< Jeremiæ 44 >
1 Verbum quod factum est per Jeremiam ad omnes Judæos qui habitabant in terra Ægypti, habitantes in Magdalo, et in Taphnis, et in Memphis, et in terra Phatures, dicens:
Uthenga umene Yeremiya analandira wonena za Ayuda onse amene ankakhala ku Igupto, ku mizinda ya Migidoli, Tapanesi ndi Mefisi, ndiponso ku Patirosi ndi uwu:
2 Hæc dicit Dominus exercituum, Deus Israël: Vos vidistis omne malum istud quod adduxi super Jerusalem, et super omnes urbes Juda: et ecce desertæ sunt hodie, et non est in eis habitator,
“Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Inu mwaona mavuto aakulu amene ndinawabweretsa pa Yerusalemu ndi mizinda yonse ya Yuda. Lero mizinda yonseyo yasanduka mabwinja, yopanda munthu wokhalamo.
3 propter malitiam quam fecerunt ut me ad iracundiam provocarent, et irent ut sacrificarent, et colerent deos alienos quos nesciebant, et illi, et vos, et patres vestri.
Zimenezi zinachitika chifukwa cha zoyipa zomwe anachita. Iwo anaputa mkwiyo wanga pofukiza lubani ndi potumikira milungu ina imene iwo kapena inu ngakhalenso makolo anu sanayidziwe.
4 Et misi ad vos omnes servos meos prophetas, de nocte consurgens, mittensque et dicens: Nolite facere verbum abominationis hujuscemodi, quam odivi.
Kawirikawiri Ine ndakhala ndikutuma atumiki anga, aneneri, amene anati, ‘Musachite chinthu chonyansachi chimene Ine ndimadana nacho!’
5 Et non audierunt, nec inclinaverunt aurem suam, ut converterentur a malis suis, et non sacrificarent diis alienis.
Koma iwo sanamvere kapena kulabadira; sanatembenuke kusiya zoyipa zawo kapena kuleka kufukiza lubani kwa milungu ina.
6 Et conflata est indignatio mea et furor meus, et succensa est in civitatibus Juda, et in plateis Jerusalem: et versæ sunt in solitudinem et vastitatem secundum diem hanc.
Nʼchifukwa chake mkwiyo wanga unayaka ngati moto kutentha mizinda ya ku Yuda ndi misewu ya mu Yerusalemu ndi kuyisandutsa bwinja mpaka lero.
7 Et nunc hæc dicit Dominus exercituum, Deus Israël: Quare vos facitis malum grande hoc contra animas vestras, ut intereat ex vobis vir et mulier, parvulus et lactens, de medio Judæ, nec relinquatur vobis quidquam residuum:
“Ndiye tsopano Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena kuti, ‘Chifukwa chiyani mukufuna kudziwononga chotere? Kodi mukufuna kuti amuna, akazi, ana ndi makanda onse aphedwe ndi kuti mu Yuda musatsale ndi munthu mmodzi yemwe?
8 provocantes me in operibus manuum vestrarum, sacrificando diis alienis in terra Ægypti, in quam ingressi estis ut habitetis ibi: et dispereatis, et sitis in maledictionem et in opprobrium cunctis gentibus terræ?
Chifukwa chiyani mukuputa mkwiyo wanga popembedza mafano pofukiza lubani kwa milungu ina mʼdziko lino la Igupto mʼmene mukukhalamo. Kodi mukuchita zimenezi kuti mudziwononge nokha ndi kuti mudzisandutse chinthu choseketsa ndi chonyozeka pakati pa mitundu yonse ya dziko lapansi?
9 Numquid obliti estis mala patrum vestrorum, et mala regum Juda, et mala uxorum ejus, et mala vestra, et mala uxorum vestrarum, quæ fecerunt in terra Juda, et in regionibus Jerusalem?
Kodi mwayiwala zoyipa zimene anachita makolo anu, mafumu a ku Yuda ndi akazi awo, ndiponso zoyipa zimene munachita inuyo ndi akazi anu mʼdziko la Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu?
10 Non sunt mundati usque ad diem hanc: et non timuerunt, et non ambulaverunt in lege Domini, et in præceptis meis quæ dedi coram vobis et coram patribus vestris.
Koma mpaka lero simunalape. Simunandilemekeze kapena kumvera malamulo anga amene ndinayikira inuyo ndi makolo anu.
11 Ideo hæc dicit Dominus exercituum, Deus Israël: Ecce ego ponam faciem meam in vobis in malum: et disperdam omnem Judam.
“Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, ‘Ine ndatsimikiza zobweretsa mavuto pa inu ndi kuwatheratu anthu a ku Yuda.
