< Ii Paralipomenon 5 >
1 Intulit igitur Salomon omnia, quæ voverat David pater suus, argentum, et aurum, et universa vasa posuit in thesauris domus Dei.
Pamene ntchito yonse imene Solomoni anagwira pa Nyumba ya Yehova inatha, anabwera ndi zinthu zonse zimene abambo ake Davide anazipereka; siliva, golide ndi ziwiya. Anaziyika mʼzipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Mulungu.
2 Post quæ congregavit maiores natu Israel, et cunctos principes tribuum, et capita familiarum de filiis Israel in Ierusalem, ut adducerent arcam fœderis Domini de Civitate David, quæ est Sion.
Kenaka Solomoni anasonkhanitsa akuluakulu a Israeli mu Yerusalemu, atsogoleri onse a mafuko ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli, kuti akatenge Bokosi la Chipangano la Yehova ku Ziyoni, mzinda wa Davide.
3 Venerunt itaque ad regem omnes viri Israel in die sollemni mensis septimi.
Ndipo Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa mfumu nthawi ya chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiwiri.
4 Cumque venissent cuncti seniorum Israel, portaverunt Levitæ arcam,
Akuluakulu onse a Israeli atafika, Alevi ananyamula Bokosi la Chipangano,
5 et intulerunt eam, et omnem paraturam tabernaculi. Porro vasa sanctuarii, quæ erant in tabernaculo, portaverunt Sacerdotes cum Levitis.
ndipo anabwera nalo bokosi lija pamodzi ndi tenti ya msonkhano ndi ziwiya zonse zopatulika zimene zinali mʼmenemo. Ansembe ndi Alevi ndiye anazinyamula,
6 Rex autem Salomon, et universus cœtus Israel, et omnes, qui fuerunt congregati ante arcam, immolabant arietes, et boves absque ullo numero: tanta enim erat multitudo victimarum.
ndipo Mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Aisraeli amene anasonkhana naye anali patsogolo pa Bokosi la Chipangano, akupereka nsembe nkhosa zambiri ndi ngʼombe zambiri zosawerengeka.
7 Et intulerunt Sacerdotes arcam fœderis Domini in locum suum, id est, ad oraculum templi, in Sancta sanctorum subter alas cherubim:
Ansembe anafika nalo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼchipinda chamʼkati mwenimweni, Malo Opatulika Kwambiri, ndipo analiyika pansi pa mapiko a Akerubi.
8 ita ut cherubim expanderent alas suas super locum, in quo posita erat arca, et ipsam arcam tegerent cum vectibus suis.
Akerubiwo anatambalitsa mapiko awo pamwamba pa Bokosi la Chipangano ndipo anaphimba bokosilo pamodzi ndi mitengo yonyamulira.
9 Vectium autem, quibus portabatur arca, quia paululum longiores erant, capita parebant ante oraculum: si vero quis paululum fuisset extrinsecus, eos videre non poterat. Fuit itaque arca ibi usque in præsentem diem.
Mitengoyi inali yayitali kwambiri ndipo inkaonekera kunja kwa chipinda chamʼkati cha Malo Opatulika, koma osati kunja kwa Malo Opatulikawo; ndipo mitengoyi ilipo mpaka lero lino.
10 Nihilque erat aliud in arca, nisi duæ tabulæ, quas posuerat Moyses in Horeb, quando legem dedit Dominus filiis Israel egredientibus ex Ægypto.
Mʼbokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iwiri imene Mose anayikamo ku Horebu, kumene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto.
11 Egressis autem sacerdotibus de Sanctuario (omnes enim Sacerdotes, qui ibi potuerant inveniri, sanctificati sunt: nec adhuc in illo tempore vices, et ministeriorum ordo inter eos divisus erat)
Kenaka ansembe anatulukamo mʼMalo Opatulika. Ansembe onse amene anali mʼmenemo anali atadziyeretsa posayangʼaniranso magulu awo ochokera.
12 tam Levitæ quam cantores, id est, et qui sub Asaph erant, et qui sub Eman, et qui sub Idithun, filii, et fratres eorum vestiti byssinis, cymbalis, et psalteriis, et citharis concrepabant, stantes ad Orientalem plagam altaris, et cum eis sacerdotes centum viginti canentes tubis.
Alevi onse amene anali oyimba: Asafu, Hemani, Yedutuni ndi ana ndiponso abale awo, amayima mbali ya kummawa kwa guwa lansembe atavala zovala zofewa zosalala akuyimba ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe. Ansembe onse amene amayimba malipenga analipo 120 pamodzi.
13 Igitur cunctis pariter, et tubis, et voce, et cymbalis, et organis, et diversi generis musicorum concinentibus, et vocem in sublime tollentibus; longe sonitus audiebatur, ita ut cum Dominum laudare cœpissent et dicere: Confitemini Domino quoniam bonus, quoniam in æternum misericordia eius; impleretur domus Dei nube,
Oyimba malipenga ndi oyimba nyimbo aja amayimba mogwirizana, monga liwu la munthu mmodzi, kutamanda ndi kuyamika Yehova. Mogwirizana ndi malipenga, ziwaya zamalipenga ndi zida zina, anakweza mawu awo motamanda Yehova poyimba kuti, “Yehova ndi wabwino; chikondi chake chikhala mpaka muyaya.” Ndipo Nyumba ya Mulungu wa Yehova inadzaza ndi mtambo,
14 nec possent Sacerdotes stare et ministrare propter caliginem. Compleverat enim gloria Domini domum Dei.
choncho ansembe sanathe kugwira ntchito yawo chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza Nyumba ya Mulungu.