< Exodus 38 >
1 Fecit et altare holocausti de lignis setim, quinque cubitorum per quadrum, et trium in altitudine:
Anapanga guwa lansembe zopsereza lamatabwa amtengo wa mkesha. Linali lofanana mbali zonse. Msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi masentimita 229.
2 cuius cornua de angulis procedebant, operuitque illum laminis æneis.
Anapanga nyanga imodziimodzi pa ngodya zake zinayizo, kotero kuti nyangazo ndi guwalo zinali chinthu chimodzi, ndipo anakuta guwalo ndi mkuwa.
3 Et in usus eius paravit ex ære vasa diversa, lebetes, forcipes, fuscinulas, uncinos, et ignium receptacula.
Anapanganso ziwiya zamkuwa izi zogwirira ntchito pa guwalo: miphika, mafosholo, mabeseni owazira magazi, ngowe zokowera nyama ndi zosonkhezera moto.
4 Craticulamque eius in modum retis fecit æneam, et subter eam in altaris medio arulam,
Anapanga sefa yachitsulo chamkuwa ya guwa lansembelo kuti ikhale mmunsi mwa khoma la guwa lansembelo, kuchokera pansi mpaka pakati pa khoma la guwalo.
5 fusis quattuor annulis per totidem retiaculi summitates, ad immittendos vectes ad portandum:
Anapanga mphete zamkuwa zinayi ndipo anazilumikiza ku ngodya zinayi za sefa ija kuti zigwire nsichi zonyamulira.
6 quos et ipsos fecit de lignis setim, et operuit laminis æneis:
Anapanga nsichi zamtengo wa mkesha ndipo anazikuta ndi mkuwa.
7 induxitque in circulos, qui in lateribus altaris eminebant. Ipsum autem altare non erat solidum, sed cavum ex tabulis, et intus vacuum.
Iwo analowetsa nsichizo mʼmphetemo mbali zonse ziwiri za guwalo kuti azinyamulira. Guwalo linali lamatabwa ndi logoba mʼkati mwake.
8 Fecit et labrum æneum cum basi sua de speculis mulierum, quæ excubabant in ostio tabernaculi.
Anapanga beseni lamkuwa lokhala ndi miyendo yamkuwanso kuchokera ku magalasi oyangʼanira nkhope a amayi amene ankatumikira pa chipata cha tenti ya msonkhano.
9 Fecit et atrium, in cuius australi plaga erant tentoria de bysso retorta, cubitorum centum,
Kenaka anapanga bwalo la chihema. Mbali yakummwera inali yotalika mamita 46 ndipo kunali nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino.
10 columnæ æneæ viginti cum basibus suis, capita columnarum, et tota operis cælatura, argentea.
Anapanganso mizati makumi awiri, matsinde makumi awiri amkuwa ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo.
11 Æque ad septentrionalem plagam tentoria, columnæ, basesque et capita columarum eiusdem mensuræ, et operis ac metalli, erant.
Mbali yakumpoto inalinso yotalika mamita 46 ndipo inali ndi mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo.
12 In ea vero plaga, quæ ad Occidentem respicit, fuerunt tentoria cubitorum quinquaginta, columnæ decem cum basibus suis æneæ, et capita columnarum, et tota operis cælatura, argentea.
Mbali yakumadzulo inali yotalika mamita 23 ndipo inali ndi nsalu yotchinga, mizati khumi ndi matsinde khumi. Inalinso ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo.
13 Porro contra orientem quinquaginta cubitorum paravit tentoria:
Mbali yakummawa, kotulukira dzuwa, inalinso yotalika mamita 23.
14 e quibus, quindecim cubitos columnarum trium, cum basibus suis unum tenebat latus:
Mbali imodzi yachipata kunali nsalu yotchinga yotalika mamita asanu ndi awiri, mizati itatu ndi matsinde atatu,
15 et in parte altera (quia inter utraque introitum tabernaculi fecit) quindecim æque cubitorum erant tentoria, columnæque tres, et bases totidem.
polowera mʼbwalo panali nsalu yotchinga ya mamita asanu ndi awiri pamodzi ndi mizati itatu ndi matsinde atatu.
16 Cuncta atrii tentoria byssus retorta texuerat.
Katani yonse yotchinga kuzungulira chihema inali yofewa, yosalala ndi yolukidwa bwino.
17 Bases columnarum fuere æneæ, capita autem earum cum cunctis cælaturis suis argentea: sed et ipsas columnas atrii vestivit argento.
Matsinde amizati anali amkuwa. Ngowe ndi zingwe za mizati zinali zasiliva, ndipo pamwamba pa mizatiyo anakutapo siliva. Choncho mizati yonse ya bwalolo inalumikizidwa ndi zingwe zasiliva.
