatione tua: et repleta es, et glorificata nimis in corde maris.
“Sitima za pa madzi za ku Tarisisi zinali zonyamula malonda ako. Motero iwe uli ngati sitima yapamadzi yodzaza ndi katundu wolemera.
26 In aquis multis adduxerunt te remiges tui: ventus auster contrivit te in corde maris.
Anthu opalasa ako amakupititsa pa nyanja yozama. Koma mphepo yakummawa idzakuthyolathyola pakati pa nyanja.
27 Divitiæ tuæ, et thesauri tui, et multiplex instrumentum tuum, nautæ tui et gubernatores tui, qui tenebant supellectilem tuam, et populo tuo præerant: viri quoque bellatores tui, qui erant in te cum universa multitudine tua, quæ est in medio tui: cadent in corde maris in die ruinæ tuæ.
Chuma chako, katundu wako, malonda ako, okuyendetsa ako, okuwongolera ako ndi opanga sitima za pa madzi, anthu ako amalonda ndi asilikali ako onse ndiponso aliyense amene ali mʼmenemo adzamira mʼnyanja tsiku limene udzawonongeka.
28 A sonitu clamoris gubernatorum tuorum conturbabuntur classes:
Madera a mʼmbali mwa nyanja adzagwedezeka chifukwa cha kufuwula kwa oyendetsa sitimawo.
29 Et descendent de navibus suis omnes, qui tenebant remum: nautæ, et universi gubernatores maris in terra stabunt:
Onse amene amapalasa sitima zapamadzi, adzatuluka mʼsitima zawo; oyendetsa ndi onse owongolera sitima zapamadzi adzayimirira mʼmbali mwa nyanja.
30 et eiulabunt super te voce magna, et clamabunt amare: et superiacient pulverem capitibus suis, et cinere conspergentur.
Iwo akufuwula, kukulira iwe kwambiri; akudzithira fumbi kumutu, ndi kudzigubuduza pa phulusa.
31 Et radent super te calvitium, et accingentur ciliciis: et plorabunt te in amaritudine animæ ploratu amarissimo.
Akumeta mpala mitu yawo chifukwa cha iwe ndipo akuvala ziguduli. Akukulira iweyo ndi mitima yowawa kwambiri.
32 Et assument super te carmen lugubre, et plangent te: Quæ est ut Tyrus, quæ obmutuit in medio maris?
Akuyimba nyimbo yokudandaulira nʼkumati: ‘Ndani anawonongedwapo ngati Turo pakati pa nyanja?’
33 Quæ in exitu negotiationum tuarum de mari implesti populos multos: in multitudine divitiarum tuarum, et populorum tuorum ditasti reges terræ.
Pamene malonda ako ankawoloka nyanja unakhutitsa mitundu yambiri ya anthu. Mafumu a dziko lapansi analemera ndi chuma chako komanso ndi malonda ako.
34 Nunc contrita es a mari, in profundis aquarum opes tuæ, et omnis multitudo tua, quæ erat in medio tui, ceciderunt.
Koma tsopano wathyokera mʼnyanja, pansi penipeni pa nyanja. Katundu wako ndi onse amene anali nawe amira pamodzi nawe.
35 Universi habitatores insularum obstupuerunt super te: et reges earum omnes tempestate perculsi mutaverunt vultus.
Onse amene amakhala mʼmbali mwa nyanja aopsedwa ndi zimene zakuchitikira. Mafumu awo akuchita mantha ndipo nkhope zangoti khululu.
36 Negotiatores populorum sibilaverunt super te: ad nihilum deducta es, et non eris usque in perpetuum.
Anthu amalonda a mitundu ina akukunyogodola. Watha mochititsa mantha ndipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.”

< Hiezechielis Prophetæ 27 >