< Danihelis Prophetæ 10 >

1 Anno tertio Cyri regis Persarum, verbum revelatum est Danieli cognomento Baltassar, et verbum verum, et fortitudo magna: intellexitque sermonem: intelligentia enim est opus in visione.
Chaka chachitatu cha Koresi mfumu ya Aperezi, Danieli amene ankatchedwa Belitesezara analandira mawu a vumbulutso. Uthenga wake unali woona ndipo anawumvetsa movutikira. Uthengawu anawumva kudzera mʼmasomphenya.
2 In diebus illis ego Daniel lugebam trium hebdomadarum diebus,
Pa nthawi imeneyi, ine Danieli ndinalira kwa masabata atatu.
3 panem desiderabilem non comedi, et caro et vinum non introierunt in os meum, sed neque unguento unctus sum: donec complerentur trium hebdomadarum dies.
Sindinadye chakudya chokoma; nyama ndi vinyo sizinakhudze milomo yanga ndi pangʼono pomwe; ndipo sindinadzole mafuta aliwonse mpaka patatha masabata atatu.
4 Die autem vigesima et quarta mensis primi eram iuxta fluvium magnum, qui est Tigris.
Pa tsiku la 24 la mwezi woyamba, nditayima mʼmbali mwa mtsinje waukulu wa Tigirisi,
5 Et levavi oculos meos, et vidi: et ecce vir unus vestitus lineis, et renes eius accincti auro obrizo:
ndinakweza maso ndipo ndinaona kuti pafupi ndi ine panali munthu wochokera ku Ufazi atavala zovala zosalala ndi lamba wa golide woyengeka bwino mʼchiwuno mwake.
6 et corpus eius quasi chrysolithus, et facies eius velut species fulguris, et oculi eius ut lampas ardens: et brachia eius, et quæ deorsum sunt usque ad pedes, quasi species æris candentis: et vox sermonum eius ut vox multitudinis.
Thupi lake linali ngati mwala wonyezimira, nkhope yake ngati chiphaliwali, maso ake ngati muni wowala, manja ndi miyendo yake ngati mkuwa wowala, ndipo mawu ake ngati liwu la chikhamu cha anthu.
7 Vidi autem ego Daniel solus visionem: porro viri, qui erant mecum, non viderunt: sed terror nimius irruit super eos, et fugerunt in absconditum.
Ine Danieli ndinali ndekha pamene ndinaona masomphenyawa; anthu amene anali ndi ine sanawaone, koma anadzazidwa ndi mantha kotero kuti anathawa ndi kukabisala.
8 Ego autem relictus solus vidi visionem grandem hanc: et non remansit in me fortitudo, sed et species mea immutata est in me, et emarcui, nec habui quidquam virium.
Choncho ndinatsala ndekha, ndikuonetsetsa masomphenya a ulemererowa. Ndiye nkhope yanga inasinthika, ndinalefuka, ndipo ndinalibenso mphamvu.
9 Et audivi vocem sermonum eius: et audiens iacebam consternatus super faciem meam, et vultus meus hærebat terræ.
Kenaka ndinamva iye akuyankhula, ndipo pamene ndinkamvetsera, ndinagwa chafufumimba ndi kugona tulo tofa nato.
10 Et ecce manus tetigit me, et erexit me super genua mea, et super articulos manuum mearum.
Dzanja linandikhudza ndi kundinyamula ndipo ndinachita ngati kuwerama pa mawondo manja atagwira pansi.
11 Et dixit ad me: Daniel vir desideriorum, intellige verba, quæ ego loquor ad te, et sta in gradu tuo: nunc enim sum missus ad te. Cumque dixisset mihi sermonem istum, steti tremens.
Iye anati, “Danieli, iwe wokondedwa kwambiri, imirira ndipo uganizire mosamala mawu ndiyankhule kwa iwe, popeza tsopano ndatumidwa kwa iwe.” Atanena izi kwa ine ndinayimirira monjenjemera.
