< 시편 77 >
1 아삽의 시, 영장으로 여두둔의 법칙에 의지하여 한 노래 내가 내 음성으로 하나님께 부르짖으리니 하나님께 내 음성으로 부르짖으면 내게 귀를 기울이시리로다
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Asafu. Ndinafuwulira Mulungu kupempha thandizo; ndinafuwula mokweza kwa Mulungu kuti anditcherere khutu.
2 나의 환난날에 내가 주를 찾았으며 밤에는 내 손을 들고 거두지 아니하였으며 내 영혼이 위로 받기를 거절하였도다
Pamene ndinali pa masautso ndinafunafuna Ambuye; usiku ndinatambasula manja mosalekeza ndipo moyo wanga unakana kutonthozedwa.
3 내가 하나님을 생각하고 불안하여 근심하니 내 심령이 상하도다(셀라)
Ndinakumbukira Inu Mulungu, ndipo ndinabuwula; ndinasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unalefuka. (Sela)
4 주께서 나로 눈을 붙이지 못하게 하시니 내가 괴로워 말할 수 없나이다
Munagwira zikope zanga kuti ndisagone ndipo ndinavutika kwambiri kuti ndiyankhule.
Ndinaganizira za masiku akale, zaka zamakedzana;
6 밤에 한 나의 노래를 기억하여 마음에 묵상하며 심령이 궁구하기를
Ndinakumbukira nyimbo zanga usiku. Mtima wanga unasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unafunsa kuti,
7 주께서 영원히 버리실까, 다시는 은혜를 베풀지 아니하실까,
“Kodi Ambuye adzatikana mpaka muyaya? Kodi Iwo sadzaonetsanso kukoma mtima kwawo?
8 그 인자하심이 길이 다하였는가, 그 허락을 영구히 폐하셨는가,
Kodi Chikondi chake chosatha chija chatheratu? Kodi malonjezo ake alephera nthawi yonse?
9 하나님이 은혜 베푸심을 잊으셨는가, 노하심으로 그 긍휼을 막으셨는가 하였나이다(셀라)
Kodi Mulungu wayiwala kukhala wokoma mtima? Kodi mu mkwiyo wake waleka chifundo chake?”
10 또 내가 말하기를 이는 나의 연약함이라 지존자의 오른손의 해
Ndipo ndinaganiza, “Pa izi ine ndidzapemphanso: zaka za dzanja lamanja la Wammwambamwamba.
11 곧 여호와의 옛적 기사를 기억하여 그 행하신 일을 진술하리이다
Ine ndidzakumbukira ntchito za Yehova; Ine ndidzakumbukira zodabwitsa zanu za kalekale.
12 또 주의 모든 일을 묵상하며 주의 행사를 깊이 생각하리이다
Ndidzakumbukira ntchito zanu ndi kulingalira zodabwitsa zanu.”
13 하나님이여 주의 도는 극히 거룩하시오니 하나님과 같이 큰 신이 누구오니이까
Njira zanu Mulungu ndi zoyera. Kodi ndi mulungu uti ali wamkulu kuposa Mulungu wathu?
14 주는 기사를 행하신 하나님이시라 민족들 중에 주의 능력을 알으시고
Inu ndinu Mulungu wochita zodabwitsa; Mumaonetsera mphamvu yanu pakati pa mitundu ya anthu.
15 주의 팔로 주의 백성 곧 야곱과 요셉의 자손을 구속하셨나이다(셀라)
Ndi dzanja lanu lamphamvu munawombola anthu anu, zidzukulu za Yakobo ndi Yosefe. (Sela)
16 하나님이여 물들이 주를 보았나이다 물들이 주를 보고 두려워하며 깊음도 진동하였고
Madzi anakuonani Mulungu, madzi anakuonani ndipo anachita mantha; nyanja yozama inakomoka.
17 구름이 물을 쏟고 궁창이 소리를 발하며 주의 살도 날아 나갔나이다
Mitambo inakhuthula madzi ake pansi, mu mlengalenga munamveka mabingu; mivi yanu inawuluka uku ndi uku.
18 회리바람 중에 주의 우뢰의 소리가 있으며 번개가 세계를 비취며 땅이 흔들리고 움직였나이다
Bingu lanu linamveka mʼmphepo ya kamvuluvulu, mphenzi yanu inawalitsa dziko lonse; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
19 주의 길이 바다에 있었고 주의 첩경이 큰 물에 있었으나 주의 종적을 알 수 없었나이다
Njira yanu inadutsa pa nyanja, njira yanu inadutsa pa madzi amphamvu, ngakhale zidindo za mapazi anu sizinaoneke.
20 주의 백성을 무리양 같이 모세와 아론의 손으로 인도하셨나이다
Inu munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa mwa dzanja la Mose ndi Aaroni.