< Genesis 35 >
1 Interea locutus est Deus ad Jacob: Surge, et ascende Bethel, et habita ibi, facque altare Deo qui apparuit tibi quando fugiebas Esau fratrem tuum.
Tsono Mulungu anati kwa Yakobo, “Nyamuka uchoke kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ukamange guwa lansembe la Mulungu amene anadza kwa iwe pamene umathawa Esau, mʼbale wako.”
2 Jacob vero convocata omni domo sua, ait: Abjicite deos alienos qui in medio vestri sunt, et mundamini, ac mutate vestimenta vestra.
Choncho Yakobo anawuza a pa banja pake ndi onse amene anali naye kuti, “Chotsani milungu yachilendo imene muli nayo, ndipo mudziyeretse nokha ndi kusintha zovala zanu.
3 Surgite, et ascendamus in Bethel, ut faciamus ibi altare Deo: qui exaudivit me in die tribulationis meæ, et socius fuit itineris mei.
Tiyeni tinyamuke kuchoka kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ndikamumangira guwa lansembe Mulungu amene anandithandiza pa nthawi za masautso anga, komanso amene wakhala nane mʼmayendedwe anga onse.”
4 Dederunt ergo ei omnes deos alienos quos habebant, et inaures quæ erant in auribus eorum: at ille infodit ea subter terebinthum, quæ est post urbem Sichem.
Choncho anamupatsa Yakobo milungu yachilendo yonse imene anali nayo pamodzi ndi ndolo. Iye anazikwirira pansi pa mtengo wa thundu ku Sekemu.
5 Cumque profecti essent, terror Dei invasit omnes per circuitum civitates, et non sunt ausi persequi recedentes.
Pamenepo ananyamuka, ndipo mtima woopa Mulungu unagwera anthu onse a mʼmizinda yozungulira, kotero kuti palibe aliyense amene anatsatira banja la Yakobo.
6 Venit igitur Jacob Luzam, quæ est in terra Chanaan, cognomento Bethel: ipse et omnis populus cum eo.
Yakobo ndi anthu onse anali naye aja anafika ku Luzi (ku Beteli) mu dziko la Kanaani.
7 Ædificavitque ibi altare, et appellavit nomen loci illius, Domus Dei: ibi enim apparuit ei Deus cum fugeret fratrem suum.
Kumeneko anamanga guwa lansembe nalitcha Eli Beteli, chifukwa kunali kumeneko kumene Mulungu anadziwulula yekha kwa Yakobo pamene ankathawa mʼbale wake.
8 Eodem tempore mortua est Debora nutrix Rebeccæ, et sepulta est ad radices Bethel subter quercum: vocatumque est nomen loci illius, Quercus fletus.
Debora mlezi wa Rakele anamwalira komweko nayikidwa mʼmanda pansi pa mtengo wa thundu cha kumunsi kwa Beteli. Choncho panatchedwa Aloni-Bakuti (mtengo wamaliro).
9 Apparuit autem iterum Deus Jacob postquam reversus est de Mesopotamia Syriæ, benedixitque ei
Yakobo atabwera kuchokera ku Padanaramu, Mulungu anabweranso kwa iye namudalitsa.
10 dicens: Non vocaberis ultra Jacob, sed Israël erit nomen tuum. Et appellavit eum Israël,
Mulungu anati kwa iye, “Dzina lako ndiwe Yakobo, koma sudzatchedwanso Yakobo; koma udzatchedwa Israeli.” Choncho anamutcha iye Israeli.
11 dixitque ei: Ego Deus omnipotens: cresce, et multiplicare: gentes et populi nationum ex te erunt, reges de lumbis tuis egredientur,
Ndipo Mulungu anati kwa iye, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse; berekanani ndi kuchulukana. Mtundu wa anthu, inde, mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe, ndipo ena mwa zidzukulu zako adzakhala mafumu.
12 terramque quam dedi Abraham et Isaac, dabo tibi et semini tuo post te.
Dziko limene ndinapereka kwa Abrahamu ndi Isake ndiliperekanso kwa iwe. Lidzakhala lako ndi la zidzukulu zako.”
Kenaka Mulungu anamusiya Yakobo.