18 Et in introitu eius opere plumario fecit tentorium ex hyacintho, purpura, vermiculo, ac bysso retorta, quod habebat viginti cubitos in longitudine, altitudo vero quinque cubitorum erat iuxta mensuram, quam cuncta atrii tentoria habebant.
Nsalu yotchinga ya pa chipata inali yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira, yofewa yosalala ndi yopangidwa ndi anthu aluso. Nsaluyo inali yotalika mamita asanu ndi anayi, molingana ndi nsalu zotchinga bwalo. Msinkhu wake unali masentimita 229,
19 Columnæ autem in ingressu fuere quattuor cum basibus æneis, capitaque earum et cælaturæ argenteæ.
pamodzi ndi mizati yake inayi ndi matsinde amkuwa anayi. Ngowe ndi zingwe zake zinali za siliva, ndipo pamwamba pake pa mzati anakutapo ndi siliva.
20 Paxillos quoque tabernaculi et atrii per gyrum fecit æneos.
Zikhomo za chihema ndi zina zonse zozungulira chihemacho zinali zamkuwa.
21 Hæc sunt instrumena tabernaculi testimonii, quæ enumerata sunt iuxta præceptum Moysi in cæremoniis Levitarum per manum Ithamar filii Aaron sacerdotis:
Chiwerengero cha zipangizo zimene anagwiritsa ntchito popanga chihema, chihema chaumboni, zimene Mose analamulira Alevi kuti alembe motsogozedwa ndi Itamara mwana wa Aaroni, wansembe, chinali ichi:
22 quæ Beseleel filius Uri filii Hur de tribu Iuda, Domino per Moysen iubente, compleverat,
Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huzi wa fuko la Yuda anapanga chilichonse Yehova analamulira Mose,
23 iuncto sibi socio Ooliab filio Achisamech de tribu Dan: qui et ipse artifex lignorum egregius fuit, et polymitarius atque plumarius ex hyacintho, purpura, vermiculo, et bysso.
pamodzi ndi Oholiabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, wa luso la zopangapanga ndi kulemba mapulani, ndi wopanga nsalu zolukidwa bwino za mtundu wa mtambo, yapepo ndi zofiira, zofewa ndi zosalala.
24 Omne aurum quod expensum est in opere Sanctuarii, et quod oblatum est in donariis, viginti novem talentorum fuit, et septingentorum triginta siclorum ad mensuram Sanctuarii.
Golide yense wochokera ku nsembe yoweyula amene anagwiritsa ntchito pa ntchito yonse yopanga malo wopatulika anali wolemera makilogalamu 1,000 potsata miyeso ya kumalo wopatulika.
25 Oblatum est autem ab his qui transierunt ad numerum a viginti annis et supra, de sexcentis tribus millibus, et quingentis quinquaginta, armatorum.
Siliva wochokera ku gulu lonse la anthu anali wolemerera makilogalamu 3,430, potsata miyeso ya ku malo wopatulika.
26 Fuerunt præterea centum talenta argenti, e quibus conflatæ sunt bases Sanctuarii, et introitus ubi velum pendet.
Munthu aliyense amapereka beka imodzi, kufanana ngati makilogalamu 6, potsata muyeso wa ku malo wopatulika. Kuchokera kwa aliyense amene anawerengedwa kuyambira zaka 20 kapena kuposerapo, amuna onse analipo 603,550.
27 Centum bases factæ sunt de talentis centum, singulis talentis per bases singulas supputatis.
Anagwiritsa ntchito siliva wolemera makilogalamu 3,400 kupanga matsinde 100 a ku malo wopatulika ndi makatani, ndipo makilogalamu 34 kupanga tsinde limodzi.
28 De mille autem septingentis, et septuaginta quinque fecit capita columnarum, quas et ipsas vestivit argento.
Makilogalamu otsalawo anagwiritsa ntchito popanga ngowe zamzati kukutira pamwamba pa mizati ndiponso kupanga zingwe zake.
29 Æris quoque oblata sunt talenta septuaginta duo millia, et quadringenti supra sicli,
Mkuwa ochokera ku nsembe yoweyula unali makilogalamu 2,425.
30 ex quibus fusæ sunt bases in introitu tabernaculi testimonii, et altare æneum cum craticula sua, omniaque vasa, quæ ad usum eius pertinent,
Iwo anawugwiritsa ntchito popanga matsinde a pa chipata cha tenti ya msonkhano, guwa la mkuwa pamodzi ndi sefa yake ndiponso ziwiya zonse,
31 et bases atrii tam in circuitu quam in ingressu eius, et paxilli tabernaculi atque atrii, per gyrum.
matsinde ozungulira bwalo ndiponso a pa chipata pake, ndi zikhomo zonse za tentiyo ndi matsinde a malo wozungulirapo.