< Liber Numeri 18 >
1 Dixitque Dominus ad Aaron: Tu, et filii tui, et domus patris tui tecum, portabitis iniquitatem sanctuarii: et tu et filii tui simul sustinebitis peccata sacerdotii vestri.
Yehova anawuza Aaroni kuti, “Iwe, ana ako aamuna ndi banja la abambo ako mudzasenza tchimo la malo wopatulika, koma iwe ndi ana ako aamuna okha mudzasenza tchimo lokhudza unsembe wanu.
2 Sed et fratres tuos de tribu Levi, et sceptrum patris tui sume tecum, præstoque sint, et ministrent tibi: tu autem et filii tui ministrabitis in tabernaculo testimonii.
Ubweretse Alevi, abale ako, kuchokera ku fuko la abambo ako kuti azikhala ndi iwe ndi kumakuthandiza pamodzi ndi ana ako amuna pamene mukutumikira mu tenti ya umboni.
3 Excubabuntque Levitæ ad præcepta tua, et ad cuncta opera tabernaculi: ita dumtaxat ut ad vasa sanctuarii et ad altare non accedant, ne et illi moriantur, et vos pereatis simul.
Iwowo azikutumikirani ndipo azichita ntchito zonse za ku tenti, koma asamafike pafupi ndi zipangizo za ku malo opatulika kapena guwa lansembe, kuopa kuti iwo ndi inu mungafe.
4 Sint autem tecum, et excubent in custodiis tabernaculi, et in omnibus cæremoniis ejus. Alienigena non miscebitur vobis.
Azikhala ndi inu ndipo azisamalira ntchito yonse ya mu tenti ya msonkhano koma munthu wina aliyense wapadera sayenera kufika pafupi nanu.
5 Excubate in custodia sanctuarii, et in ministerio altaris: ne oriatur indignatio super filios Israël.
“Inuyo muzisamalira malo wopatulika ndi guwa lansembe, kuti ukali wa Yehova usawagwerenso Aisraeli.
6 Ego dedi vobis fratres vestros Levitas de medio filiorum Israël, et tradidi donum Domino, ut serviant in ministeriis tabernaculi ejus.
Ine mwini ndasankha Alevi, abale ako, pakati pa Aisraeli ngati mphatso yako ndipo aperekedwa kwa Yehova kuti azigwira ntchito ku tenti ya msonkhano.
7 Tu autem et filii tui custodite sacerdotium vestrum: et omnia quæ ad cultum altaris pertinent, et intra velum sunt, per sacerdotes administrabuntur: si quis externus accesserit, occidetur.
Koma iwe wekha ndi ana ako aamuna muzitumikira ngati ansembe ndi zina zonse zokhudza pa guwa lansembe ndi za mʼkati mwa malo wopatulika kwambiri. Ndikukupatsani mphatso ya utumiki wa unsembe. Aliyense woyandikira malo wopatulika ayenera kuphedwa.
8 Locutusque est Dominus ad Aaron: Ecce dedi tibi custodiam primitiarum mearum. Omnia quæ sanctificantur a filiis Israël, tradidi tibi et filiis tuis pro officio sacerdotali legitima sempiterna.
“Kenaka Yehova anati kwa Aaroni, ona, Ine mwini ndikukuyika kuti ukhale woyangʼanira zopereka zobwera kwa Ine; zopereka zonse zopatulika za Aisraeli zimene amapereka kwa ine ndi kuzipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ngati gawo lanu la nthawi zonse.
9 Hæc ergo accipies de his, quæ sanctificantur et oblata sunt Domino. Omnis oblatio, et sacrificium, et quidquid pro peccato atque delicto redditur mihi, et cedit in Sancta sanctorum, tuum erit, et filiorum tuorum.
Uzilandiranso gawo la zopereka zopatulika kwambiri zomwe sizinawotchedwe pa moto. Kuchokera pa mphatso zonse zimene amabweretsa kwa Ine ngati zopatulika kwambiri, nsembe zachakudya kapena nsembe zopepesera machimo, gawo limenelo ndi lako ndi ana ako aamuna.