14 Ille vero erexit titulum lapideum in loco quo locutus fuerat ei Deus: libans super eum libamina, et effundens oleum:
Yakobo anayika mwala wachikumbutso pa malo pamene Mulungu anayankhula naye paja. Iye anathirapo nsembe yachakumwa ndi yamafuta.
15 vocansque nomen loci illius Bethel.
Yakobo anawatcha malo amene Mulungu anayankhula naye aja kuti Beteli.
16 Egressus autem inde, venit verno tempore ad terram quæ ducit Ephratam: in qua cum parturiret Rachel,
Kenaka anachoka ku Beteli. Koma ali pafupi kufika ku Efurata nthawi yakuti Rakele aone mwana inakwana. Iye anavutika pobereka.
17 ob difficultatem partus periclitari cœpit. Dixitque ei obstetrix: Noli timere, quia et hunc habebis filium.
Akanali chivutikire choncho, mzamba anamulimbikitsa nati, “Usaope pakuti ubala mwana wina wamwamuna.”
18 Egrediente autem anima præ dolore, et imminente jam morte, vocavit nomen filii sui Benomi, id est, Filius doloris mei: pater vero appellavit eum Benjamin, id est, Filius dextræ.
Tsono pamene Rakele ankapuma wefuwefu (popeza ankamwalira) iye anatcha mwana uja kuti Beni-Oni. Koma abambo ake anamutcha kuti Benjamini.
19 Mortua est ergo Rachel, et sepulta est in via quæ ducit Ephratam, hæc est Bethlehem.
Choncho Rakele anamwalira ndipo anayikidwa pa njira yopita ku Efurata (Kumeneko ndiye ku Betelehemu).
20 Erexitque Jacob titulum super sepulchrum ejus: hic est titulus monumenti Rachel, usque in præsentem diem.
Pa manda ake, Yakobo anayimika mwala wachikumbutso wa pa manda ndipo ulipobe mpaka lero.
21 Egressus inde, fixit tabernaculum trans Turrem gregis.
Israeli (Yakobo) anasunthanso nakamanga tenti yake kupitirira nsanja ya Ederi.
22 Cumque habitaret in illa regione, abiit Ruben, et dormivit cum Bala concubina patris sui: quod illum minime latuit. Erant autem filii Jacob duodecim.
Israeli akanali mʼderali, Rubeni anapita nakagonana ndi Biliha, mdzakazi wa abambo ake. Yakobo uja anazimva zimenezi. Yakobo anali ndi ana aamuna khumi ndi awiri:
23 Filii Liæ: primogenitus Ruben, et Simeon, et Levi, et Judas, et Issachar, et Zabulon.
Ana a Leya ndi awa: Rubeni anali mwana woyamba wa Yakobo, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, ndi Zebuloni.
24 Filii Rachel: Joseph et Benjamin.
Ana a Rakele ndi awa: Yosefe ndi Benjamini.
25 Filii Balæ ancillæ Rachelis: Dan et Nephthali.
Ana a Biliha, wantchito wa Rakele ndi awa: Dani ndi Nafutali.
26 Filii Zelphæ ancillæ Liæ: Gad et Aser: hi sunt filii Jacob, qui nati sunt ei in Mesopotamia Syriæ.
Ana a Zilipa wantchito wa Leya ndi awa: Gadi ndi Aseri. Awa ndiwo ana a Yakobo amene anabadwira ku Padanaramu.
27 Venit etiam ad Isaac patrem suum in Mambre, civitatem Arbee, hæc est Hebron, in qua peregrinatus est Abraham et Isaac.
Yakobo anafika ku mudzi kwa abambo ake Isake ku Mamre, (kumene kunkatchedwa ku Kiriyati-Ariba kapenanso Hebroni) kumene Abrahamu ndi Isake anakhalako kale.
28 Et completi sunt dies Isaac centum octoginta annorum.
Isake anakhala ndi moyo zaka 180.
29 Consumptusque ætate mortuus est: et appositus est populo suo senex et plenus dierum: et sepelierunt eum Esau et Jacob filii sui.
Anamwalira ali wokalamba kwambiri ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. Ndipo ana ake Esau ndi Yakobo anamuyika mʼmanda.