12 Et ait ad me: Noli metuere Daniel: quia ex die primo, quo posuisti cor tuum ad intelligendum ut te affligeres in conspectu Dei tui, exaudita sunt verba tua: et ego veni propter sermones tuos.
Ndipo iye anapitiriza nati, “Usachite mantha Danieli. Kuyambira tsiku loyamba pamene unatsimikiza mtima kuti umvetse zinthuzi ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, pempho lako linamveka ndipo ndabwera kudzayankha mapemphero akowo.
13 Princeps autem regni Persarum restitit mihi viginti et uno diebus: et ecce Michael unus de principibus primis venit in adiutorium meum, et ego remansi ibi iuxta regem Persarum.
Koma mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya ananditchingira pa masiku 21, kenaka Mikayeli, mmodzi mwa angelo akuluakulu anadza kudzandithandiza chifukwa ndinakhala komweko ndi mafumu a ku Peresiya.
14 Veni autem ut docerem te quæ ventura sunt populo tuo in novissimis diebus, quoniam adhuc, visio in dies.
Tsopano ndafika kuti ndidzakufotokozere zimene zidzachitika kwa anthu a mtundu wako kutsogolo. Ndipo pali masomphenya enanso okhudza nthawi imene ikudza.”
15 Cumque loqueretur mihi huiuscemodi verbis, deieci vultum meum ad terram, et tacui.
Pa nthawi yomwe ankanena izi kwa ine, ndinazolika nkhope yanga pansi kusowa chonena.
16 Et ecce quasi similitudo filii hominis tetigit labia mea: et aperiens os meum locutus sum, et dixi ad eum, qui stabat contra me: domine mi, in visione tua dissolutæ sunt compages meæ, et nihil in me remansit virium.
Kenaka wina wa maonekedwe ngati munthu anakhudza milomo yanga, ndipo ndinatsekula pakamwa panga ndi kuyamba kuyankhula. Ndinati kwa amene anayima patsogolo panga, “Ine ndasweka mtima chifukwa cha masomphenyawa mbuye wanga, ndipo ndalefuka.
17 Et quomodo poterit servus domini mei loqui cum domino meo? nihil enim in me remansit virium, sed et halitus meus intercluditur.
Kodi ine mtumiki wamba wa mbuye wanga ndingathe bwanji kuyankhula ndi inu mbuye wanga? Mphamvu zanga zatha, ndipo ndikulephera kupuma.”
18 Rursum ergo tetigit me quasi visio hominis, et confortavit me,
Kenaka wooneka ngati munthu uja anandikhudzanso ndipo anandipatsa mphamvu.
19 et dixit: Noli timere vir desideriorum: pax tibi: confortare, et esto robustus. Cumque loqueretur mecum, convalui, et dixi: Loquere Domine mi, quia confortasti me.
Iye anati, “Usachite mantha, munthu wokondedwa kwambiriwe. Mtendere ukhale ndi Iwe ndipo ukhale wolimba.” Atayankhula nane, ndinalimbikitsidwa ndipo ndinati, “Yankhulani Mbuye wanga, popeza mwandipatsa mphamvu.”
20 Et ait: Numquid scis quare venerim ad te? et nunc revertar ut prœlier adversum principem Persarum; cum ego egrederer, apparuit princeps Græcorum veniens.
Ndipo iye anati, “Kodi ukudziwa chifukwa chimene ndabwerera kwa iwe? Ndiyamba ndabwerera kukamenyana ndi mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya, ndipo ndikakanthana naye, kenaka mtsogoleri wa ufumu wa Grisi adzabwera.
21 Verumtamen annuntiabo tibi quod expressum est in scriptura veritatis: et nemo est adiutor meus in omnibus his, nisi Michael princeps vester.
Koma ndikuwuza zimene zalembedwa mʼbuku la zoona koma palibe wondithandiza kulimbana nawo kupatula Mikayeli, kalonga wako.”

< Danihelis Prophetæ 10 >