12 Et assumam reliquias Judæ, qui posuerunt facies suas ut ingrederentur terram Ægypti, et habitarent ibi, et consumentur omnes in terra Ægypti: cadent in gladio, et in fame, et consumentur a minimo usque ad maximum: in gladio et in fame morientur, et erunt in jusjurandum, et in miraculum, et in maledictionem, et in opprobrium.
Ndidzatenga anthu otsala a ku Yuda amene atsimikiza zopita ku Igupto ndi kukakhala kumeneko. Onse adzathera ku Igupto. Adzaphedwa ndi lupanga kapena kufa ndi njala. Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, adzaphedwa ndi lupanga kapena kufa ndi njala. Adzasanduka chinthu chotembereredwa ndi chochititsa mantha, chinthu choseketsa ndi chonyozeka.
13 Et visitabo super habitatores terræ Ægypti sicut visitavi super Jerusalem, in gladio, et fame, et peste:
Ndidzalanga Ayuda okhala ku Igupto ndi lupanga, njala ndi mliri, ngati mmene ndinalangira anthu a ku Yerusalemu.
14 et non erit qui effugiat, et sit residuus de reliquiis Judæorum qui vadunt ut peregrinentur in terra Ægypti, et revertantur in terram Juda, ad quam ipsi elevant animas suas ut revertantur, et habitent ibi: non revertentur, nisi qui fugerint.
Motero mwa anthu amene anapita ku Igupto palibe ndi mmodzi yemwe adzapulumuke, kapena kukhala ndi moyo, kapena kubwerera ku Yuda. Palibe amene adzabwerere kupatula othawa nkhondo.’”
15 Responderunt autem Jeremiæ omnes viri scientes quod sacrificarent uxores eorum diis alienis, et universæ mulieres quarum stabat multitudo grandis, et omnis populus habitantium in terra Ægypti in Phatures, dicentes:
Tsono amuna onse amene anadziwa kuti akazi awo ankafukiza lubani kwa milungu ina, ndiponso akazi onse amene anali pamenepo, gulu lalikulu la anthu, pamodzi ndi anthu onse amene amakhala ku Patirosi mʼdziko la Igupto, anati kwa Yeremiya,
16 Sermonem quem locutus es ad nos in nomine Domini, non audiemus ex te:
“Ife sitimvera uthenga umene watiwuza mʼdzina la Yehova!
17 sed facientes faciemus omne verbum quod egredietur de ore nostro, ut sacrificemus reginæ cæli, et libemus ei libamina, sicut fecimus nos et patres nostri, reges nostri et principes nostri, in urbibus Juda, et in plateis Jerusalem: et saturati sumus panibus, et bene nobis erat, malumque non vidimus.
Koma tidzachitadi chilichonse chimene tinanena kuti tidzachita: Tidzafukiza lubani kwa mfumukazi yakumwamba ndipo tidzayipatsa nsembe yachakumwa ngati mmene tinkachitira ifeyo ndi makolo athu, mafumu athu ndi akuluakulu mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu. Nthawi imeneyo ife tinali ndi chakudya chochuluka ndipo tinali pabwino, sitimapeza mavuto.
18 Ex eo autem tempore quo cessavimus sacrificare reginæ cæli, et libare ei libamina, indigemus omnibus, et gladio et fame consumpti sumus.
Koma kuchokera nthawi imene tinasiya kufukiza lubani ndi kupereka chopereka cha chakumwa kwa mfumukazi yakumwamba, ifeyo takhala tikusowa zinthu ndipo takhala tikuphedwa ndi lupanga ndi kufa ndi njala.”
19 Quod si nos sacrificamus reginæ cæli, et libamus ei libamina, numquid sine viris nostris fecimus ei placentas ad colendum eam, et libandum ei libamina?
Akazi anawonjezera kunena kuti, “Pamene tinkafukiza lubani kwa mfumukazi yakumwamba ndi kuyipatsa chopereka cha chakumwa, kodi suja amuna athu ankavomereza mmene timayipangira mfumukazi yakumwambayo makeke abwino olembapo chinthunzi chake ndi kuyipatsa chopereka cha chakumwa?”
20 Et dixit Jeremias ad omnem populum, adversum viros, et adversum mulieres, et adversum universam plebem, qui responderant ei verbum, dicens:
Yeremiya atamva kuyankha kumeneku anawawuza kuti,
21 Numquid non sacrificium quod sacrificastis in civitatibus Juda, et in plateis Jerusalem, vos et patres vestri, reges vestri, et principes vestri, et populus terræ, horum recordatus est Dominus, et ascendit super cor ejus?
“Kodi mukuganiza kuti Yehova nʼkuyiwala kuti inuyo ndi makolo anu, mafumu anu ndi akuluakulu anu, ndiponso anthu onse, munkafukiza lubani kwa mafano a mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu?