10 In sanctuario comedes illud: mares tantum edent ex eo, quia consecratum est tibi.
Muzidya zimenezo ngati zinthu zopatulika kwambiri; mwamuna aliyense adyeko. Uzitenge kukhala zopatulika.
11 Primitias autem, quas voverint et obtulerint filii Israël, tibi dedi, et filiis tuis, ac filiabus tuis, jure perpetuo: qui mundus est in domo tua, vescetur eis.
“Izinso ndi zako: chilichonse chopatulidwa kuchokera ku mphatso zoweyula za Aisraeli ndapereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lako la nthawi zonse. Aliyense wa mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa monga mwa mwambo angathe kudyako.
12 Omnem medullam olei, et vini, ac frumenti, quidquid offerunt primitiarum Domino, tibi dedi.
“Ndikukupatsani mafuta onse abwino kwambiri a olivi ndi vinyo yense watsopano wabwino kwambiri ndi tirigu yense zomwe Aisraeli amapereka kwa Yehova ngati zipatso zoyamba pa zokolola zawo.
13 Universa frugum initia, quas gignit humus, et Domino deportantur, cedent in usus tuos: qui mundus est in domo tua, vescetur eis.
Zipatso zonse zoyamba kucha za mʼdziko lawo zomwe amapereka kwa Yehova zidzakhala zako. Aliyense mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa angathe kudyako.
14 Omne quod ex voto reddiderint filii Israël, tuum erit.
“Chilichonse mu Israeli chomwe chapatulidwira Yehova ndi chako.
15 Quidquid primum erumpit e vulva cunctæ carnis, quam offerunt Domino, sive ex hominibus, sive de pecoribus fuerit, tui juris erit: ita dumtaxat ut pro hominis primogenito pretium accipias, et omne animal quod immundum est redimi facias,
Chilichonse choyamba kubadwa kwa munthu kaya nyama, chomwe chaperekedwa kwa Yehova ndi chako. Koma uyenera kuwombola mwana aliyense wamwamuna ndi mwana aliyense woyamba wa nyama zodetsedwa.
16 cujus redemptio erit post unum mensem, siclis argenti quinque, pondere sanctuarii. Siclus viginti obolos habet.
Pamene zili ndi mwezi umodzi wa kubadwa, uziwombole pa mtengo wowombolera wa ndalama zisanu zasiliva, monga mwa ndalama za ku malo wopatulika.
17 Primogenitum autem bovis, et ovis, et capræ, non facies redimi, quia sanctificata sunt Domino. Sanguinem tantum eorum fundes super altare, et adipes adolebis in suavissimum odorem Domino.
“Koma usawombole ana oyamba kubadwa a ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi. Iwo ndi opatulika. Uwaze magazi a nyamazi pa guwa lansembe ndi kutentha mafuta ake ngati nsembe yotentha ndi moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova.
18 Carnes vero in usum tuum cedent, sicut pectusculum consecratum, et armus dexter: tua erunt.
Nyama yake ikhale yanu monga momwe chimakhalira chidale cha nsembe yoweyula ndi ntchafu za miyendo ya kumanja, zonsezi ndi zako.
19 Omnes primitias sanctuarii, quas offerunt filii Israël Domino, tibi dedi, et filiis, ac filiabus tuis, jure perpetuo. Pactum salis est sempiternum coram Domino, tibi ac filiis tuis.
Zonse zimene mwazichotsa ku zopereka zoyera zomwe Aisraeli anapereka kwa Yehova ndazipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lanu nthawi zonse. Ili ndi pangano losatha la mchere pamaso pa Yehova kwa iwe ndi ana ako.”
20 Dixitque Dominus ad Aaron: In terra eorum nihil possidebitis, nec habebitis partem inter eos: ego pars et hæreditas tua in medio filiorum Israël.
