< 시편 16 >
1 다윗의 믹담 하나님이여 나를 보호하소서 내가 주께 피하나이다
Mikitamu ya Davide. Ndisungeni Inu Mulungu, pakuti ine ndimathawira kwa Inu.
2 내가 여호와께 아뢰되 주는 나의 주시오니 주 밖에는 나의 복이 없다 하였나이다
Ndinati kwa Yehova, “Inu ndinu Ambuye anga; popanda Inu, ine ndilibe chinthu chinanso chabwino.”
3 땅에 있는 성도는 존귀한 자니 나의 모든 즐거움이 저희에게 있도다
Kunena za oyera mtima amene ali pa dziko, amenewa ndi olemekezeka, amene ndimakondwera nawo.
4 다른 신에게 예물을 드리는 자는 괴로움이 더할 것이라 나는 저희가 드리는 피의 전제를 드리지 아니하며 내 입술로 그 이름도 부르지 아니하리로다
Anthu amene amathamangira kwa milungu ina mavuto awo adzachulukadi. Ine sindidzathira nawo nsembe zawo zamagazi kapena kutchula mayina awo ndi pakamwa panga.
5 여호와는 나의 산업과 나의 잔의 소득이시니 나의 분깃을 지키시나이다
Yehova, Inu mwandipatsa cholowa changa ndi chikho changa; mwateteza kolimba gawo langa.
6 내게 줄로 재어 준 구역은 아름다운 곳에 있음이여 나의 기업이 실로 아름답도다
Malire a malo anga akhala pabwino; ndithudi, ine ndili cholowa chokondweretsa kwambiri.
7 나를 훈계하신 여호와를 송축할지라 밤마다 내 심장이 나를 교훈하도다
Ine ndidzatamanda Yehova amene amandipatsa uphungu; ngakhale usiku mtima wanga umandilangiza.
8 내가 여호와를 항상 내 앞에 모심이여 그가 내 우편에 계시므로 내가 요동치 아니하리로다
Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
9 이러므로 내 마음이 기쁘고 내 영광도 즐거워하며 내 육체도 안전히 거하리니
Choncho mtima wanga ndi wosangalala ndipo pakamwa panga pakukondwera; thupi langanso lidzakhala pabwino,
10 이는 내 영혼을 음부에 버리지 아니하시며 주의 거룩한 자로 썩지 않게 하실 것임이니이다 (Sheol )
chifukwa Inu simudzandisiya ku manda, simudzalola kuti woyera wanu avunde. (Sheol )
11 주께서 생명의 길로 내게 보이시리니 주의 우편에는 영원한 즐거움이 있나이다
Inu mwandidziwitsa njira ya moyo; mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu, ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja.