< 이사야 59 >
1 여호와의 손이 짧아 구원치 못하심도 아니요 귀가 둔하여 듣지 못하심도 아니라
Taonani, mkono wa Yehova si waufupi kuti sungathe kupulumutsa, kapena khutu lake kuti ndilogontha kuti sangamve.
2 오직 너희 죄악이 너희와 너희 하나님 사이를 내었고 너희 죄가 그 얼굴을 가리워서 너희를 듣지 않으시게 함이니
Koma zoyipa zanu zakulekanitsani ndi Mulungu wanu; ndipo wakufulatirani chifukwa cha machimo anu, kotero Iye sadzamva.
3 이는 너희 손이 피에, 너희 손가락이 죄악에 더러웠으며 너희 입술은 거짓을 말하며 너희 혀는 악독을 발함이라
Pakuti manja anu ali psuu ndi magazi. Munayipitsa zala zanu ndi zamphulupulu. Pakamwa panu payankhula zabodza, ndipo lilime lanu lanena zinthu zoyipa.
4 공의대로 소송하는 자도 없고 진리대로 판결하는 자도 없으며 허망한 것을 의뢰하며 거짓을 말하며 잔해를 잉태하여 죄악을 생산하며
Palibe amene akuyimba mnzake mlandu molungama, palibe amene akupita ku mlandu moona mtima. Iwo amadalira mawu opanda pake ndipo amayankhula mabodza; amalingalira za mphulupulu ndipo amachita zoyipa.
5 독사의 알을 품으며 거미줄을 짜나니 그 알을 먹는 자는 죽을 것이요 그 알이 밟힌즉 터져서 독사가 나올 것이니라
Iwo amayikira mazira a mamba ndipo amaluka ukonde wakangawude. Aliyense amene adzadya mazira awo adzafa, ndipo ngati dzira limodzi lasweka limatulutsa mphiri.
6 그 짠 것으로는 옷을 이룰 수 없을 것이요 그 행위로는 자기를 가리울 수 없을 것이며 그 행위는 죄악의 행위라 그 손에는 강포한 행습이 있으며
Ukonde wawo wa kangawude sangawuvale ngati chovala; ndipo chimene apangacho sangachifunde. Ntchito zawo ndi zoyipa, ndipo amakonda kuchita zandewu ndi manja awo.
7 그 발은 행악하기에 빠르고 무죄한 피를 흘리기에 신속하며 그 사상은 죄악의 사상이라 황폐와 파멸이 그 길에 끼쳐졌으며
Amathamangira kukachita zoyipa; sachedwa kupha anthu osalakwa. Maganizo awo ndi maganizo oyipa; kulikonse kumene amapita amasiyako bwinja ndi chiwonongeko.
8 그들은 평강의 길을 알지 못하며 그들의 행하는 곳에는 공의가 없으며 굽은 길을 스스로 만드나니 무릇 이 길을 밟는 자는 평강을 알지 못하느니라
Iwo sadziwa kuchita za mtendere; zonse zimene amachita nʼzopanda chilungamo. Njira zawo zonse nʼzokhotakhota; aliyense oyenda mʼnjira zimenezo sadzapeza mtendere.
9 그러므로 공평이 우리에게서 멀고 의가 우리에게 미치지 못한즉 우리가 빛을 바라나 어두움뿐이요 밝은 것을 바라나 캄캄한 가운데 행하므로
Anthu akuti, “Chifukwa cha zimenezi chilungamo chatitalikira; ndipo chipulumutso sichitifikira. Timafunafuna kuwala koma timangopeza mdima okhaokha; tinayembekezera kuyera koma timayenda mu mdima wandiweyani.
10 우리가 소경 같이 담을 더듬으며 눈 없는 자 같이 두루 더듬으며 낮에도 황혼 때 같이 넘어지니 우리는 강장한 자 중에서도 죽은 자 같은지라
Timapapasapapasa khoma ngati munthu wosaona, kuyangʼanayangʼana njira ngati anthu opanda maso. Timapunthwa dzuwa lili paliwombo ngati kuti ndi usiku; timakhala pansi mu mdima ngati anthu akufa.
11 우리가 곰 같이 부르짖으며 비둘기 같이 슬피 울며 공평을 바라나 없고 구원을 바라나 우리에게서 멀도다
Tonse timabangula ngati zimbalangondo: Timalira modandaula ngati nkhunda. Tinayembekezera kuweruza kolungama; koma sitikupeza. Timayembekezera chipulumutso koma chimakhala nafe kutali.”
12 대저 우리의 허물이 주의 앞에 심히 많으며 우리의 죄가 우리를 쳐서 증거하오니 이는 우리의 허물이 우리와 함께 있음이라 우리의 죄악을 우리가 아나이다
Pakuti zolakwa zathu nʼzochuluka pamaso panu, ndipo machimo athu akutsutsana nafe. Zolakwa zathu zili ndi ife nthawi zonse ndipo tikuvomereza machimo athu:
13 우리가 여호와를 배반하고 인정치 아니하며 우리 하나님을 좇는데서 돌이켜 포학과 패역을 말하며 거짓말을 마음에 잉태하여 발하니
Tawukira ndi kumukana Yehova. Tafulatira Mulungu wathu, pa kupondereza anzathu ndi kupandukira Yehova, ndi pa kuyankhula mabodza amene tawaganiza mʼmitima mwathu.
14 공평이 뒤로 물리침이 되고 의가 멀리 섰으며 성실이 거리에 엎드러지고 정직이 들어가지 못하는도다
Motero kuweruza kolungama kwalekeka ndipo choonadi chili kutali ndi ife; kukhulupirika sikukupezekanso mʼmabwalo a milandu, ndipo kuona mtima sikukupezekanso mʼmenemo.
15 성실이 없어지므로 악을 떠나는 자가 탈취를 당하는도다 여호와께서 이를 감찰하시고 그 공평이 없은 것을 기뻐 아니하시고
Choonadi sichikupezeka kumeneko, ndipo wina akakana kuchita nawo zoyipa amapeza mavuto. Yehova anaziona zimenezi ndipo zinamunyansa kuti panalibe chiweruzo cholungama.
16 사람이 없음을 보시며 중재자 없음을 이상히 여기셨으므로 자기 팔로 스스로 구원을 베푸시며 자기의 의를 스스로 의지하사
Yehova anaona kuti panalibe ndi mmodzi yemwe, Iye anadabwa kuti panalibe ndi mmodzi yemwe woti nʼkupembedzera; Choncho mphamvu zake zomwe zinamuthandiza, ndipo anadzilimbitsa ndi kulungama kwake;
17 의로 호심경을 삼으시며 구원을 그 머리에 써서 투구를 삼으시고 보수로 옷을 삼으시며 열심을 입어 겉옷을 삼으시고
Iye anavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa, ndipo kumutu kwake amavala chipewa chachipulumutso; anavala kulipsira ngati chovala ndipo anadzikuta ndi mkwiyo ngati chofunda.
18 그들의 행위대로 갚으시되 그 대적에게 분노하시며 그 원수에게 보응하시며 섬들에게 보복하실 것이라
Iye adzawabwezera chilango adani a anthu ake molingana ndi zimene anachita, adzaonetsa ukali kwa adani ake ndi kubwezera chilango odana naye. Adzalanga ngakhale okhala mayiko akutali.
19 서방에서 여호와의 이름을 두려워하겠고 해돋는 편에서 그 기운에 몰려 급히 흐르는 하수 같이 오실 것임이로다
Choncho akadzabwera ngati madzi oyendetsedwa ndi mphepo yamphamvu yamkuntho. Anthu onse kuyambira kumadzulo mpaka kummawa adzaopa dzina la Yehova ndi ulemerero wake.
20 여호와께서 가라사대 구속자가 시온에 임하며 야곱 중에 죄과를 떠나는 자에게 임하리라
“Mpulumutsi adzabwera ku Ziyoni kudzapulumutsa anthu a fuko la Yakobo amene analapa machimo awo,” akutero Yehova.
21 여호와께서 또 가라사대 내가 그들과 세운 나의 언약이 이러하니 곧 네 위에 있는 나의 신과 네 입에 둔 나의 말이 이제부터 영영토록 네 입에서와 네 후손의 입에서와 네 후손의 후손의 입에서 떠나지 아니하리라 하시니라 여호와의 말씀이니라
Yehova akuti, “Kunena za pangano lake ndi iwo, Mzimu wanga umene uli pa inu, ndiponso mawu anga amene ndayika mʼkamwa mwanu sadzachoka mʼkamwa mwanu, kapena kuchoka mʼkamwa mwa ana anu, kapena mʼkamwa mwa zidzukulu zawo kuyambira tsopano mpaka kalekale,” akutero Yehova.