< 여호수아 16 >
1 요셉 자손이 제비 뽑은 것은 여리고 곁 요단 곧 여리고 물 동편 광야에서부터 나아가 여리고로 말미암아 올라가서 산지를 지나 벧엘에 이르고
Dziko limene linapatsidwa kwa fuko la Yosefe linayambira ku mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, kummawa kwa akasupe a Yeriko, ndiponso kuyambira mtsinje wa Yorodaniwo nʼkumakwera, kudutsa mʼchipululu mpaka ku mapiri a ku Beteli.
2 벧엘에서부터 루스로 나아가 아렉 사람의 경계로 지나 아다롯에 이르고
Kuchokera ku Beteli malire ake anakafika ku Luzi, kudutsa dziko la Ataroti kumene kumakhala Aariki.
3 서편으로 내려가서 야블렛 사람의 경계에 이르러 아래 벧 호론 곧 게셀에 미치고 그 끝은 바다라
Malirewo anatsikira cha kumadzulo kwa dziko la Yafuleti mpaka ku chigawo cha kumunsi kwa Beti-Horoni. Kuchokera kumeneko anapitirira mpaka ku Gezeri nʼkuthera ku Nyanja.
4 요셉의 자손 므낫세와 에브라임이 그 기업을 얻었더라
Choncho Manase ndi Efereimu, ana a Yosefe analandira cholowa chawo.
5 에브라임 자손의 그 가족대로 얻은 것의 경계는 이러하니라 그 기업의 경계는 동으로 아다롯 앗달에서 윗 벧 호론에 이르고
Dziko la mabanja a fuko la Efereimu ndi ili: Malire a dzikolo anachokera kummawa kwa Ataroti Adari mpaka ku mtunda kwa Beti-Horoni.
6 또 서편으로 나아가 북편 믹므다에 이르고 동편으로 돌아 다아낫 실로에 이르러 야노아 동편을 지나고
Malirewo anapitirira mpaka ku nyanja. Mikimetati anali kumpoto kwake. Kuchokera kumeneko anakhotera cha kummawa kuloza ku Taanati Silo ndi kudutsa kumeneko cha kummawa mpaka ku Yanowa.
7 야노아에서부터 아다롯과 나아라도 내려가서 여리고에 미치며 요단으로 나아가고
Ndipo kuchokera ku Yanowa anatsikira ku Ataroti ndi Naara, nakafika ku Yeriko ndi kukathera ku mtsinje wa Yorodani.
8 또 답부아에서부터 서편으로 지나서 가나 시내에 미치나니 그 끝은 바다라 에브라임 자손의 지파가 그 가족대로 얻은 기업이 이러하였고
Kuchokera ku Tapuwa anapita kumadzulo mpaka ku mtsinje wa Kana ndi kukathera ku nyanja. Dziko ili linali cholowa cha mabanja afuko la Efereimu,
9 그 외에 므낫세 자손의 기업 중에서 에브라임 자손을 위하여 구별한 모든 성읍과 촌락도 있었더라
kuphatikizapo mizinda yonse ndi midzi yake yopatsidwa kwa Efereimu, koma yokhala mʼkati mwa dziko la Manase.
10 그들이 게셀에 거하는 가나안 사람을 쫓아내지 아니하였으므로 가나안 사람이 오늘날까지 에브라임 가운데 거하며 사역하는 종이 되니라
Iwo sanapirikitse Akanaani amene amakhala ku Gezeri ndipo mpaka lero Akanaani akukhala pakati pa Aefereimu koma amagwira ntchito ngati akapolo.