Ndipo Yehova anati kwa Aaroni, “Iweyo sudzakhala ndi cholowa mʼdziko lawo, ndiponso sudzalandira gawo lililonse pakati pawo. Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisraeli.
21 Filiis autem Levi dedi omnes decimas Israëlis in possessionem, pro ministerio, quo serviunt mihi in tabernaculo fœderis:
“Taonani, ndawapatsa Alevi chakhumi chonse mu Israeli ngati cholowa chawo chifukwa cha ntchito ya ku tenti ya msonkhano.
22 ut non accedant ultra filii Israël ad tabernaculum, nec committant peccatum mortiferum,
Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo Aisraeli asamapite pafupi ndi tenti ya msonkhano. Ngati atero adzasenza zotsatira za tchimo lawo ndipo adzafa.
23 solis filiis Levi mihi in tabernaculo servientibus, et portantibus peccata populi. Legitimum sempiternum erit in generationibus vestris. Nihil aliud possidebunt,
Alevi ndi amene azidzagwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano ndipo adzalangidwa chilichonse chikalakwika. Ili ndi lamulo losatha kwa mibado yawo yonse. Iwowo sadzalandira cholowa pakati pa Aisraeli.
24 decimarum oblatione contenti, quas in usus eorum et necessaria separavi.
Mʼmalo mwake, ndikuwapatsa Aleviwo chakhumi ngati cholowa chawo chimene Aisraeli amapereka kwa Yehova. Nʼchifukwa chake zokhudza iwo ndinati: ‘Sadzakhala ndi cholowa pakati pa Aisraeli.’”
25 Locutusque est Dominus ad Moysen, dicens:
Yehova anati kwa Mose,
26 Præcipe Levitis, atque denuntia: Cum acceperitis a filiis Israël decimas, quas dedi vobis, primitias earum offerte Domino, id est, decimam partem decimæ,
“Yankhula ndi Alevi ndi kunena nawo kuti, ‘Pamene mulandira chakhumi kuchoka kwa Aisraeli chimene ndimakupatsani ngati cholowa chanu, muyenera kupereka chakhumi cha choperekacho kwa Yehova.
27 ut reputetur vobis in oblationem primitivorum, tam de areis quam de torcularibus:
Chopereka chanucho chidzawerengedwa kwa inu ngati tirigu wochokera kopunthira kapena ngati mphesa zopsinya kuchokera kopsinyira mphesa.
28 et universis quorum accipitis primitias, offerte Domino, et date Aaron sacerdoti.
Mwa njira imeneyi inunso muzipereka chopereka kwa Yehova kuchokera ku chakhumi chanu chilichonse chimene mumalandira kuchokera kwa Aisraeli. Kuchokera ku chakhumicho muziperekako gawo la Yehova kwa Aaroni, wansembe.
29 Omnia quæ offeretis ex decimis, et in donaria Domini separabitis, optima et electa erunt.
Muyenera kupereka monga gawo la Yehova magawo abwino kwambiri ndi opatulika a chilichonse chimene chapatsidwa kwa inu.’
30 Dicesque ad eos: Si præclara et meliora quæque obtuleritis ex decimis, reputabitur vobis quasi de area, et torculari dederitis primitias:
“Nena kwa Alevi: ‘Pamene mupereka gawo labwino lopambana zonse, gawo limenelo lidzawerengedwa kwa inu ngati lochokera popunthira tirigu kapenanso kopsinyira mphesa.
31 et comedetis eas in omnibus locis vestris, tam vos quam familiæ vestræ: quia pretium est pro ministerio, quo servitis in tabernaculo testimonii.
Inu ndi a pa banja panu mungathe kudyera zimenezi paliponse chifukwa ndi malipiro a ntchito yanu ya ku tenti ya msonkhano.
32 Et non peccabitis super hoc, egregia vobis et pinguia reservantes, ne polluatis oblationes filiorum Israël, et moriamini.
Popereka gawo labwino kwambirilo simudzapezeka olakwa. Mukatero simudzadetsa zopereka zoyera za Aisraeli, ndipo simudzafa.’”