22 Et non poterat Dominus ultra portare propter malitiam studiorum vestrorum, et propter abominationes quas fecistis: et facta est terra vestra in desolationem, et in stuporem, et in maledictum, eo quod non sit habitator, sicut est dies hæc.
Ndiye Yehova sakanathanso kupirira ndi machitidwe anu ndi zonyansa zimene munkachita. Nʼchifukwa chake dziko lanu linasanduka chipululu, chinthu choopsa ndi chotembereredwa. Dziko lopandamo anthu monga zilili lero lino.
23 Propterea quod sacrificaveritis idolis, et peccaveritis Domino, et non audieritis vocem Domini, et in lege, et in præceptis, et in testimoniis ejus non ambulaveritis, idcirco evenerunt vobis mala hæc, sicut est dies hæc.
Mavuto awa akugwerani chifukwa munkafukiza lubani ndipo munkachimwira Yehova pokana kumvera mawu ake ndi kutsatira malamulo ndi malangizo ake.”
24 Dixit autem Jeremias ad omnem populum, et ad universas mulieres: Audite verbum Domini, omnis Juda qui estis in terra Ægypti.
Kenaka Yeremiya anawuza anthu onse, makamaka akazi kuti, “Imvani mawu a Yehova, anthu onse a ku Yuda amene muli mu Igupto.
25 Hæc inquit Dominus exercituum, Deus Israël, dicens: Vos et uxores vestræ locuti estis ore vestro, et manibus vestris implestis, dicentes: Faciamus vota nostra quæ vovimus, ut sacrificemus reginæ cæli, et libemus ei libamina. Implestis vota vestra, et opere perpetrastis ea.
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Inu ndi akazi anu munalonjeza ndi pakamwa panu, ndipo malonjezowo mwakwaniritsa. Inu munanena kuti, ‘Tidzachita zimene tinalonjeza, kufukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuyipatsa chopereka cha zakumwa.’ Tsopano chitanitu zimene munalonjezazo! Kwaniritsani malumbiro anu. “Yambani, chitani zimene munalonjeza! Kwaniritsani malumbiro anu!
26 Ideo audite verbum Domini, omnis Juda qui habitatis in terra Ægypti: Ecce ego juravi in nomine meo magno, ait Dominus, quia nequaquam ultra vocabitur nomen meum ex ore omnis viri Judæi, dicentis: Vivit Dominus Deus, in omni terra Ægypti.
Koma imvani mawu a Yehova, inu Ayuda nonse amene mukukhala mu Igupto: Yehova akuti, ‘Ine ndikulumbira mʼdzina langa lopambana kuti palibe wochokera ku Yuda amene akukhala mu Igupto amene adzatchule dzina langa polumbira kuti, ‘Pali Ambuye Yehova wamoyo.’
27 Ecce ego vigilabo super eos in malum, et non in bonum: et consumentur omnes viri Juda qui sunt in terra Ægypti gladio et fame, donec penitus consumantur.
Pakuti ndionetsetsa kuti ndiwachitire choyipa, osati chabwino. Anthu a ku Yuda amene akukhala ku Igupto adzaphedwa pa nkhondo. Ena adzafa ndi njala mpaka onse atatheratu.
28 Et qui fugerint gladium, revertentur de terra Ægypti in terram Juda viri pauci: et scient omnes reliquiæ Juda, ingredientium terram Ægypti ut habitent ibi, cujus sermo compleatur, meus an illorum.
Amene adzapulumuke ku lupanga ndi kubwerera ku dziko la Yuda kuchokera ku Igupto adzakhala ochepa kwambiri. Choncho otsala onse a ku Yuda amene anapita kukakhala ku Igupto adzadziwa kuti mawu woona ndi ati, anga kapena awo.
29 Et hoc vobis signum, ait Dominus, quod visitem ego super vos in loco isto, ut sciatis quia vere complebuntur sermones mei contra vos in malum:
“Ine Yehova ndikukupatsani chizindikiro chakuti ndidzakulangani ku malo ano. Motero mudzadziwa kuti mawu anga akuti ndidzakulangani ndi woona.
30 hæc dicit Dominus: Ecce ego tradam Pharaonem Ephree regem Ægypti in manu inimicorum ejus, et in manu quærentium animam illius, sicut tradidi Sedeciam regem Juda in manu Nabuchodonosor regis Babylonis inimici sui, et quærentis animam ejus.
Yehova akuti, ‘Ine ndidzamupereka Farao Hofira mfumu ya Igupto kwa adani ake amene akufuna kumupha, monga momwe ndinaperekera Zedekiya mfumu ya Yuda kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, mdani wake amene ankafuna kumupha.’”